Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?

Werengani Mateyo 25:1-12. Ndiyeno yang’anani pa chithunzipa. Kodi chalakwika pati? Lembani mayankho anu pa mizere ili m’munsiyi.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

4. ․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi n’chifukwa chiyani anamwali asanu aja sanagawire anzawo mafuta?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyo 25:8, 9.

Kodi kugawira ena zinthu zimene tili nazo n’kofunika panthawi iti? Kodi ndi nthawi iti imene sitifunika kugawira ena zimene tili nazo?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunso awa ndipo tchulani mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.

TSAMBA 6 Kodi dziko lapansi ndi zonse zili m’menemo n’zandani? Salmo 24:․․․

TSAMBA 9 Kodi munthu aliyense wa ludzu angalandire chiyani? Chivumbulutso 22:․․․

TSAMBA 18 Kodi munthu wofatsa mtima ndi wotani? Miyambo 17:․․․

TSAMBA 29 Kodi utsiru ungachititse munthu chiyani? Miyambo 19:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Kodi Mumadziwa Chiyani za Aneneri?

5. ․․․․․

Kodi ndi mneneri uti amene anathawa mfumu Yehoyakimu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yeremiya 26:17-23.

6. ․․․․․

Hezekiya ali mfumu, kodi ndani amene analosera kuti Yerusalemu adzakhala “miunda”?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Yeremiya 26:18.

KAMBIRANANI:

Pamene mwawerenga za aneneri awiri amenewa, n’chifukwa chiyani simuyenera kuopa kulalikira za Mulungu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Miyambo 29:25.

▪ Mayankho ali pa tsamba 21

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Nkhaniyi siitchula mkwatibwi.

2. Ndi anamwali asanu amene analowa ku phwando.

3. Anamwali asanu anali ndi nyali ndi nsupa, koma asanu enawo anali ndi nyali zokha.

4. Palibe chitseko choti mkwati atseke.

5. Uriya.—Yeremiya 26:20.

6. Mika.