Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesu Achiritsa Anthu Mozizwitsa

Yesu Achiritsa Anthu Mozizwitsa

Zoti Achinyamata Achite

Yesu Achiritsa Anthu Mozizwitsa

Malangizo: Chitani zotsatirazi muli pa malo opanda phokoso. Mukamawerenga mavesiwo, muziyerekezera kuti pamene zinthuzo zinkachitika inuyo munalipo. Yesani kuona nkhanizi m’maganizo mwanu. Yerekezerani kuti mukumva mawu a m’nkhanizi.

ONANI BWINOBWINO NKHANI IYI.​—WERENGANI MATEYO 15:21-28.

Kodi mukuganiza kuti mayiyu anamva bwanji mumtima mwake?

․․․․․

Kodi mukuganiza kuti Yesu analankhula motani m’mavesi otsatirawa?

24 ․․․․․ 26 ․․․․․ 28 ․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Mwa zimene analankhula kapena kuchita, kodi Yesu anasonyeza kangati kuti sanafune kuchiritsa mwana wa mkazi wa mayiyu?

․․․․․

N’chifukwa chiyani poyamba Yesu sanafune kuchiritsa mwanayo?

․․․․․

Nanga n’chifukwa chiyani Yesu anam’chiritsa?

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Mmene Yesu anasonyezera kulolera.

․․․․․

Zimene mungachite potsanzira khalidwe limeneli pamene mukuchita zinthu ndi anthu ena.

․․․․․

ONANI BWINOBWINO NKHANI IYI.​—WERENGANI MALIKO 8:22-25.

Kodi mukuganiza kuti m’mudzi ndi kunja kwa mudziwu munali kuoneka zotani ndiponso kumveka phokoso lotani?

․․․․․

FUFUZANI MOZAMA.

Mukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Yesu anatengera munthu uja kunja kwa mudzi asanam’chiritse?

․․․․․

GWIRITSANI NTCHITO ZIMENE MWAPHUNZIRA. LEMBANI ZIMENE MWAPHUNZIRA PONENA ZA . . .

Mmene Yesu ankaonera anthu olumala, ngakhale kuti iyeyo analibe chilema chilichonse.

․․․․․

M’NKHANI ZIWIRIZI, KODI NDI MFUNDO ZITI ZIMENE ZAKUKHUDZANI KWAMBIRI NDIPO N’CHIFUKWA CHIYANI?

․․․․․