Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yosefe wa ku Arimateya Analimba Mtima

Yosefe wa ku Arimateya Analimba Mtima

YOSEFE WA KU ARIMATEYA sanamvetse kuti analimba mtima bwanji kuti alankhule ndi bwanamkubwa wa Roma. Pontiyo Pilato ankadziwika ndi khalidwe losamva zonena za ena. Komabe, kuti Yesu aikidwe m’manda mwaulemu, panafunika kuti munthu wina akapemphe kaye chilolezo kwa Pilatoyo. Yosefe anapita kukakambirana ndi Pilato pamasom’pamaso, ndipo ayenera kuti anadabwa kuti anakambirana nkhaniyo bwinobwino. Pilato anapereka chilolezocho pambuyo poti msilikali wamutsimikizira kuti Yesu wamwaliradi. Yosefe anali adakali ndi chisoni kwambiri, koma atangomuloleza ananyamuka kupita kumene Yesu anaphedwera.—Maliko 15:42-45.

  • Kodi Yosefe wa ku Arimateya anali ndani?

  • Nanga ankadziwana motani ndi Yesu?

  • Kodi nkhani yake ndi yofunika bwanji kwa inuyo?

ANKAWERUZA NAWO MU KHOTI LALIKULU LA AYUDA

Nkhani ya mu Uthenga Wabwino wa Maliko imanena kuti Yosefe anali “munthu wodziwika wa m’Bungwe Lalikulu la Ayuda.” Bungwe Lalikulu la Ayuda limeneli linkadziwikanso kuti Khoti Lalikulu la Ayuda. (Maliko 15:1, 43) Zimenezi zikusonyeza kuti Yosefe anali mmodzi wa atsogoleri a Ayuda ndipo n’chifukwa chake zinatheka kukaonana ndi bwanamkubwa wa Roma. N’chifukwa chakenso si zodabwitsa kuti anali wolemera.​—Mat. 27:57.

Kodi mumalimba mtima n’kuvomereza kuti Yesu ndi Mfumu yanu?

Khoti Lalikulu la Ayuda linkadana ndi Yesu moti oweruza ake anagwirizana kuti amuphe. Koma Baibulo limanena kuti Yosefe anali “munthu wabwino ndi wolungama.” (Luka 23:50) Mosiyana ndi anzake ambiri m’khotili, iye anali woona mtima, wamakhalidwe abwino ndipo ankayesetsa kumvera malamulo a Mulungu. ‘Ankayembekezeranso ufumu wa Mulungu,’ ndipo mwina n’chifukwa chake anakhala wophunzira wa Yesu. (Maliko 15:43; Mat. 27:57) Ayenera kuti ankachita chidwi ndi uthenga wa Yesu chifukwa chakuti ankaona kuti choonadi ndiponso chilungamo ndi zofunika kwambiri.

ANALI WOPHUNZIRA WAMSERI WA YESU

Lemba la Yohane 19:38 limanena kuti Yosefe “anali wophunzira wa Yesu koma wamseri chifukwa anali kuopa Ayuda.” Koma kodi Yosefe ankaopa Ayudawo chifukwa chiyani? Iye ankadziwa kuti Ayuda ankadana kwambiri ndi Yesu komanso anali okonzeka kuchotsa musunagoge munthu aliyense amene amamukhulupirira. (Yoh. 7:45-49; 9:22) Munthu akachotsedwa musunagoge ankanyozedwa ndiponso kusalidwa ndi Ayuda anzake. N’chifukwa chake poyamba Yosefe sankanena poyera kuti amakhulupirira Yesu. Kuchita zimenezi kukanapangitsa kuti achotsedwe pa udindo wake komanso anthu akanasiya kumulemekeza.

Si Yosefe yekha amene ankaopa zimenezi. Mwachitsanzo, lemba la Yohane 12:42 limanena kuti “ambiri, ngakhalenso olamulira anamukhulupirira [Yesu], koma chifukwa cha Afarisi sanavomereze poyera, poopa kuti angawachotse musunagoge.” Munthu winanso amene anali ndi vuto lofanana ndi limeneli anali Nikodemo, yemwenso anali wa mu Khoti Lalikulu la Ayuda.​—Yoh. 3:1-10; 7:50-52.

Koma Yosefe anali wophunzira, chabe kuti sankafuna kunena poyera zimenezi. Limenelitu linali vuto lalikulu makamaka tikaganizira mawu a Yesu akuti: “Aliyense wovomereza pamaso pa anthu kuti ali kumbali yanga, inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate wanga wakumwamba kuti ndili kumbali yake. Koma aliyense wondikana ine pamaso pa anthu, inenso ndidzamukana pamaso pa Atate wanga wakumwamba.” (Mat. 10:32, 33) N’zoona kuti Yosefe sanakane Yesu, koma vuto ndi lakuti sanalimbe mtima n’kuvomereza Yesuyo pamaso pa anthu. Kodi inuyo mumalimba mtima?

Komabe pali chinthu china chabwino chimene Yosefe anachita. Baibulo limanena kuti iye sanagwirizane ndi Khoti Lalikulu la Ayuda pa chiwembu chimene linkafuna kuchitira Yesu. (Luka 23:51) Ndipo ena amanena kuti Yosefe ayenera kuti panalibe pa nthawi imene Yesu ankazengedwa mlandu. Kaya zinthu zinali bwanji, Yosefe ayenera kuti anakhumudwa kwambiri kuona kuti mlanduwu sanauzenge mwachilungamo, koma palibe chimene akanachita.

ANALIMBA MTIMA

Zikuoneka kuti pa nthawi imene Yesu amamwalira, Yosefe anali atasiya kuchita mantha ndipo anayamba kuchita zinthu limodzi ndi otsatira a Yesu. Zimenezi zikuonekera bwino tikaganizira lemba la Maliko 15:43 lomwe limati: “Anapita kwa Pilato molimba mtima kukapempha mtembo wa Yesu.”

Zikuoneka kuti pamene Yesu amamwalira n’kuti Yosefe ali pomwepo, moti iye anadziwa zoti Yesu wafa Pilato asanadziwe. N’chifukwa chake Yosefe atapempha za mtembo wa Yesu, bwanamkubwayo “anali kukayikira ngati anali atamwalira kale.” (Maliko 15:44) N’kutheka kuti Yosefe zinamukhudza kwambiri ataona mmene Yesu anazunzikira atapachikidwa pamtengo, ndipo zinamupangitsa kuti alimbe mtima n’kunena poyera kuti ndi wophunzira wa Yesu. Kaya zinalidi choncho kapena ayi, pa nthawiyi Yosefe anali wokonzeka kugwira ntchito monga wotsatira wa Yesu popanda kudzibisa.

YOSEFE ANAIKA YESU M’MANDA

Ayuda anali ndi lamulo lakuti munthu amene wapatsidwa chilango chophedwa aziikidwa m’manda dzuwa lisanalowe. (Deut. 21:22, 23) Koma Aroma akapha munthu wopalamula mlandu, thupi lake ankalisiya kuti liwolere pamtengo pomwepo kapena ankangolitaya m’dzenje linalake. Koma Yosefe sankafuna kuti zimenezi zichitike ndi thupi la Yesu. Yosefe anali atagobetsa manda atsopano pafupi ndi pamene Yesu anaphedwera. Mandawa anali asanayambe kuwagwiritsa ntchito, ndipo mfundo imeneyi ikusonyeza kuti Yosefe anali atangosamukira kumene ku Yerusalemu kuchokera ku Arimateya. * N’kutheka kuti mandawa anali oti muziikidwa anthu a m’banja lake. (Luka 23:53; Yoh. 19:41) Choncho zimene Yosefe anachita poika Yesu m’manda ake kunali kukoma mtima ndipo zinakwaniritsa ulosi wakuti Mesiya adzaikidwa m’manda “limodzi ndi anthu olemera.”​—Yes. 53:5, 8, 9.

Kodi pali chinachake chomwe mumaona kuti n’chofunika kwambiri kuposa ubwenzi wanu ndi Yehova?

Mabuku onse 4 a Uthenga Wabwino amanena kuti thupi la Yesu litachotsedwa pamtengopo, Yosefe analikulunga munsalu yabwino kwambiri n’kuliika m’manda ake. (Mat. 27:59-61; Maliko 15:46, 47; Luka 23:53, 55; Yoh. 19:38-40) Munthu amene amatchulidwa kuti anathandizana naye ndi Nikodemo yekha, yemwe anabweretsa zinthu zonunkhiritsa kuti apake thupilo. Popeza anthuwa anali ndi maudindo akuluakulu, ayenera kuti anali ndi antchito amene anawathandiza kunyamula ndi kuika m’manda mtembowo. Koma kaya analidi ndi antchito, zomwe anthu awiriwa anachita inali nkhani yaikulu. Paja aliyense wokhudza mtembo ankakhala wodetsedwa kwa masiku 7 ndipo chilichonse chimene angachikhudze chinkakhalanso chodetsedwa. (Num. 19:11; Hag. 2:13) Choncho ngati anthuwa anakhudza mtembo wa Yesu sakanaloledwa kukhala limodzi ndi anthu ena pa nthawi ya Pasika ndipo sakanachita nawo zikondwerero zonse za pa nthawiyo. (Num. 9:6) Pokonza zoti Yesu aikidwe m’manda, Yosefe analolera kunyozedwa ndi anzake amene ankagwira nawo ntchito. Iye anali wokonzeka kukumana ndi mavuto amene angabwere chifukwa choika Yesu m’manda mwaulemu komanso kudziwika kuti ndi wotsatira wake.

MMENE NKHANI YA YOSEFE IMATHERA

Pambuyo poti Yesu waikidwa m’manda, Baibulo silitchulanso za Yosefe wa ku Arimateya. Zimenezi zikubweretsa funso lakuti: Kodi chinamuchitikira n’chiyani? Yankho ndi lakuti sitikudziwa. Koma malinga ndi zimene takambiranazi, zikuoneka kuti iye anayamba kuuza anthu kuti ndi Mkhristu. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawi yovuta kwambiriyi chikhulupiriro chake chinkawonjezereka, osati kuchepa.

Nkhani imeneyi ikubweretsa funso limene aliyense ayenera kudzifunsa. Funso lake ndi lakuti: Kodi pali chinachake, kaya ndi udindo, ntchito, chuma, achibale kapena mtima wofuna ufulu, chomwe mumaona kuti n’chofunika kwambiri kuposa ubwenzi wanu ndi Yehova?

^ ndime 18 Mzinda wa Arimateya uyenera kuti ndi umene umadziwikanso kuti Rama, womwe masiku ano amauti Rentis (Rantis). Kumeneku ndi kumene kunali kwawo kwa mneneri Samueli, ndipo mzindawu unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 35 kumpoto chakumadzulo kwa Yerusalemu.​—1 Sam. 1:19, 20.