Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Zina Zopezeka mu ”Nsanja ya Olonda” Yophunzira

Nkhani Zina Zopezeka mu ”Nsanja ya Olonda” Yophunzira

Ofalitsa ambiri amagwiritsa ntchito JW Library pokonzekera misonkhano ndipo amaona kuti imawathandiza kupeza mosavuta nkhani iliyonse yophunzira. Koma magazini yophunzira nthawi zambiri imakhalanso ndi nkhani zina zomwe ndi chakudya chauzimu. Kodi mungapeze bwanji nkhanizi pa JW Library kuti zizikuthandizani?

  • Kumapeto kwa nkhani zonse zophunzira kumakhala kamutu kakuti “Zinanso Zimene Mungawerenge.” Pansi pa kamutu kameneka, dinani pamene alemba kuti “Nkhani zina m’magaziniyi.” Mukapita pa mbali ya “Zimene Zili M’magaziniyi,” muona mitu komanso manambala a nkhani zophunzira. Kenako mungasankhe nkhani zina zomwe si zophunzira kuti muwerenge.

  • Pa tsamba loyamba la JW Library, pa gawo lakuti “What’s New,” pangani dawunilodi magazini iliyonse yatsopano ya Nsanja ya Olonda. Tsegulani magaziniyo ndipo pitani pa “Zimene Zili M’magaziniyi” n’cholinga choti muphunzire nkhani zonse.