Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Rebeka Anali Mkazi Wolimbikira Ntchito Ndiponso Woopa Mulungu

Rebeka Anali Mkazi Wolimbikira Ntchito Ndiponso Woopa Mulungu

Rebeka Anali Mkazi Wolimbikira Ntchito Ndiponso Woopa Mulungu

TIYEREKEZE kuti mufunika kusankhira mwana wanu mkazi. Kodi mukanasankha munthu wotani? Kodi mkaziyo akanafunika kukhala wotani? Kodi mukanafunafuna munthu wokongola, wanzeru, wokoma mtima, ndi wolimbikira ntchito? Kapena kodi mukanayamba mwafufuza ziyeneretso zina osati zimenezi?

Abrahamu anakumana ndi vuto limeneli. Yehova anamulonjeza kuti mbadwa zake zidzalandira madalitso kudzera mwa mwana wake Isake. Pamene tikuyamba kuona nkhaniyi, Abrahamu n’kuti atakalamba, koma mwana wake anali asanakwatire. (Genesis 12:1-3, 7; 17:19; 22:17, 18; 24:1) Popeza kuti Isake anali kudzalandira madalitso pamodzi ndi mkazi amene adzam’kwatira komanso ndi ana amene adzabereka naye, Abrahamu anakonza zopeza mkazi womuyenerera Isake. Chinthu chofunika kwambiri n’chakuti mkaziyo anayenera kukhala mtumiki wa Yehova. Popeza ku Kanani, kumene Abrahamu anali kukhala, sikukanapezeka mkazi wotero, anafunika kukafufuza kwina. Munthu amene anasankhidwa pomalizira pake anali Rebeka. Kodi anam’peza bwanji? Kodi anali mkazi wokonda zinthu zauzimu? Kodi tingaphunzire zotani mwa kuona chitsanzo chake?

Kufunafuna Mkazi Woyenera

Abrahamu anatuma wantchito wake wamkulu, mwachionekere anali Eliezere, kupita kudziko lakutali la Mesopotamiya kuti akam’tengere Isake mkazi pakati pa abale a Abrahamu, anthu amenenso anali kulambira Yehova. Nkhaniyi inali yaikulu kwambiri moti Abrahamu analumbiritsa Eliezere kuti asakatenge Mkanani kukhala mkazi wa Isake. Ndi zochititsa chidwi kuona khama la Abrahamu pankhaniyi.​—Genesis 24:2-10.

Atayenda ulendo wopita ku mudzi wa abale a Abrahamu, Eliezere anafika ndi ngamila khumi pa chitsime. Yerekezani kuti mukuona zomwe zikuchitika! Ndi madzulo, ndipo Eliezere akupemphera kuti: “Taonani, ine ndiima pa chitsime cha madzi; ndipo ana aakazi a m’mudzi atuluka kudzatunga madzi; ndipo pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, Tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, Imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake.”​—Genesis 24:11-14.

Mkazi aliyense wa m’derali ayenera kuti anali kudziŵa kuti ngamila yaludzu imamwa madzi ambiri (mpaka malita 100). Motero mkazi amene akanadzipereka kumwetsa ngamila khumi anafunika kukonzekera kugwira chintchito chachikulu. Kuchita zimenezi ena akungomuyang’anira osam’thandiza kukanasonyeza kuti ndi wamphamvu, woleza mtima, wodzichepetsa ndiponso wokoma mtima kwa anthu ndiponso kwa nyama.

Ndiyeno n’chiyani chinachitika? “Asanathe kunena, taonani, anatuluka Rebeka, amene anam’bala Betuele, mwana wamwamuna wa Milika, mkazi wa Nahori mphwake wa Abrahamu, ndi mtsuko wake paphewa pake. Ndipo namwaliyo anali wokongola kwambiri m’maonekedwe ake, ndiye namwali . . . ndipo anatsikira kukasupe, nadzaza mtsuko wake, nakwera. Ndipo mnyamatayo anam’thamangira kukomana naye, nati, Ndimwetu madzi pang’ono a m’mtsuko mwako. Ndipo anati, Imwa mbuyanga; nafulumira nayangata mtsuko m’manja mwake namwetsa iye.”​—Genesis 24:15-18.

Kodi Rebeka Anali Woyenera?

Rebeka anali mdzukulu wa mchimwene wa Abrahamu, ndipo analinso wa makhalidwe abwino kuwonjezera pa kukongola kwake. Sanachite mantha kulankhula ndi munthu wachilendo, komanso sanali womasuka mopambanitsa. Eliezere atapempha madzi, anam’patsa kuti amwe. Tingayembekezere munthu aliyense kuchita zimenezi, popeza timatero pofuna kusonyeza ulemu. Koma bwanji za mbali yachiŵiri ya zimene Eliezere anatchula m’pemphero lija?

Rebeka anati: “Imwa mbuyanga.” Koma sanalekeze pomwepo. Rebeka anapitiriza kuti: “Ndidzatungiranso ngamila zako, mpaka zitamwa zonse.” Anadzipereka kuchita zochuluka kuposa zimene munthu angayembekezere. Modzipereka, ‘anafulumira kuthira madzi a m’mtsuko wake m’chomwera, n’kuthamangiranso kuchitsime kukatunga, nazitungira ngamila zake zonse.’ Anajijirika nayo ntchito. Nkhaniyo imati: “Munthuyo ndipo anamyang’anira iye.”​—Genesis 24:19-21.

Atamva kuti mtsikanayo ndi wachibale wa Abrahamu, Eliezere anawerama ndi kuthokoza Yehova. Anamufunsa ngati m’nyumba ya bambo ake muli malo oti iye pamodzi ndi anthu amene anali nawo angagone. Rebeka anavomera ndi kuthamangira kumudzi kukafotokoza za alendowo.​—Genesis 24:22-28.

Atamvetsera nkhani ya Eliezere, mchimwene wa Rebeka, Labani, ndi bambo ake, Betueli, anaona kuti Mulungu ndiye anali kuyendetsa zinthu. Kunena zoona Rebeka anayenera kukhala mkazi wa Isake. Iwo anati: “Mtenge ndi kumuka, akhale mkazi wa mwana wa mbuyako, monga wanena Yehova.” Kodi Rebeka anamva bwanji? Atafunsidwa ngati akufuna kunyamuka nthaŵi yomweyo, iye anayankha ndi mawu amodzi m’Chihebri, omwe amatanthauza kuti: “Ndidzanka.” Sanakakamizidwe kuvomera ukwatiwu. Abrahamu anauza Eliezere kuti adzamasuka pa lumbiro lake ‘ngati mkaziyo sadzafuna’ kuchoka. Koma Rebeka nayenso anaona kuti Mulungu anali kuyendetsa nkhaniyi. Ndiye popanda kuzengereza, iye anasiya banja lake kupita kukakwatiwa ndi mwamuna amene anali asanamuonepo. Kusankha zochita molimba mtima kumeneko ndi umboni waukulu wakuti anali ndi chikhulupiriro. Kunena zoona, uyu ndiye analidi mkazi woyenera.​—Genesis 24:29-59.

Pokumana ndi Isake, Rebeka anaphimba kumutu kusonyeza kugonjera. Isake anam’tenga kukhala mkazi wake, ndipo mosakayikira, chifukwa cha makhalidwe ake abwino, Isake anamukonda mkaziyu.​—Genesis 24:62-67.

Ana Aamuna Amapasa

Rebeka anakhala wopanda mwana zaka pafupifupi 19. Kenako anakhala ndi pakati pa mapasa, koma anavutika napo kwambiri, chifukwa chakuti anawo anali kulimbana m’mimba mwake, zomwe zinachititsa Rebeka kudandaulira Mulungu. Nafe tingachite chimodzimodzi tikakumana ndi mavuto aakulu pamoyo wathu. Yehova anamva kudandaula kwa Rebeka ndipo anamulimbikitsa. Adzakhala nakubala wa mitundu iŵiri ya anthu, ndipo “wamkulu adzakhala kapolo wa wamng’ono.”​—Genesis 25:20-26.

N’kutheka kuti si mawu okhaŵa amene anachititsa Rebeka kukonda kwambiri mwana wake wamng’ono Yakobo. Anawo anali osiyana. Yakobo anali “wofatsa,” koma Esau anali ndi mtima wonyalanyaza zinthu zauzimu moti anagulitsa kwa Yakobo ukulu wake, ufulu wake wolandira choloŵa cha malonjezo a Mulungu, ndi chakudya chongodya kamodzi. Zomwe Esau anachita pokwatira akazi aŵiri achihiti zinasonyeza kunyalanyaza, ngakhalenso kunyoza kumene, zinthu zauzimu, zimene zinachititsa makolo ake kuvutika kwambiri.​—Genesis 25:27-34; 26:34, 35.

Kum’pezera Yakobo Madalitso

Baibulo silifotokoza ngati Isake ankadziŵa kuti Esau adzakhala kapolo wa Yakobo. Mulimonse mmene zinalili, Rebeka ndi Yakobo ankadziŵa kuti Yakoboyo ndi amene anayenera kudalitsidwa. Rebeka sanachedwe kuchitapo kanthu atangomva kuti Isake akufuna kudalitsa Esau akam’phikira nyama yakuthengo yomwe anali kuikonda kwambiri. Rebeka anali asanasiyebe kulimbikira ndi kuchita changu pogwira ntchito monga mmene ankachitira ali mtsikana. ‘Anauza’ Yakobo kuti am’patsire tiana ta mbuzi tiŵiri, kuti adzaphikire mwamuna wake chakudya chomwe anali kuchikonda kwambiri. Kenako Yakobo adzanamizire kuti ndi Esau n’cholinga choti akalandire madalitsowo. Yakobo anakana. Bambo wake akanatha kutulukira chinyengo chakecho n’kum’temberera. Rebeka analimbikirabe kuti ayenera kuchita zimenezo. Anati: “Pa ine likhale temberero lako mwana wanga.” Kenako anaphika chakudyacho, anam’chititsa Yakobo kuoneka ngati Esau, ndipo anamuuza kuti apite kwa mwamuna wake.​—Genesis 27:1-17.

Malemba sakunena kuti n’chifukwa chiyani Rebeka anachita zimenezi. Anthu ambiri amati analakwa, koma Baibulo silitero, ndiponso Isake sanam’dzudzule Yakobo atatulukira kuti walandira madalitso. M’malo mwake Isake anawonjezera madalitsowo. (Genesis 27:29; 28:3, 4) Rebeka anali kudziŵa zomwe Yehova analosera zokhudza ana ake. Motero anali kuchita zinthu mofuna kuonetsetsa kuti Yakobo walandira madalitso amene anayenera kulandira. Izi zinali zogwirizana kwambiri ndi zofuna za Yehova.​—Aroma 9:6-13.

Yakobo Atumizidwa ku Harana

Rebeka analepheretsa zolinga za Esau mwa kulangiza Yakobo kuti athaŵe mpaka mkwiyo wa mchimwene wake utaphwa. Anapempha chilolezo kwa Isake kuti Yakobo achite zimenezo koma mokoma mtima anapeŵa kutchula za mkwiyo wa Esau. M’malo mwake, analankhula moti mwamuna wakeyo avomere pofotokoza mochenjera nkhaŵa yake yoti Yakobo angakwatire Mkanani. Mfundo imeneyi inali yokwanira kukopa Isake kuti auze Yakobo kupeŵa ukwati wotero ndi kum’tumiza ku banja la Rebeka kuti akakwatire mkazi woopa Mulungu. Palibe paliponse pamene pamanena kuti Rebeka anadzaonananso ndi Yakobo, koma zochita zake zinapindulitsa kwambiri mtundu wa Israeli wam’tsogolo.​—Genesis 27:43–28:2.

Timamusirira Rebeka chifukwa cha zomwe timadziŵa za iye. Anali wokongola, koma kukongola kwake kwenikweni kunagona pa kudzipereka kwake kwa Mulungu. Ndi zimene Abrahamu ankafuna mwa mpongozi wake. Mosakayikira makhalidwe ake ena abwino anaposa zonse zimene Abrahamu ankayembekezera. Chikhulupiriro chake ndiponso kulimba mtima kwake potsatira malangizo a Mulungu, komanso changu chake, kudzichepetsa, ndiponso kuchereza kwake mowoloŵa manja ndiwo makhalidwe amene akazi onse achikristu ayenera kutsanzira. Ameneŵa ndi makhalidwe amene Yehova amafuna mwa mkazi wachitsanzo chabwino kwambiri.