Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zimene Mulungu Akufuna Zikuchitika?

Kodi Zimene Mulungu Akufuna Zikuchitika?

Kodi Zimene Mulungu Akufuna Zikuchitika?

“Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”​—Mateyu 6:10.

JULIO ndi Christina anaona ali ndi chisoni chachikulu zedi ana awo anayi akupsa ndi moto mpaka kumwalira. Galimoto yawo imene anaimitsa pa malo ena inagundidwa ndi galimoto imene dalaivala wake anali ataledzera, ndipo galimoto yawoyo inayaka moto. Mwana wawo wachisanu, Marcos, anapulumutsidwa m’motowo, koma thupi lake linapsa ndipo anapunduka moti sizikanatheka kuti azionekanso monga kale. Anali ndi zaka zisanu ndi zinayi. Bambo ake anali ndi chisoni chosaneneka. Anadzilimbitsa mtima komanso kulimbitsa mtima banja lawo ponena kuti: “Izi ndi zimene Mulungu akufuna, tiyenera kumvetsa zimenezi, kaya zikhale zabwino, zoipa, kapena zina zilizonse.”

Anthu ambiri akakumana ndi zinthu zomvetsa chisoni ngati zimenezi, amachitanso monga mmene anachitira bamboyu. Iwo amaganiza kuti, ‘Ngati Mulungu ndi wamphamvuyonse ndipo amatiganizira, zimene zachitikazi ziyenera kuti mwa njira ina n’zoti zitipindulitse, ngakhale kuti zingakhale zovuta kumvetsa.’ Kodi mumavomereza maganizo ameneŵa?

Maganizo akuti zonse zimene zimachitika, zabwino kapena zoipa, zimasonyeza zimene Mulungu akufuna, nthaŵi zambiri amakhalapo chifukwa cha mawu a Yesu a m’pemphero limene limatchedwa Pemphero la Ambuye, lomwe taligwira mawu pamwambapa. Zimene Mulungu akufuna zikuchitika kumwamba, kodi si choncho? Popemphera kuti ‘Kufuna kwanu kuchitidwe pansi pano,’ kodi sitikhala tikuvomereza kuti zimene zimachitika pa dziko lapansi ndi zimene Mulungu akufuna?

Anthu ambiri sakhulupirira maganizo ameneŵa. Kwa anthu oterowo, zimenezo zimasonyeza kuti Mulungu saganizira anthu amene anawalenga. Amafunsa kuti, ‘Kodi Mulungu wachikondi angafune bwanji kuti zinthu zomvetsa chisoni zichitikire anthu osalakwa? Ngati amafuna kuti anthuwo atengepo phunziro, ndiye phunziro lake n’lotani?’ Mwina mmenemu ndi mmene inunso mumamvera.

Pankhani imeneyi, mbale wake wa Yesu, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Mulungu si amene amayambitsa zinthu zoipa. Motero, n’zoonekeratu kuti si zonse zimene zimachitika pansi pano masiku ano zomwe ndi chifuniro cha Mulungu. Malemba amanenanso za chifuniro cha munthu, chifuniro cha mitundu, ndiponso ngakhale chifuniro cha Mdyerekezi. (Yohane 1:13; 2 Timoteo 2:26; 1 Petro 4:3) Kodi mukuvomereza zoti zimene zinachitikira banja la Julio ndi Christina sizingakhale zofuna za Atate wachikondi wakumwamba?

Motero, kodi Yesu anatanthauza chiyani makamaka pamene anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti: ‘Kufuna kwanu kuchitidwe’? Kodi linangokhala pempho loti Mulungu aziloŵererapo pa nkhani zina zapadera, kapena Yesu anali kutiphunzitsa kupempherera chinthu chinachake chachikulu ndiponso chabwinopo, chomwe ndi kusintha kwa zinthu kumene anthu onse angayembekezere? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Car: Dominique Faget-STF/​AFP/​Getty Images; child: FAO photo/​B. Imevbore