Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nzeru za Mulungu Zimaonekera M’chilengedwe

Nzeru za Mulungu Zimaonekera M’chilengedwe

Nzeru za Mulungu Zimaonekera M’chilengedwe

‘[Iye] amatilangiza ife koposa nyama za padziko, amatipatsa nzeru zoposa mbalame za m’mlengalenga.’​—YOBU 35:11.

MBALAME zimatha kuchita zinthu zodabwitsa kwambiri. Zimauluka mwaluso kwambiri moti anthu opanga ndege amachita nazo chidwi zedi. Mbalame za mitundu ina zimauluka mtunda wautali, kuoloka nyanja zikuluzikulu koma osasochera ngakhale kuti panyanjapo sipakhala zizindikiro zothandiza mbalamezo kudziwa kumene zikupita.

Mbalame zilinso ndi luso lina lapadera kwambiri limene limasonyeza nzeru za amene anazilenga. Zimalankhulana mwa kulira ndi kuimba. Taonani zitsanzo izi.

Mbalame Zimalankhulana

Mbalame za mitundu ina zimayamba kulankhulana zidakali m’mazira. Mwachitsanzo, chinziri chachikazi chimaikira dzira limodzi patsiku ndipo chingaikire mazira okwana 8. Chinziri chikamafungatira, anapiye a m’maziramo sakula mofanana, motero pangathe kudutsa maola 48 kuchokera pamene mwanapiye woyamba watuluka m’dzira mpaka pamene womaliza angatuluke m’dzira. Zimenezi zingachititse kuti chinziricho chizivutika kusamalira anapiye a masiku awiri kwinaku chikufungatirabe mazira otsala. M’malo mwa maola 48, pamangotha maola 6 okha. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Ofufuza apeza kuti zimenezi zimatheka chifukwa choti anapiye omwe ali m’mazira amalankhulana ndipo mwanjira inayake amagwirizana kuti atuluke m’maziramo panthawi yofananirako.

Ndipo mbalame zikakula, kawirikawiri zazimuna ndi zimene zimakonda kuimba. Nthawi zambiri zimachita zimenezi m’nyengo yoswana n’cholinga choteteza madera awo kapena pofuna kukopa zazikazi. Mtundu uliwonse wa mbalame uli ndi chilankhulo chake ndipo zimenezi zimathandiza zazikazi kuti zizindikire zazimuna za mtundu wawo.

Kawirikawiri, mbalame zimakonda kuimba m’mawa ndi madzulo. Zimachita zimenezi chifukwa choti panthawiyi kunja sikukhala mphepo ndiponso phokoso lambiri. Ofufuza apeza kuti nyimbo za mbalame zimamveka bwino kwambiri panthawi imeneyi, kuwirikiza nthawi 20 kuposa masana.

Ngakhale kuti nthawi zambiri mbalame zazimuna n’zimene zimakonda kuimba, zonse ndi zazikazi zomwe zimalira mosiyanasiyana ndipo kulira kulikonse kuli ndi tanthauzo lake. Mwachitsanzo, mtundu wina wa mpheta uli ndi kaliridwe kamitundu yokwanira 9. Zimatha kulira mwa mtundu winawake pochenjezana zikaona mbalame yodya mbalame zinzake ikuuluka chapafupi. Komanso zimalira mwa mtundu wina pochenjezana zikaona chinthu choopsa chimene chili pansi.

Mphatso Yapadera Kwambiri

Nzeru zimene mbalame zili nazo n’zochititsa chidwi kwambiri. Komabe tikanena za luso lotha kulankhulana, anthu ndi ochititsa chidwi zedi. Mulungu anapatsa anthu “nzeru zoposa mbalame za m’mlengalenga,” limatero lemba la Yobu 35:11. Ndiponso chimene chimachititsa anthu kukhala apadera kwambiri n’choti amatha kufotokoza bwinobwino zinthu zovuta mwa kugwiritsira ntchito mawu kapena manja.

Mwachibadwa, ana akhanda amatha kuphunzira zinenero zovuta mosiyana ndi zolengedwa zina. Magazini ina inati: “Ana amatha kuphunzira chinenero ngakhale ngati makolo awo sakulankhula nawo mwachindunji. Ana ogontha amatha kuyambitsa chinenero chawochawo chamanja ngakhale kuti sanaphunzitsidwe chinenero choterechi.”​—American Scientist.

Luso lotha kufotokoza maganizo athu ndiponso mmene tikumvera pogwiritsa ntchito mawu kapena manja ndi mphatso yapadera kwambiri imene Mulungu anatipatsa. Koma mphatso yaikulu kwambiri kuposa imeneyi ndiyo kulankhula ndi Mulungu m’pemphero. Ndipotu Yehova Mulungu amatilimbikitsa kuti tizilankhula naye. Baibulo limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”​—Afilipi 4:6.

Tikafunika kusankha chochita pankhani zovuta, Yehova amafuna kuti tigwiritsire ntchito nzeru zopezeka m’Baibulo. Iye angatithandizenso kudziwa mmene tingagwiritse ntchito malangizo ake. Ndipo Yakobe, yemwe analemba nawo Baibulo, anati: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzam’patsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndi mosatonza.”​—Yakobe 1:5.

Kodi Inuyo Zimakukhudzani Bwanji?

Kodi mumamva bwanji mumtima mwanu mukamva nyimbo zokoma za mbalame kapena mawu oyamba a mwana amene akuphunzira kulankhula? Kodi mumaona nzeru za Mulungu m’zinthu zimene iye analenga?

Wamasalmo Davide atasinkhasinkha za mmene iye analengedwera anathokoza Mulungu kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwiza; ntchito zanu n’zodabwiza; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.” (Salmo 139:14) Mosakayikira, pamene mukusinkhasinkha za nzeru za Mulungu zomwe zimaonekera m’chilengedwechi, mudzatha kukhulupirira kwambiri kuti Mulunguyo angakutsogolereni bwino.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Kulankhulana ndi mphatso yochokera kwa Mulungu

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

© Dayton Wild/​Visuals Unlimited