Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungam’dziwe Bwanji Mulungu?

Mungam’dziwe Bwanji Mulungu?

Mungam’dziwe Bwanji Mulungu?

Ena amakayikira kuti Mulungu amafuna kuti anthu amudziwe. ngati amafunadi kuti anthu am’dziwe, kodi wasonyeza motani zimenezo?

MPOLOTESITANTI wina, amene anasintha zinthu m’zaka za m’ma 1500, John Calvin, ananena molondola kuti anthu sangamudziwe Mulungu paokha, kupatulapo ngati Mulunguyo atadzidziwikitsa yekha kwa anthu. Komabe, ena amakayikira kuti Mulungu amafuna kuti anthu amudziwe. Ndipo ngati amafunadi kuti anthu am’dziwe, kodi wasonyeza motani zimenezo?

Chilichonse chimene Yehova, “Mlengi Wamkulu,” amachita chimakhala ndi chifukwa. Komanso, monga “Mulungu Wamphamvuyonse,” sizim’vuta kukwaniritsa zolinga zake. (Mlaliki 12:1, NW; Eksodo 6:3) Tikudziwa kuti wakhala akufuna kuulula zolinga zake kwa anthu, chifukwa chakuti anauzira mneneri wake Amosi kulemba kuti: “Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri.” Komano, onani kuti lembali likuti Mulungu amaulula chifuniro chake kwa atumiki ake okha basi, anthu amene amamukondadi. Kodi zimenezo sizomveka? Kodi inuyo mumauza ndani nkhani zanu zachinsinsi? Munthu wina aliyense kapena mnzanu wapamtima?​—Amosi 3:7; Yesaya 40:13, 25, 26.

Anthu odzichepetsa amachita chidwi kuona nzeru ndiponso kuchuluka kwa zinthu zimene Mulungu amadziwa, ndipo n’koyeneradi kutero. Komabe, kudabwa kokha sikokwanira ngati tikufuna kupindula ndi nzeru ndiponso zinthu zimene Mulungu amaulula. Baibulo limagogomezera kuti tiyenera kukhala amtima wodzichepetsa ngati tikufuna kuphunzira maganizo a Mulungu, limati: ‘Sunga malamulo anga; tcherera makutu ako kunzeru, lozetsa mtima wako kukuzindikira; itana luntha, ndi kuifuulira kuti ukazindikire; ifunefune ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika.’​—Miyambo 2:1-4.

Zoonadi, munthu wodzichepetsa amene amachita khama lotere, angathedi kum’dziwa Mulungu. Mavesi a m’buku la Miyambo amenewa, amapitiriza n’kuti: “Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m’kamwa mwake.” Inde, anthu amene amafunafuna choonadi moona angathe ‘kuzindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.’​—Miyambo 2:6-9.

Kufunafuna Choonadi

Buku lakuti The Encyclopedia of Religion limati: “Nthawi zambiri, anthu pamoyo wawo amafuna kusiyanitsa zinthu zenizeni ndi zonama, zamphamvu ndi zopanda mphamvu, zoona ndi zachinyengo, zabwino ndi zoipa, zomveka bwino ndi zosokoneza, komanso amafuna kudziwa bwino pakatikati pa zinthu ziwiri zosiyana.” Pofuna kukwaniritsa zimenezi, anthu akhala akufunafuna choonadi kuyambira kalekale. Am’fufuza kwambiri Yehova, amene wamasalmo anamutchula kuti ndi “Mulungu wa choonadi,” ndipo tsopano akumudziwa kwambiri.​—Salmo 31:5.

M’Chihebri, dzina lakuti Yehova kwenikweni limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” (Genesis 2:4) Choncho, tanthauzo la dzina la Mulungu limasonyeza kuti iye ndi Mlengi ndiponso limatiuza zambiri za cholinga chake. Chenicheni n’chakuti, kudziwa ndi kugwiritsa ntchito dzina la Yehova ndi chizindikiro cha chipembedzo choona. N’zoonekeratu kuti Yesu ankadziwa zimenezi. Ponena za ophunzira ake, m’pemphero lake kwa Mulungu, iye anati: “Ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi Ine mwa iwo.”​—Yohane 17:26.

Podalira ubwenzi wake womwe anali nawo ndi Mulungu, Mhebri wina wakale, dzina lake Yosefe, atapatsidwa ntchito yomasulira maloto, ananena mosakayikira kuti: “Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu?”​—Genesis 40:8; 41:15, 16.

Pambuyo pa zaka zambirimbiri, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inalota maloto omwe anzeru ake sanathe kumasulira. Mneneri Danieli anati kwa mfumuyo: “Kuli Mulungu Kumwamba wakuvumbulutsa zinsinsi; Iye ndiye wadziwitsa mfumu Nebukadinezara chimene chidzachitika masiku otsiriza.”​—Danieli 2:28.

Zitsanzo za Yosefe ndi Danieli zimasonyeza kuti Yehova Mulungu amapatsa anthu okhawo amene akum’tumikira, nzeru ndi kuzindikira. N’zoona kuti ngati munthu akufuna kugwirizana ndi Mulungu, afunika kusiyiratu maganizo olakwika amene anali nawo poyamba. Ayuda a m’zaka 100 zoyambirira amene anakhala Akristu, ankayenera kuchita zimenezo. Chifukwa choti anaphunzitsidwa kuyambira ali ana kumvera malamulo amene anakhazikitsidwa ndi dongosolo la zinthu la Chiyuda, ankafunika nthawi yokwanira kuti avomereze Yesu kuti ndi Mesiya. Ndiponso kuti anabwera kudzakwaniritsa Chilamulo cha Mose, chimene chinkagwira ntchito ngati “mthunzi wa zokoma zilinkudza.” (Ahebri 10:1; Mateyu 5:17; Luka 24:44, 45) Chilamulochi chinalowedwa m’malo ndi “chilamulo cha Kristu,” chimene chili chopambana kwambiri kuposa Chilamulo cha Mose.​—Agalatiya 6:2; Aroma 13:10; Yakobo 2:8.

Tonsefe tinabadwira m’dziko losakhulupirira Mulungu. Chifukwa cha uchimo umene tinatengera kuchokera ku banja loyamba la anthu, tinabadwa tili paudani ndi Mulungu ndipo sitidziwa molondola zolinga zake. Tinatengeranso mtima wonyenga. (Yeremiya 17:9; Aefeso 2:12; 4:18; Akolose 1:21) Kuti tikhalenso pa ubwenzi ndi Mulungu, tiyenera kuphunzira ndi kutsanzira mmene Mulungu amaganizira. Kuchita zimenezo sikophweka.

Kumakhala kovuta kusiya maganizo kapena zochita za zipembedzo zonyenga, makamaka ngati tinaphunzitsidwa zimenezi kuyambira tili ana. Koma kodi kupitiriza kuchita zinthu molakwika ndi njira yanzeru? Ndithudi ayi! Koma nzeru ili pa kusintha mmene munthu amaganizira kuti akhale wovomerezeka kwa Mulungu.

Kuzindikira Njira Imene Mulungu Amaperekera Malangizo

Kodi tingapeze kuti thandizo kuti timvetse Mawu a choonadi ndi kukhala mogwirizana ndi Mawuwo? Kale ku Israyeli, Mulungu ankaika anthu odalirika ndiponso okhulupirika paudindo wotsogolera mtunduwo. Mofanana ndi zimenezi, monga Mutu wa mpingo wachikristu masiku ano, Kristu, akutsogolera anthu amene akufunafuna choonadi moona mtima. Akuchita zimenezi kudzera mwa otsatira ake odalirika ndiponso okhulupirika, amene ndi njira yotsogolerera ndi kutetezera anthu amene akufunafuna choonadi moona mtima. (Mateyu 24:45-47; Akolose 1:18) Koma kodi munthu angadziwe bwanji njira imene Mulungu akuperekera malangizo?

Otsatira oona a Yesu Kristu amayesetsa kutsatira makhalidwe ofanana ndi amene Yesu anasonyeza pamene anali munthu. M’dzikoli, lomwe likuipiraipirabe, otsatira a Yesu amenewa ndi osavuta kuwazindikira chifukwa amasonyeza makhalidwe apadera auzimu. (Onani bokosi patsamba 6.) Kodi makhalidwe amenewo amasonyezedwa m’chipembedzo chanu kapena m’chipembedzo cha anzanu omwe mwayandikana nawo nyumba? Kungakhale kopindulitsa kufufuza nkhani imeneyi mothandizidwa ndi Baibulo.

Nonse owerenga magazini athu, tikukulimbikitsani kuti muchite zimenezo mwa kuphunzira Baibulo. Chaka chathachi, anthu oposa 6,000,000, m’mayiko okwana 235 anagwiritsa ntchito mwayi umenewu, mwa kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kupeza nzeru ndi kuzindikira zinthu za Mulungu sikutha ndipo n’kosangalatsa ndi kopindulitsa kwambiri. Bwanji osayamba kuphunzira Baibulo kuti mupeze nzeru ndi kudziwa zinthu zambiri zokhudza Mulungu? Ngati mutayamba kuchita zimenezi simudzanong’oneza bondo. Inde, tingam’dziwedi Mulungu!

[Bokosi patsamba 6]

ANTHU AMENE AMACHITA ZINTHU MOGWIRIZANA NDI MULUNGU . . .

salowerera m’mikangano ya ndale.​—Yesaya 2:4.

amasonyeza zipatso zabwino mwa kuchita chifuniro cha Mulungu.​—Mateyu 7:13-23.

amasonyezana chikondi chenicheni.​—Yohane 13:35; 1 Yohane 4:20.

amalankhula zinthu zogwirizana.​—Mika 2:12.

satsanzira maganizo olakwika ndiponso makhalidwe a dziko.​—Yohane 17:16.

amachitira umboni choonadi ndi kupanga ophunzira.​—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

amasangalala ndi misonkhano nthawi zonse kuti azilimbikitsana.​—Ahebri 10:25.

amatamanda Mulungu monga gulu la padziko lonse.​—Chivumbulutso 7:9, 10.

[Zithunzi patsamba 7]

Tingadziwe Mulungu, patokha, monga banja, ndiponso monga mpingo