Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liyambenso Kuyenda Bwino?

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liyambenso Kuyenda Bwino?

Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liyambenso Kuyenda Bwino?

Eni ake a nyumba aona kuti nyumba yawo yawonongeka kwambiri koma aganiza zoikonzanso.

KODI nanunso mukufuna kukonza banja lanu kuti liyambe kuyendanso bwino? Ngati ndi choncho, kodi mungayambire pati? Yesani kutsatira mfundo izi:

1 Khalani otsimikiza.

Kambiranani ndi mkazi kapena mwamuna wanu kuti nonse mufunika kuyesetsa kukonza zinthu kuti banja lanu liyambenso kuyenda bwino. Lembani zimene mwagwirizanazo papepala. Sizingakhale zovuta kuthetsa mavuto anu ngati nonse mwatsimikiza kutsatira zimene mwagwirizanazo.—Mlaliki 4:9, 10.

2 Pezani chimene chachititsa.

Kodi n’chiyani chachititsa kuti banja lanu lisamayende bwino? Lembani chinthu chimodzi chimene mukufunikira kuchita kapena kusintha kuti banja lanu liyambenso kuyenda bwino. (Aefeso 4:22-24) Zingatheke kuti vuto limene mkazi kapena mwamuna wanu angatchule lingakhale losiyana ndi lanu.

3 Khalani ndi cholinga.

Kodi mukufuna kuti ukwati wanu udzakhale wotani miyezi 6 kutsogoloku? Kodi ndi zinthu ziti kwenikweni zimene mukufuna kuzisintha? Lembani zolinga zanu papepala. Mukadziwa bwinobwino zimene mukufunikira kukonza pabanja panu, simungavutike kukwaniritsa zolinga zanuzo.—1 Akorinto 9:26.

4 Muzigwiritsa Ntchito Malangizo a M’Baibulo.

Mukadziwa chimene chikuchititsa kuti banja lanu lisamayende bwino, muyenera kupeza njira zothetsera vutolo pogwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo. Malangizo ake ndi othandiza komanso odalirika kwambiri. (Yesaya 48:17; 2 Timoteyo 3:17) Baibulo lingakuthandizeni inuyo ndi mkazi kapena mwamuna wanu kuti muzikhululukirana. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti ‘kukhululukira cholakwa ndi ulemerero.’—Miyambo 19:11; Aefeso 4:32.

Musafooke ngakhale mutaona kuti khama lanu lofuna kukonzanso banja lanu silikuthandiza. Lipoti la kafukufuku amene akatswiri ena anapanga linati: “Zotsatira za kafukufukuyu n’zosangalatsa kwambiri: Anthu 86 pa 100 aliwonse amene mabanja awo sankayenda bwino koma anapirirabe, anaona kuti patatha zaka zisanu, mabanjawo anayambanso kuyenda bwino.” (The Case for Marriage) Ngakhale anthu amene amaona kuti sizingatheke kuti banja lawo liyende bwino, anayambanso kusangalala.

Mwina inunso ngati mutapirira, banja lanu lingayambenso kuyenda bwino. Ofalitsa magazini ino, omwe ndi a Mboni za Yehova, amaona kuti malangizo a m’Baibulo amathandiza kwambiri mabanja. Mwachitsanzo, mabanja ambiri amayamba kuyenda bwino chifukwa chakuti mwamuna ndi mkazi amachita zinthu mokoma mtima, mwachifundo ndiponso mokhululukirana. Akazi aphunzira kufunika kokhala ndi “mzimu wabata ndi wofatsa” ndipo amuna aona kuti zinthu zimayenda bwino iwo akamapewa kupsera mtima akazi awo.—1 Petulo 3:4; Akolose 3:19.

Malangizo a m’Malemba amenewa amathandiza kwambiri chifukwa Yehova Mulungu amene analemba Baibulo ndi amenenso anayambitsa ukwati. Mungachite bwino kupempha a Mboni za Yehova kuti akuuzeni malangizo ena a m’Baibulo amene angathandize banja lanu. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Pofuna kuthandiza mabanja, Mboni za Yehova zinatulutsa buku la masamba 192 lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Mukafuna kudziwa zambiri, lemberani Mboni za Yehova pa adiresi yoyenerera pa maadiresi amene ali patsamba 5 la magazini ino.