Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Yesu atabadwa, n’chifukwa chiyani Yosefe ndi Mariya anakhalabe ku Betelehemu m’malo mobwerera kwawo ku Nazareti?

Baibulo silifotokoza. Komabe limafotokoza mfundo zina zochititsa chidwi zomwe mwina zinachititsa kuti asabwerere ku Nazareti.

Mngelo anauza Mariya kuti adzakhala woyembekezera komanso adzakhala ndi mwana. Pamene mngeloyu ankafikitsa uthengawu n’kuti Mariya ndi Yosefe akukhala m’tauni ya Nazareti ku Galileya. (Luka 1:26-31; 2:4) Komanso m’tsogolo mwake, pamene ankachokera ku Iguputo iwo anabwerera ku Nazareti. Yesu anakulira kumeneko ndipo anakhala Mnazareti. (Mat. 2:19-23) Choncho m’pomveka kuti timaganizira za ku Nazareti tikangomva za Yesu, Yosefe ndi Mariya.

Mariya anali ndi wachibale dzina lake Elizabeti yemwe ankakhala ku Yuda. Elizabeti anali mkazi wa Zekariya yemwe anali wansembe ndipo anadzakhala mayi wa Yohane M’batizi. (Luka 1:5, 9, 13, 36) Mariya anapita kukaona Elizabeti ku Yuda komwe anakhalako miyezi itatu. Kenako iye anabwerera ku Nazareti. (Luka 1:39, 40, 56) Choncho Mariya ankadziwa zinthu zambiri zokhudza ku Yuda.

Patapita nthawi, Yosefe anamvera lamulo loti ‘akalembetse’ m’kaundula. Choncho Yosefe anachoka ku Nazareti kupita ku Betelehemu womwe unali “mzinda wa Davide,” komanso kumene ulosi unaneneratu kuti Mesiya adzabadwirako. (Luka 2:3, 4; 1 Sam. 17:15; 20:6; Mika 5:2) Yesu atabadwa, Yosefe sanalole kuti Mariya ayende mtunda wautali kubwerera ku Nazareti ali ndi mwana wakhanda. Iwo anakhala ku Betelehemu, dera lomwe linali makilomita pafupifupi 9 kuchokera ku Yerusalemu. Zimenezi zikanathandiza kuti asavutike kupita ndi mwana wawoyo kukachisi kukapereka nsembe yomwe inkafunikira.​—Lev. 12:2, 6-8; Luka 2:22-24.

Mngelo anali atauza Mariya kuti mwana wakeyo adzakhala “pampando wachifumu wa Davide” ndipo “adzalamulira monga mfumu.” Kodi n’kutheka kuti Yosefe ndi Mariya anaona kuti n’zochititsa chidwi kuti Yesu anabadwira mumzinda wa Davide? (Luka 1:32, 33; 2:11, 17) Mwinanso anaona kuti ndi bwino kuti apitirize kukhala komweko n’kudikira kuti aone zimene Mulungu akufuna kuti iwo achite.

Sitikudziwa kuti iwo anali atakhala nthawi yaitali bwanji ku Betelehemu pamene okhulupirira nyenyezi aja anabwera. Komabe pofika pa nthawiyi, banjali linali likukhala m’nyumba ndipo “mwanayo” sanali wakhanda koma wokulirapo. (Mat. 2:11) Zikuoneka kuti m’malo mobwerera ku Nazareti, iwo anakhazikika ku Betelehemu.

Herode analamula kuti “ana onse aamuna m’Betelehemu . . . kuyambira azaka ziwiri kutsika m’munsi,” aphedwe. (Mat. 2:16) Mogwirizana ndi zimene analamulazi, Yosefe ndi Mariya anatenga Yesu n’kuthawira ku Iguputo, kumene anakhalako mpaka pamene Herode anamwalira. Pambuyo pake, Yosefe anatenga banja lake n’kupita ku Nazareti. N’chifukwa chiyani atachoka ku Iguputo sanabwererenso ku Betelehemu? Chifukwa chakuti Arikelao mwana wa Herode, yemwe anali wankhanza, anali akulamulira ku Yudeya, ndiponso ankafuna kumvera chenjezo la Mulungu. Ku Nazaretiko, banjalo likanakhala lotetezeka komanso akanatha kulera bwino Yesu kuti azilambira Mulungu.​—Mat. 2:19-22; 13:55; Luka 2:39, 52.

Zikuoneka kuti Yosefe anamwalira Yesu asanatsegule mwayi woti anthu ena adzapite kumwamba. Choncho Yosefe adzaukitsidwa n’kukhala ndi moyo padziko lapansi. Anthu ambiri adzakhala ndi mwayi wokumana naye komanso kumufunsa zifukwa zomwe zinachititsa kuti iye ndi Mariya akhalebe ku Betelehemu Yesu atabadwa.