Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nankapakapa Ndi Mbalame Yokongola Kwambiri

Nankapakapa Ndi Mbalame Yokongola Kwambiri

Nankapakapa Ndi Mbalame Yokongola Kwambiri

MBALAME ya nankapakapa ikamadumphira m’madzi, imathamanga kwambiri ndipo chifukwa cha liwiro lake sidziwika bwinobwino kuti ndi mbalame koma imangooneka ngati ndi chinthu chinachake cha buluu chikulowa m’madzi. Imavuukamo mwamsangamsanga ili ndi nsomba kukamwa uku ikukupiza mapiko ake, ndipo apa m’pamene anthu amadziwa kuti ndi mbalame. Mbalameyi ili ndi mutu komanso mlomo waukulu ndipo ndi yokongola kwambiri. Mitundu ina ya mbalamezi imadya zinthu zina monga abuluzi, njoka, nkhanu, ngakhalenso tizilombo tosiyanasiyana. Imakonda kugwira tizilomboti ikuuluka. Pafupifupi mtundu umodzi pa mitundu itatu iliyonse ya mbalamezi imakhala pafupi ndi madzi. Zimapezekanso m’madera osiyanasiyana monga m’nkhalango zikuluzikulu, m’zilumba komanso m’zipululu. Mtundu wina wa mbalamezi womwe umakhala kuchipululu, ndi wofiira pamsana, ndipo umapezeka kwambiri mkati mwenimweni mwa dziko la Australia, komwe ndi kouma kwambiri.

Mitundu ya nankapakapa imene imadya nsomba imadziwa kwambiri kusodza. Nthawi zambiri imakhala ili phee pamtengo n’kumayang’ana m’madzi, n’cholinga choti ione nsomba. Ikaona nsomba, imachalira kukaigwira. Mbalameyi imatha kudziwa malo enieni amene nsombayo ili. Apa pamafunika luso chifukwa malo amene nsomba imaoneka ikakhala m’madzi amasiyana ndi malo enieni amene nsombayo ili. Kenako mbalameyi imadumphira m’madzimo uku ikukupiza mapiko ake n’cholinga choti iuluke mothamanga kwambiri. Ngati nsombayo ili pafupi kwambiri, mbalameyi imatha kungoikwatula popanda kulowa m’madzimo. Koma nsombayo ikakhala kuti ili pansi kwambiri, mbalameyi imapinda mapiko n’kudumphira m’madzimo mwakachetechete. Buku lina lonena za mbalame, linati: “Mbalameyi ndi yaluso kwambiri ndipo ikafuna kugwira nsomba siizengereza ndipo siiphonya.” (The Life of Birds) Mbalame ya nankapakapa imatha kugwira nsomba zingapo nthawi imodzi. Ndipo m’madera ozizira kwambiri, anthu ena aonapo mbalame zina za mtunduwu zikugwira nsomba m’madzi oyamba kuundana. Ku Australia, anthu aonapo mtundu wina wa nankapakapa ukutsomphola tinyama ting’onoting’ono tam’madzi tomwe tinagwidwa ndi nyama inayake yamadzi.

Kufuna Banja Ndiponso Malo Okhala

Mbalamezi zikamatchetcherera, zimachita zinthu zosangalatsa kwambiri. Mitundu ina ya mbalamezi imathamangitsana m’mlengalenga, ndipo kenako yaimuna imaonetsa mbalame yaikaziyo mmene imakumbira una wake pomanga chisa. Pofunanso kukopa yaikaziyo, yaimunayo imafufuza chakudya chopatsa madyo n’kukapereka kwa mbalame yaikaziyo.

Zisa za mbalamezi zimakhala zosiyana ndi zisa za mbalame zina. Zina zimakumba una m’mphepete mwa madzi ndipo kumapeto kwa unawo n’kumene kumakhala chisa chawo. Zinanso zimamanga zisa zawo mu una wa kalulu kapena mu phanga la mtengo.

Mbalameyi ikafuna kumanga chisa, imakumba una wautali mwina mpaka mita imodzi. Poyamba kukumba unawu, sipamakhala ntchito yamasewera. Mitundu yambiri ya mbalamezi ikafuna kukumba una, zimauluka kuchokera m’mwamba n’kuzondoka ndipo kenako imakazika milomo yake pamene ikufuna kukumbapo mwamphamvu. Imeneyi ndi ntchito yoopsa chifukwa nthawi zina mbalamezi zimavulala kapena kufa kumene. M’nkhalango zikuluzikulu za ku New Guinea ndi kumpoto kwa dziko la Australia, nthawi zambiri mbalamezi zimakumba una wake pachifunkha cha chiswe. Mbalamezi zikaikira mazira n’kuulutsa ana ake, chiswecho chimakonzanso malo amene mbalamezi zinagumula pachifunkhapo popanda kudandaula.

Mbalamezi zimakhalanso ndi ntchito yaikulu yodyetsa ana. Munthu wina ku Africa anaonapo mbalame yaimuna ndi yaikazi ya nankapakapa zili kalikiliki kudyetsa ana awo asanu. Zinkawapatsa anawa nsomba 60 kapena 70 tsiku lililonse kwinakunso zikupeza chakudya chawo. Panthawi inanso munthuyu anaona mbalame yaimuna ikufungatira yokha mazira. Yaikazi inafa patatsala masiku anayi kuti iswe. M’mitundu ina, mbalame zimene siziswa zimathandiza mbalame zina kufungatira mazira ndiponso kudyetsa ana.

Zimapezeka M’madera Ambiri

Mitundu yofala ya nankapakapa imapezeka m’mayiko ambiri, kuyambira ku Ireland mpaka ku Ulaya ndiponso kuyambira ku Russia mpaka ku Solomon Islands. Popeza kuti zimapezekanso m’madera amene madzi amaundana m’nyengo yozizira, mbalamezi zili m’gulu la mbalame zochepa zimene zimasamuka kupita ku dera lina. Mbalamezi zimatha kuuluka mtunda wa makilomita 3,000. Mitundu inanso yambiri ya mbalameyi imapezeka ku Israeli pafupi ndi nyanja ya Galileya ndiponso m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano. N’kutheka kuti Yesu Khristu anaona mbalame zokongola zimenezi pamene amanena fanizo lokhudza mbalame.—Onani bokosi lakuti  “Onetsetsani Mbalame za Mlengalenga.”

Mtundu wina wodziwika kwambiri wa nankapakapa umapezeka ku Australia ndipo umadziwika ndi dzina lakuti kookaburra. Mbalameyi imakhala yaitali masentimita 43 ndipo imakhala ndi mlomo wamphamvu komanso wautali masentimita 8. Imakonda kupezeka m’minda yambiri ku Australia ndipo imaoneka yakhakhi. Mbalameyi ikamalira imakhala ngati ikuseka. Komanso ndi yopanda mantha chifukwa imatha kugwira njoka yaitali mpaka mita imodzi. *

Ngakhale kuti mbalame za nankapakapa zilibe adani ambiri, chiwerengero chake chikuchepa chifukwa chakuti mitsinje komanso nkhalango zambiri zikuwonongedwa. Pafupifupi mitundu 25 ya mbalamezi zaikidwa m’gulu la mbalame zomwe zatsala pang’ono kutha. Koma ngati anthu atayesetsa kusamalira mitsinje ndiponso m’nkhalango, tikukhulupirira kuti mbalame zokongola komanso zosangalala zimenezi sizingatheretu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mtundu wina wa kookaburra, womwe umapezeka ku Australia umalira mosiyana ndi mtundu umenewu.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 17]

 “ONETSETSANI MBALAME ZA MLENGALENGA”

Yesu Khristu ankachita chidwi kwambiri ndi zinthu zam’chilengedwe, ndipo nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mafanizo a zinthu zimene waona m’chilengedwe kuti aphunzitse anthu mfundo zofunika kwambiri zokhudza makhalidwe abwino komanso choonadi chonena za Mulungu. Mwachitsanzo, Yesu anati: “Onetsetsani mbalame za mlengalenga, pajatu sizifesa kapena kukolola kapena kututira m’nkhokwe ayi; komabe Atate wanu wa kumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu a mtengo wapatali kuposa mbalame kodi?” (Mateyo 6:26) Fanizo limeneli likutiphunzitsa kuti Mulungu amatikonda kwambiri.

[Chithunzi patsamba 16]