Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Chikondi Chimene Anatisonyeza Chinatikhudza Kwambiri”

“Chikondi Chimene Anatisonyeza Chinatikhudza Kwambiri”

LOWERUKA pa 25 April 2015, ku Nepal kunachitika chivomerezi chachikulu. Dziko la Nepal lili kumpoto kwa dziko la India ndipo lili ndi mapiri ambiri. Dera limene kunachitika chivomerezichi lili pa mtunda wa makilomita 80 kumpoto chakumadzulo kwa mzinda wa Kathmandu, womwe ndi likulu la dzikoli. Nyumba zoposa 500,000 zinawonongedwa ndipo n’zomvetsa chisoni kuti anthu oposa 8,500 anafa pa ngoziyi. Chiwerengerochi n’chachikulu kuposa chiwerengero cha anthu amene anafapo pa ngozi zina m’dzikoli. Ku Nepal kuli a Mboni za Yehova okwana 2,200 ndipo ambiri amakhala m’dera limene kunachitika chivomerezichi. Ndipo ndi zomvetsa chisoni kuti wa Mboni mmodzi limodzi ndi ana ake awiri anamwalira pangoziyi.

Wa Mboni wina dzina lake Michelle ananena kuti: “Chivomerezichi chinachitika a Mboni amene amakhala m’dera limene linawonongedwa kwambiri ali kumisonkhano yawo yachikhristu. Zikanakhala kuti chinachitika ali kunyumba, ambiri akanamwalira.” Kodi anthu amene anali kumisonkhanowo anapulumuka chifukwa chiyani? Chimene chinathandiza kwambiri ndi mmene anamangira Nyumba za Ufumu.

“PANOPA UBWINO WAKE WAONEKA”

Nyumba za Ufumu za ku Nepal amazimanga zolimba kwambiri n’cholinga choti zisamawonongeke kukachitika chivomerezi. Wa Mboni wina amene amamanga nawo Nyumba za Ufumu, dzina lake Man Bahadur, anati: “Anthu ankakonda kutifunsa kuti n’chifukwa chiyani timayala maziko olimba kwambiri pamene nyumbazi si zazikulu. Koma panopa ubwino wake waoneka.” Chivomerezichi chitachitika, Nyumba za Ufumu zinayamba kugwiritsidwa ntchito ngati malo osungira anthu amene anakhudzidwa ndi ngoziyi. Ngakhale kuti kunachitikanso zivomerezi zina zing’onozing’ono, a Mboni za Yehova komanso anthu ena anali otetezeka m’nyumbazi.

A Mboni za Yehova komanso anthu ena ankakhala mu Nyumba za Ufumu

Chivomerezichi chitangochitika, akulu a m’mipingo ya Mboni za Yehova anayamba kufufuza a Mboni anzawo omwe anali asanapezeke. Wa Mboni wina dzina lake Babita anati: “Akulu anadzipereka kwambiri kuti athandize anthu a mumpingo. Chikondi chimene anatisonyeza chinatikhudza kwambiri.” Tsiku lotsatira, anthu atatu a m’komiti imene imayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikoli komanso anthu ena amene amagwira ntchito yoyendera mipingo, anayamba kupita kumipingo kuti adziwe zimene anthu ankafunikira komanso kuti athandize akulu a m’mipingoyo.

Gary Breaux wa ku likulu la Mboni za Yehova akulimbikitsa anthu okhudzidwa ndi chivomerezi

Patapita masiku 6 kuchokera pamene chivomerezichi chinachitika, munthu wina dzina lake Gary Breaux, yemwe amagwira ntchito kulikulu la Mboni za Yehova lomwe lili ku United States, anapita ku Nepal limodzi ndi mkazi wake dzina lake Ruby. Munthu wina dzina lake Reuben yemwe ali m’komiti ija anati: “Tinkakayikira kuti M’bale Breaux akhoza kufika ku Kathmandu chifukwa kunali chipwirikiti komanso kunkachitika tizivomerezi tina ting’onoting’ono. Komabe ankafunitsitsa atabwera ndipo anafikadi. Atafika, a Mboni analimbikitsidwa kwambiri.”

“CHINATHANDIZA KUTI TIGWIRIZANE KWAMBIRI”

Wa Mboni wina dzina lake Silas, yemwe amagwira ntchito ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Nepal, anati: “Telefoni zitangoyamba kugwiranso ntchito, anthu ankatiimbira ndi usiku womwe. A Mboni anzathu padziko lonse ankatidera nkhawa. Ngakhale kuti ena ankalankhula zilankhulo zomwe sitinkazimva tinkaona kuti amatikonda komanso akufunitsitsa kutithandiza.”

A Mboni ochokera ku Europe akuthandiza anthu ovulala

Kwa masiku ambiri chivomerezichi chitachitika, a Mboni a m’madera ena ankabweretsa chakudya ku Nyumba za Ufumu kuti adzagawire anthu okhudzidwa ndi ngoziyi. A Mboni anakhazikitsanso komiti yopereka chithandizo ndipo pasanapite nthawi yaitali anthu anayamba kulandira zinthu zochokera ku Bangladesh, India, Japan ndiponso mayiko ena. Patapita masiku ochepa, kunafika a Mboni ogwira ntchito zachipatala ochokera ku Europe ndipo anakhazikitsa malo othandizira anthu pa Nyumba ya Ufumu inayake. Kenako anayamba kuthandiza anthu ovulala komanso omwe ankavutika maganizo.

Mayi wina dzina lake Uttara anafotokoza mmene anthu ambiri ankamvera. Iye anati: “Chivomerezichi chinali choopsa kwambiri. Koma chinathandiza kuti tigwirizane kwambiri ndi Akhristu anzathu.” Chivomerezichi sichinasokoneze mgwirizano wa anthu a Yehova kapenanso kuwalepheretsa kumukonda. M’malomwake, chinachititsa kuti azigwirizana kwambiri ndi Akhristu anzawo komanso kuti azikonda kwambiri Mulungu.