Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO

N’chifukwa Chiyani Achinyamata Ambiri Akudwala Matenda Ovutika Maganizo?

N’chifukwa Chiyani Achinyamata Ambiri Akudwala Matenda Ovutika Maganizo?

MTSIKANA wina dzina lake Anna * ananena kuti: “Ndikayamba kuvutika maganizo, sindifuna kuchita chilichonse. Ndimafuna kuti ndizingogona. Nthawi zambiri ndimaona ngati palibe amene amandikonda, ndine wosafunika komanso ndimaona kuti ndimatopetsa anthu ena.”

Mtsikana winanso dzina lake Julia ananena kuti: “Ndinkaona kuti ndi bwino kungodzipha. Sikuti ndinkafunadi kufa. Kungoti ndinali nditatopa ndi zimene zinkandichitikirazi. Mwachibadwa ndine munthu woti ndimaganizira ena, koma ndikayamba kuvutika maganizo sindisamala za munthu.”

Anna ndi Julia anayamba kuvutika ndi matendawa asanakwanitse zaka 15. Achinyamata ena akhoza kumavutika maganizo mwa apo ndi apo, koma Anna ndi Julia ankavutika kwa milungu ingapo kapenanso miyezi. Anna ananena kuti: “Ukamavutika maganizo zimakhala ngati uli m’dzenje lakuya komanso lamdima lomwe lilibe potulukira. Umangokhala ngati si iweyonso moti umaona ngati wayamba misala.”

Nkhani ya Anna ndi Julia si yachilendo. Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti: “Masiku ano chiwerengero cha achinyamata amene akupezeka ndi vuto la matenda a maganizo chikuchuluka kwambiri ndipo nthawi zambiri n’zomwe zimachititsa kuti anyamata a zaka za pakati pa 10 ndi 19 azidwaladwala komanso kulumala.”

Zizindikiro za matenda ovutika maganizo zikhoza kuonekera munthu akangopitirira zaka 10 ndipo zingaphatikizepo kusagona mokwanira kapena kugona kwambiri, kusafuna kudya ndiponso thupi la munthuyo limasintha, mwina anganenepe kapena kuwonda. Nthawi zinanso munthu akhoza kumakhala ndi nkhawa, kukhumudwa komanso kumangodziona ngati wachabechabe. Angamakonde kukhala payekha, angamavutike kuika maganizo pa zimene akuchita kapenanso angamavutike kukumbukira zinthu. Akhozanso kumalankhula kapena kuchita zinthu zosonyeza kuti akufuna kudzipha. Nthawi zinanso angakhale ndi zizindikiro zina zomwe ngakhale achipatala sangathe kuzifotokoza bwinobwino. Nthawi zambiri akatswiri a zachipatala amayang’ana zizindikiro zosiyanasiyana zimene wakhala akusonyeza kwa milungu ingapo komanso zinthu zimene zikumamusokoneza zochita zake za tsiku ndi tsiku.

ZIMENE ZINGAYAMBITSE MATENDAWA

Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse linanena kuti “achinyamata angayambe kuvutika maganizo chifukwa cha zinthu zimene akukumana nazo komanso zomwe zikuchitika m’thupi mwawo.” Zinthu zina zomwe zingayambitse matendawa ndi monga:

Zimene zikuchitika m’thupi. Mofanana ndi Julia, nthawi zambiri matenda ovutika maganizo amakhala akumtundu ndipo zikuoneka kuti majini amene munthu anatengera kwa makolo ake akhoza kuchititsa kuti ubongo wake uzichita zinthu mwanjira inayake. Zifukwa zinanso ndi monga kudwala matenda amtima ndiponso kuchuluka kapena kuchepa kwa mahomoni. Vutoli lingakulenso kwambiri ngati munthu amagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo. *

Nkhawa. N’zoona kuti kudera nkhawa zinthu zina n’kothandiza. Komabe kuda nkhawa kwambiri kungatidwalitse ndipo kukhoza kuchititsa kuti achinyamata ena ayambe kudwala mosavuta matenda ovutika maganizo. Ngakhale zili choncho, tisaiwale kuti chimene chimayambitsa matendawa sichikudziwika bwinobwino ndipo nthawi zina angayambe chifukwa cha zinthu zingapo.

Achinyamata akhoza kukhala ndi nkhawa chifukwa cha kutha kwa banja la makolo awo, imfa ya wachibale kapena mnzawo, kuzunzidwa kapena kuchitidwa nkhanza zokhudza kugonana, kuchita ngozi yoopsa, matenda kapenanso chifukwa chodziona kuti amasekedwa kapena kusalidwa chifukwa cholephera kuphunzira zinthu. Nthawi zinanso mwana akhoza kudwala matenda a maganizo ngati makolo ake akumuyembekezera kuti azichita zinthu zimene sangakwanitse, mwina zokhudza maphunziro. Ana enanso angavutike maganizo chifukwa chovutitsidwa ndi anzawo kusukulu, kudera nkhawa kwambiri za tsogolo lawo kapena kuleredwa ndi kholo lomwenso lili ndi matenda a maganizo ndipo likulephera kuwasonyeza chikondi. Komano ngati wachinyamata ali ndi matendawa, kodi n’chiyani chingamuthandize kupirira?

MUZITETEZA THANZI LANU

Anthu amene akudwala matenda a maganizo nthawi zambiri amapatsidwa mankhwala komanso malangizo ndi akatswiri a matendawa. * Yesu Khristu ananena kuti: “Anthu amphamvu safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.” (Maliko 2:17) Matenda akhoza kukhudza mbali iliyonse ya thupi lathu, kuphatikizapo ubongo. Choncho nthawi zina munthu angalimbikitsidwe kusintha zimene amachita pa moyo wake chifukwa pali kugwirizana pakati pa maganizo a munthu ndi zochita zake.

Ngati muli ndi matenda a maganizo muyenera kumasamalira bwino thanzi lanu. Mwachitsanzo, muyenera kumadya zakudya zopatsa thanzi, kumagona mokwanira ndiponso kumachita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse. Masewera olimbitsa thupi amathandiza kuti thupi lanu litulutse timadzi tinatake tokuthandizani kuti mukhale osangalala, amphamvu komanso kuti muzigona bwino. Ngati n’zotheka, muziyesetsa kudziwa zimene zimayambitsa vutolo komanso zizindikiro zake n’kukonzekeratu zomwe mungachite ngati zitachitika. Muyeneranso kufotokozera mnzanu wodalirika vuto limene muli nalo. Kukhala ndi achibale komanso anzanu ambiri omwe amakuganizirani kungakuthandizeni kupirira vuto lanulo. Mukhale ndi buku n’kumalembamo zimene zikuyenda m’mutu mwanu komanso mmene mukumvera. Zimenezi ndi zomwe zinathandiza Julia, yemwe tamutchula kale uja. Komabe chinthu chofunika kwambiri ndi kuyesetsa kuchita zinthu zauzimu. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti muzisangalala. Yesu Khristu ananena kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”Mateyu 5:3.

Muzidya mokwanira, muzichita masewera olimbitsa thupi komanso muzigona mokwanira

Mukhoza kumakhala osangalala ngati mutamachita zinthu zauzimu

Anna ndi Julia amaona kuti zimene Yesu ananenazi ndi zoona. Anna anati: “Kutumikira Mulungu kumandithandiza kuti ndiziganizira anthu ena, m’malo momangoganizira za mavuto anga. Nthawi zina kuchita zimenezi si kophweka, komabe kumandithandiza kuti ndizikhala wosangalala.” Julia amalimbikitsidwanso akamapemphera kwa Mulungu komanso akamawerenga Baibulo. Iye ananena kuti: “Ndikamuuza Mulungu nkhawa zanga m’pemphero mtima wanga umakhala m’malo. Baibulo limandithandiza kuona kuti Mulungu amandiwerengera komanso kuti amandikonda kwambiri. Kuwerenga Baibulo kumandithandizanso kuganizira zinthu zosangalatsa zimene zikubwera kutsogoloku.”

Yehova ndi Mlengi wathu ndipo amadziwa mmene zinthu zimene tinakumana nazo pa moyo wathu komanso majini athu zimakhudzira maganizo komanso zochita zathu. Choncho akhoza kutithandiza ndi kutilimbikitsa ndipo nthawi zina akhoza kugwiritsa ntchito anzathu omwe amatikonda komanso kutimvetsa. Komanso cholimbikitsa kwambiri n’choti kutsogoloku Mulungu adzathetseratu matenda onse, kuphatikizapo okhudza maganizo. Lemba la Yesaya 33:24 limati: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”

Baibulo limalonjeza kuti Mulungu “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu], ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chivumbulutso 21:4) Zimenezitu ndi zolimbikitsa kwambiri. Ngati mukufuna kuphunzira zambiri zokhudza zimene Mulungu adzachite padzikoli komanso zimene adzachitire anthu, pitani pawebusaiti yathu ya jw.org/ny. Pawebusaitiyi pali Baibulo labwino kwambiri komanso nkhani zosiyanasiyana, kuphatikizapo zokhudza matenda ovutika maganizo.

^ ndime 3 Mayina asinthidwa.

^ ndime 10 Matenda ambiri komanso mankhwala amene anthu wamba amagulitsa angachititsenso munthu kukhala ndi zizindikiro za matenda a maganizo. Choncho ndi bwino kupita kuchipatala kuti akakuyezeni komanso kukulemberani mankhwala oyenerera.

^ ndime 14 Magazini ya Galamukani! sisankhira anthu zochita pa nkhani ya mankhwala.