Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ubatizo Unayambira pa Mwambo Wosamba wa Ayuda?

Kodi Ubatizo Unayambira pa Mwambo Wosamba wa Ayuda?

Kodi Ubatizo Unayambira pa Mwambo Wosamba wa Ayuda?

YOHANE MBATIZI analalikira za “ubatizo wa kutembenuka mtima.” Yesu nayenso analamula ophunzira ake kuti aphunzitse anthu ndi kuwabatiza.​—Marko 1:4; Mateyu 28:19.

Baibulo limasonyeza kuti ubatizo wachikristu umafuna kuti thupi lonse la munthu wobatizidwayo limizidwe. Buku lakuti Jesus and His World, limati: “N’zotheka kuona miyambo yofanana ndi imeneyi m’zipembedzo zambiri, zakale ndiponso zamakono, m’mayiko ambirimbiri ndiponso m’zikhalidwe zosiyanasiyana.” Bukuli limanenanso kuti, “ubatizo wachikristu . . . unayambira ku Chiyuda.” Kodi zimenezi n’zoona?

Maiwe Omwe Ayuda Ankasambiramo Mwamwambo

Akatswiri a mbiri ya zinthu zakale atakumba kufupi ndi malo omwe kunali kachisi ku Yerusalemu, anapeza malo kapena kuti maiwe osambiramo mwamwambo okwana pafupifupi 100, a m’zaka 100 zomalizira za m’ma B.C.E. ndiponso m’zaka 100 zoyambirira za m’ma C.E. Mawu amene analembedwa m’sunagoge m’zaka za m’ma 100 kapena m’ma 200 C.E. amanena za malo osambiramo amenewa kuti anali a “alendo ofuna kuwagwiritsa ntchito.” Maiwe ena anapezeka m’chigawo china cha ku Yerusalemu kumene kunkakhala anthu olemera ndiponso mabanja a ansembe ndipo pafupifupi nyumba iliyonse inali ndi dziwe lakelake.

Maiwe amenewa anali ndi makona anayi ndipo ankawapanga mwa kusema miyala kapena ankakumba pansi n’kuwaka ndi njerwa kapena miyala. Ankawapaka pulasitala kuti azisunga madzi. Maiwe ambiri anali aakulu mamita 1.8 m’lifupi mwake ndi mamita 2.7 m’litali mwake. Madzi a mvula ankadutsa m’ngalande n’kumalowa m’maiwemo. Maiwewo anali ozama mamita 1.2, kuti munthu akagwada azitha kumira. Masitepe olowera m’madzimo nthawi zina anali kuwagawa pakati ndi khoma lalifupi. Anthu akuganiza kuti mbali imodzi ya masitepewo inali yolowera m’madzimo pokadziyeretsa, ndipo munthu akatha kusamba ankatulukira mbali ina ya masitepewo kuti asadetsedwenso.

Maiwe amenewa ankawagwiritsa ntchito pochita mwambo woyeretsa wa Ayuda. Kodi zimenezi zinkatanthauza chiyani?

Chilamulo ndi Mwambo pa Nkhani Yosamba

Chilamulo cha Mose chinatsindika kufunika koti anthu a Mulungu azikhala oyera, mwauzimu ngakhalenso mwakuthupi. Panali zinthu zambiri zosiyanasiyana zimene zinkachititsa Aisrayeli kukhala odetsedwa ndipo ankafunikira kudziyeretsa posamba ndiponso kuchapa zovala zawo.​—Levitiko 11:28; 14:1-9; 15:1-31; Deuteronomo 23:10, 11.

Yehova Mulungu ndi waudongo ndipo woyera pa chilichonse. N’chifukwa chake ansembe ndi Alevi ankafunikira kusamba manja awo ndi mapazi awo asanayandikire guwa lake lansembe, ndipo akapanda kutero ankaphedwa.​—Eksodo 30:17-21.

Akatswiri amaphunziro amakhulupirira kuti m’zaka 100 zoyambirira, chipembedzo chachiyuda chinakhazikitsa lamulo lakuti munthu aliyense ngakhale amene sanali Mlevi, azidziyeretsa. Aesene ndiponso Afarisi ankasamba mwamwambo nthawi zonse. Ponena za nthawi ya Yesu, lipoti lina linati: “Ayuda ankafunika kudziyeretsa mwamwambo asanalowe kukachisi, asanapereke nsembe, asanalandire udindo wothandiza ansembe ndiponso asanachite ntchito zina zofanana ndi zimenezo.” Mawu a m’buku la Talmud amanena kuti, anthu amene akusamba ankayembekezeka kudzimiza thupi lonse m’madzi.

Yesu anadzudzula Afarisi chifukwa choumirira pa kudziyeretsa mwamwambo. Mwachionekere, iwo ankachita “miyambo yosiyanasiyana yoviika zinthu m’madzi,” kuphatikizapo matsukidwe a “zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.” Yesu ananena kuti Afarisiwo ankanyalanyaza malamulo a Mulungu ndi kukakamiza anthu ena kutsatira miyambo yawo. (Ahebri 9:10, NW; Marko 7:1-9; Levitiko 11:32, 33; Luka 11:38-42) Koma palibe paliponse m’Chilamulo cha Mose pamene pankafuna kuti azimiza thupi lonse.

Kodi ubatizo wachikristu unayambira pa kusamba mwamwambo kumene Ayuda ankachita? Ayi!

Kodi Pali Mgwirizano Uliwonse Pakati pa Mwambo Wosamba ndi Ubatizo Wachikristu

Ayuda ankachita mwambo wodziyeretsa pa iwo wokha. Komabe, ubatizo umene Yohane ankachita, sikuti unali kusamba mwamwambo komwe Ayuda ankakudziwa ayi. Popeza kuti Yohane anali kudziwika monga Mbatizi, zikusonyeza kuti kumiza anthu m’madzi kumene iye ankachita kunali kosiyana ndi kusamba mwamwambo. Ngakhale atsogoleri achipembedzo Achiyuda anatumiza nthumwi kwa Yohane kukam’funsa kuti, kodi “ubatiza bwanji?”​—Yohane 1:25.

Chilamulo cha Mose chinkafuna kudziyeretsa mobwerezabwereza nthawi iliyonse, wolambira akadetsedwa. Zimenezi sizinali choncho ndi ubatizo umene Yohane ankachita kapenanso ubatizo umene Akristu anadzayamba kuchita. Ubatizo wa Yohane unkasonyeza kulapa ndi kusiya moyo umene munthu anali nawo kale. Ubatizo wachikristu umaimira mfundo yakuti munthu wadzipereka kwa Mulungu. Mkristu amadzipereka kamodzi, osati mobwerezabwereza.

Mwambo wosamba umene unkachitika ku nyumba za ansembe Achiyuda ndiponso m’maiwe a pamalo ozungulira Kachisi amene anthu ena onse ankasambiramo unkangofanana chabe ndi ubatizo wachikristu. Matanthauzo a kumira m’madzi pa ubatizo wachikristu ndi pa kusamba mwamwambo anali osiyana kwambiri. The Anchor Bible Dictionary imati: “Akatswiri amaphunziro amavomerezana kuti Yohane [Mbatizi] sanalowe m’malo kapena kutengera ubatizo uliwonse kuchokera kwa mtundu wa anthu uliwonse umene anayandikana nawo,” kutanthauza kuti kuchokera kwa Ayuda. N’chimodzimodzinso ndi ubatizo umene mipingo yachikristu imachita.

Ubatizo wa Mkristu umaimira “funso [kapena kuti pempho] lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu.” (1 Petro 3:21) Umasonyeza kuti munthu wadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse kuti am’tumikire Iye monga wophunzira wa Mwana Wake. Kumiza thupi lonse ndi chizindikiro choyenera cha ubatizo umenewu. Munthu akamira m’madzi mophiphiritsa, amafa ku njira zake zakale za moyo. Akam’vuula m’madzi, amakhala kuti amuukitsa mophiphiritsa kuti ayambe kuchita chifuniro cha Mulungu.

Yehova Mulungu amapereka chikumbumtima chabwino kwa anthu amene amadzipereka choncho ndi kubatizidwa. Choncho mtumwi Petro mouziridwa anauza okhulupirira anzake kuti: ‘[Ubatizo] ukukupulumutsani tsopano.’ Zimenezi ndi zimene mwambo wosamba uliwonse wa Ayuda sukanakwaniritsa.