Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo ndi Lodalirika Ndipo Limatiuza Choonadi

Baibulo ndi Lodalirika Ndipo Limatiuza Choonadi

Kuyambira kale, anthu osiyanasiyana akhala akuona kuti Baibulo ndi lodalirika ndipo limanena zoona. Masiku ano anthu mamiliyoni ambiri amatsatira zimene limaphunzitsa. Komabe pali anthu enanso ambiri amene amaona kuti nkhani za m’Baibulo ndi nthano chabe ndipo mfundo zake n’zosathandiza. Kodi inuyo mumaliona bwanji? Kodi mungapeze choonadi m’Baibulo?

CHIFUKWA CHAKE MUYENERA KUKHULUPIRIRA BAIBULO

Kodi n’chiyani chimene chingakuchititseni kuti muzikhulupirira Baibulo? Tiyerekeze kuti muli ndi mnzanu amene kwa zaka zambiri wakhala akukuuzani zoona. N’zosakayikitsa kuti mungamaone kuti mnzanuyo ndi wodalirika. Ndiye kodi Baibulo limanena zoona nthawi zonse? Tiyeni tione zitsanzo zotsatirazi.

Olemba Ake Ankanena Zoona Zokhazokha

Anthu amene analemba Baibulo anali oona mtima, ndipo ankafotokoza zimene ankalakwitsa. Mwachitsanzo mneneri Yona analemba za kusamvera kwake. (Yona 1:1-3) Ndipotu iye anamaliza kulemba buku lake ndi mfundo zosonyeza kuti Mulungu anam’dzudzula koma sanalembe zabwino zimene anachita atadzudzulidwa chifukwa mwina sanafune kuti anthu azimutamanda. (Yona 4:1, 4, 10, 11) Kuona mtima kwa anthu onse amene analemba Baibulo kumasonyeza kuti ankakonda choonadi.

Malangizo Othandiza

Kodi Baibulo lili ndi malangizo amene angatithandize pa moyo wathu? Inde. Mwachitsanzo, taonani zimene limanena zomwe zingatithandize kuti tizigwirizana ndi anzathu. Limati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12) Limanenanso kuti: “Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo, koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Choncho mfundo za m’Baibulo n’zothandizabe panopa ngati mmene zinalili pamene linkalembedwa.

Limafotokoza Mbiri Yakale Molondola

Akatswiri ambiri ofukula zinthu zakale akhala akupeza zinthu zosonyeza kuti anthu, malo komanso nkhani zotchulidwa m’Baibulo n’zolondola. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti m’nthawi ya Nehemiya, anthu a ku Turo (Afoinike a ku Turo) omwe ankakhala ku Yerusalemu ‘ankabweretsa nsomba ndi malonda osiyanasiyana.’​—Nehemiya 13:16.

Kodi pali umboni uliwonse wosonyeza kuti zimene Baibulo limanenazi ndi zoona? Inde ulipo. Ofukula zinthu zakale anapeza zinthu za ku Foinike ku Isiraeli zomwe zikusonyeza kuti anthu a mitundu iwiriyi ankagulitsana malonda. Kuwonjezera pamenepo, ku Yerusalemu kunapezeka minga za nsomba za kunyanja ya Mediterranean. Akatswiri ofukula zinthu zakale amakhulupirira kuti anthu ochita malonda ochokera kunyanja yakutali imeneyi ndi amene ankabweretsa nsombazi. Ataona bwinobwino maumboni onsewa, katswiri wina anati: “Mawu a pa Nehemiya 13:16, akuti anthu a ku Turo ankagulitsa nsomba ku Yerusalemu ayenera kuti ndi oona.”

Limanena Zoona pa Nkhani za Sayansi

Baibulo si buku la sayansi koma ndi buku lachipembedzo komanso la mbiri yakale. Komabe likamanena nkhani zasayansi, zimakhala zolondola. Taonani chitsanzo ichi.

Zaka pafupifupi 3,500 zapitazo Baibulo linanena kuti dziko lapansili lili “m’malere.” (Yobu 26:7) Zimenezi zinali zosiyana ndi zimene anthu ambiri ankakhulupirira zoti dzikoli limayandama pamadzi kapena lili pamsana pa chikamba chachikulu. Patapita zaka pafupifupi 1,100 kuchokera pamene buku la Yobu linalembedwa anthu ankaonabe kuti n’zosatheka kuti dziko lapansili likhale m’malere. Koma zaka 300 zapitazo, mu 1687, wasayansi wina dzina lake Isaac Newton ananena m’buku lake zokhudza mphamvu yokoka komanso kuti dzikoli lili m’malere ndipo mphamvu yokokayo ndi imene imathandiza kuti likhalebe m’maleremo. Sayansi imeneyi inatsimikizira kuti zimene Baibulo linanena zaka 3,000 m’mbuyomo ndi zoona.

Limanena Zoona pa Nkhani ya Maulosi

Kodi maulosi a m’Baibulo ndi olondola? Taonani chitsanzo ichi chomwe ndi ulosi wa Yesaya wonena za kuwonongedwa kwa mzinda wa Babulo.

Ulosi: M’zaka za m’ma 700 B.C. E., Yesaya yemwe analemba nawo Baibulo analosera kuti mzinda wa Babulo, womwe kenako unadzakhala likulu la ufumu wamphamvu padziko lonse, udzawonongedwa ndipo simuzidzakhalanso anthu. (Yesaya 13:17-20) Yesaya anatchulanso dzina la munthu amene adzachite zimenezi kuti ndi Koresi. Anafotokozanso njira imene Koresiyo adzagwiritse ntchito. Iye anati mitsinje ‘idzauma’ komanso mageti adzasiyidwa osatseka.​—Yesaya 44:27, 28; 45:1.

Kukwaniritsidwa Kwake: Patatha zaka pafupifupi 200 kuchokera pamene Yesaya ananena ulosiwu, mfumu ina ya ku Perisiya inaukira Babulo. Kodi dzina lake anali ndani? Anali Koresi. Popeza mzinda wa Babulo unali wotetezeka kwambiri chifukwa unazunguliridwa ndi mtsinje wa Firate, Koresi ndi asilikali ake anakumba ngalande n’cholinga choti apatutse madzi a mumtsinjewo. Zimenezi zinachititsa kuti madzi a mumtsinjewo achepe mpaka kufika m’ntchafu moti iye ndi asilikali akewo anatha kuwoloka n’kukafika pampanda wa mzindawo. N’zodabwitsa kuti pa nthawiyi Ababulo anasiya mageti oyang’ana kumtsinjewo ali osatseka. Koresi ndi asilikali ake analowa mumzinda wa Babulo n’kulanda mzindawo.

Komabe panali ulosi wina womwe unatsala kuti ukwaniritsidwe. Ulosi wake unali wakuti mumzindawu sumuzidzakhalanso anthu. Kwa zaka mahandiredi angapo anthu anapitirizabe kukhala mumzinda wa Babulo. Koma panopa mzindawu unasanduka bwinja. Malo amene panali mzindawu panopa ndi pafupi ndi Baghdad ku Iraq ndipo mabwinjawo ndi umboni wakuti ulosiwu unakwaniritsidwa. Choncho Baibulo ndi lodalirika ngakhalenso pa nkhani ya maulosi.