Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?

Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?

Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?

Kodi munayamba mwakhalapo ndi udindo kapena vuto linalake lalikulu mosayembekezera? Kodi mumavutika kupeza chakudya ndi zinthu zina zofunika pamoyo wanu wa tsiku ndi tsiku? Kodi munathawa kwanu ndipo mukukhala movutika m’dziko lina? Kapena kodi muli ndi chisoni chifukwa chakuti munthu amene munkam’konda anamwalira?

KODI mukudziwa kuti mayi ake a Yesu, Mariya, anakumana ndi mavuto onse amene tatchulawa ndipo anawapirira? Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinamuchitikira?

Mariya ndi wotchuka padziko lonse ndipotu zimenezi n’zomveka chifukwa iye anakwaniritsa cholinga chapadera cha Mulungu. Anthu ambiri padziko lonse amamulambira. Tchalitchi cha Katolika chimamulemekeza mwapadera monga mayi wokondeka, wokhulupirika, ndiponso wachifundo. Anthu ambiri amaphunzitsidwa kuti azilambira Mulungu kudzera mwa Mariya.

Kodi inuyo mumamuona bwanji Mariya? Nanga kodi Mulungu amamuona bwanji?

Anapatsidwa Udindo Wapadera

Mariya anali mwana wa Heli, m’Isiraeli wa fuko la Yuda. Nthawi yoyamba imene Mariya anatchulidwa m’Baibulo ndi pamene ankapatsidwa udindo wapadera. Mngelo anafika kwa iye n’kumuuza kuti: “Mtendere ukhale nawe, wodalitsika koposatu iwe, Yehova ali nawe.” Poyamba Mariya anadabwa kwambiri ndi mawu amenewa ndipo “anayamba kusinkhasinkha za moni wamtundu woterewu.” Mngeloyo anamuuza kuti iye wasankhidwa kuti apatsidwe udindo wapadera wokhala ndi pathupi, kubereka ndi kulera Mwana wa Mulungu.​—Luka 1:26-33.

Namwaliyu anapatsidwadi udindo waukulu kwambiri. Kodi iye anamva bwanji? Mariya ayenera kuti ankaopa kuti anthu sakhulupirira nkhaniyi. Ankaganiza kuti akakhala ndi mimba, chibwenzi chake ndi Yosefe chikhoza kutha, ndiponso azinyozedwa ndi anthu. (Deuteronomo 22:20-24) Komabe iye sanakane udindo wofunika umenewu.

Mariya anamvera Yehova Mulungu chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro champhamvu. Iye sanakayikire kuti Mulungu amuthandiza. N’chifukwa chake anati: “Ndinetu mdzakazi wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” Mariya analolera kuvutika chifukwa anaona kuti ntchito imene anapatsidwa inali yofunika kwambiri.​—Luka 1:38.

Mariya atauza Yosefe kuti ali ndi pakati, Yosefe anaganiza zothetsa chibwenzi chawo. Panthawi imeneyi Yosefe ndiponso Mariya ayenera kuti anasokonezeka maganizo kwambiri. Baibulo silinena kuti nthawi imeneyi inali yaitali bwanji. Koma Mariya ndi Yosefe ayenera kuti anasangalala pamene mngelo wa Yehova anaonekera kwa Yosefe. Mngeloyu anafotokozera Yosefe mmene Mariya anakhalira ndi pakati mozizwitsa ndipo anamuuza kuti atenge Mariya kukhala mkazi wake.​—Mateyo 1:19-24.

Nthawi Yovuta

Kwa miyezi yambiri, amayi apakati amakonzekera kubadwa kwa mwana ndipo Mariya ayeneranso kuti anachita chimodzimodzi. Ndipotu ameneyu anali mwana wake woyamba. Koma panachitika zinthu zosayembekezereka zomwe zinamusokoneza kwambiri. Kaisara Augusto analamula kuti pachitike kalembera, ndipo aliyense anafunika kukalembetsera ku mzinda umene anabadwira. Choncho, Yosefe anatenga Mariya, ali ndi pakati pa miyezi 9, ndipo anayenda ulendo wa makilomita pafupifupi 150, ndipo zikuoneka kuti paulendowu anakwera bulu. Panthawiyi ku Betelehemu kunali kutadzaza anthu odzalembetsa ndipo Mariya ankafunikira kupeza malo abwino oti aberekeremo mwana koma malo amene anapezeka anali m’khola. Zinali zovuta kwa Mariya kuberekera m’khola. Iye ayenera kuti ankachita manyazi ndiponso mantha.

Panthawi yovuta imeneyi, Mariya ayenera kuti anapemphera kwa Mulungu ndipo anali ndi chikhulupiriro chakuti Yehova am’thandiza pamodzi ndi mwana wake. Kenako kunabwera abusa amene ankafuna kudzaona mwanayo. Ndipo abusawo ananena kuti angelo anamutcha mwanayo kuti ndi “Mpulumutsi, amene ndi Khristu Ambuye.” Baibulo limanena kuti: “Mariya anasunga mawu onsewa, ndi kuwalingalira mu mtima mwake.” Iye anasinkhasinkha za mawu amenewa ndipo analimbikitsidwa kwambiri.​—Luka 2:11, 16-19.

Ifenso timakumana ndi mavuto pamoyo wathu, ndipo Baibulo limanena kuti tonsefe ‘timangoona zotigwera m’nthawi mwake.’(Mlaliki 9:11) Kodi zimenezi zikatichitikira, timakhumudwa n’kuyamba kumuimba mlandu Mulungu? Tingachite bwino kutsatira chitsanzo cha Mariya ndi kuyandikira kwa Yehova Mulungu. Tingachite zimenezi mwa kuwerenga Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kusinkhasinkha zimene tawerengazo. Zimenezi zingatithandize kuti tipirire mayesero.

Anali Wosauka Ndiponso Wothawa Kwawo

Mariya anakumana ndi mavuto enanso ambiri. Iye anali wosauka ndiponso wothawa kwawo. Kodi inunso mwakumanapo ndi mavuto amenewa? Lipoti lina linanena kuti: “Pafupifupi theka la anthu a padziko lapansi amapeza ndalama zosakwana madola awiri patsiku.” Anthu enanso mamiliyoni ambiri amavutika kupeza zinthu zofunika pamoyo, ngakhale kuti akukhala m’mayiko olemera. Kodi nanunso mukuvutika kupezera banja lanu chakudya, zovala, ndi malo ogona?

Baibulo limasonyeza kuti Yosefe ndi Mariya anali osauka. Mfundo imodzi yolembedwa m’mabuku a uthenga wabwino wa Mateyo, Maliko, Luka ndi Yohane, imasonyeza kuti patatha masiku 40 kuchokera pamene Yesu anabadwa, Mariya ndi Yosefe anapita ku kachisi kukapereka nsembe ya “njiwa ziwiri kapena maunda awiri a nkhunda.” * (Luka 2:22-24) Anthu amene ankaloledwa kupereka nsembe yotereyi, ankakhala osauka kwambiri amene sakanakwanitsa kupereka nsembe ya mwana wa nkhosa. Choncho, Yosefe ndi Mariya ayenera kuti anali osauka. Ngakhale zinali choncho, iwo anali ndi banja labwino ndipo n’zosakayikitsa kuti banja lawo linkakonda kwambiri Mulungu kuposa china chilichonse.​—Deuteronomo 6:6, 7.

Pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Yesu anabadwa, Mariya anakumana ndi vuto linanso lalikulu. Mngelo anauza Yosefe kuti athawire ku Iguputo ndi banja lake. (Mateyo 2:13-15) Kameneka kanali kachiwiri kuti Mariya achoke kwawo, koma ulendo uno anapita ku dziko lachilendo ku Iguputo. Ngakhale kuti ku Iguputo kunalinso anthu ambiri ochokera ku Yuda, Mariya ndi Yosefe ankavutikabe chifukwa kukhala m’dziko lachilendo n’kovuta. Kodi inuyo ndi banja lanu munathawa kwanu chifukwa choopa kuti ana anu angakumane ndi mavuto kapena chifukwa cha mavuto ena? Ngati ndi choncho, mungamvetse mavuto amene Mariya anakumana nawo ku Iguputo.

Anali Mkazi Ndiponso Mayi Wodzipereka

Kupatula pa nkhani za kubadwa ndi kukula kwa Yesu, Mariya sanatchulidwe kwambiri m’mabuku a uthenga wabwino. Komabe, timadziwa kuti Mariya ndi Yosefe anali ndi ana ena 6 kapena kuposerapo. Mwina zimenezi zingakudabwitseni, koma ganizirani zimene mabuku a uthenga wabwino amanena.

Yosefe ankalemekeza kwambiri udindo wobereka Mwana wa Mulungu umene Mariya anali nawo. Motero, iye sanagone naye mpaka Yesu atabadwa. Lemba la Mateyo 1:25 limanena kuti Yosefe “sanagone naye mpaka anabereka mwana wamwamuna.” Mawu akuti “mpaka” amasonyeza kuti Yesu atabadwa, Mariya ndi Yosefe anayamba kukhalira pamodzi ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. * Mayina a ana aamunawo anali Yakobe, Yosefe, Simoni ndi Yuda.​—Mateyo 13:55, 56.

Mariya ankakonda kwambiri Mulungu. Ngakhale kuti Chilamulo sichinkakamiza akazi kupita ku madyerero a Pasika, chaka chilichonse iye ankapita ndi Yosefe ku madyerero amenewa ku Yerusalemu. (Luka 2:41) Ulendowu unali wa makilomita pafupifupi 300, koma iwo ankayendabe ngakhale kuti banja lawo linali likukula. N’zosakayikitsa kuti banja lawo linkasangalala ndi maulendo amenewa.

Akazi ambiri masiku ano amatengera chitsanzo chabwino cha Mariya. Amayesetsa kukwaniritsa udindo wawo wa m’Malemba. Akazi odzipereka amenewa, ndi ofatsa, opirira ndiponso odzichepetsa. Chitsanzo cha Mariya chimawathandiza kukonda kwambiri zinthu zauzimu m’malo mofuna moyo wabwino ndi zosangalatsa. Mofanana ndi Mariya, iwo amadziwa kuti kulambira Mulungu pamodzi ndi mwamuna ndiponso ana awo kumalimbitsa ndi kugwirizanitsa banja lawo.

Pamene Mariya ndi Yosefe anali paulendo wochokera ku phwando ku Yerusalemu limodzi ndi ana awo, anazindikira kuti Yesu amene panthawiyi anali ndi zaka 12, sanali pagululi. Mariya ayenera kuti anavutika maganizo kwambiri pomwe ankafunafuna Yesu kwa masiku atatu. Iye limodzi ndi Yosefe atapeza Yesu ali m’kachisi, Yesuyo anawafunsa kuti:“Simunadziwe kodi kuti ndiyenera kupezeka m’nyumba ya Atate wanga?” Ndipo nkhaniyi imanenanso kuti, “mayi wake anasunga mosamalitsa mawu onsewa mu mtima mwake.” Apanso Mariya anasonyeza kuti ankakonda kwambiri Mulungu. Iye ankaganizira kwambiri zimene zinachitikazi. Patapita zaka zingapo Mariya ayenera kuti anafotokozera anthu olemba mabuku a uthenga wabwino nkhani zimenezi ndiponso zina zimene zinachitika Yesu ali mwana.​—Luka 2:41-52.

Anapirira Imfa ya Mwamuna Wake

Kodi chinachitikira Yosefe, bambo a Yesu omulera n’chiyani? Nthawi yomaliza imene mabuku a uthenga wabwino amatchula Yosefe, ndi pankhani yokhudza zimene Yesu anachita ku kachisi, ali mnyamata. Choncho, ena amaganiza kuti Yosefe satchulidwanso chifukwa choti anamwalira Yesu asanayambe utumiki wake. * Kaya chinamuchitikira n’chiyani, koma mfundo ndi yakuti pamene Yesu ankamaliza utumiki wake, n’kuti Mariya ali mayi wamasiye. Panthawi imene Yesu amafa, anauza mtumwi Yohane kuti azisamalira amayi ake. (Yohane 19:26, 27) Yesu sakananena zimenezi, zikanakhala kuti Yosefe anali moyo panthawiyo.

Mariya ndi Yosefe anakumana ndi zambiri ali limodzi. Anachezeredwa ndi angelo, anathawa wolamulira wankhanza, anasamuka kambirimbiri ndipo ankasamalira banja lalikulu. Iwo ayenera kuti ankacheza, n’kumakambirana za Yesu. Ayeneranso kuti ankakambirana zimene Yesu anali kudzakumana nazo ndiponso ngati iwo akum’lera bwino. Kenako mwadzidzidzi, Mariya anakhala mayi wamasiye.

Kodi inuyo ndinu mayi wamasiye? Kodi mumamvabe chisoni kapena kumva kuti muli nokhanokha, ngakhale kuti papita zaka zambiri chimwalirireni amuna anu? Mariya ayenera kuti anatonthozedwa chifukwa chokhulupirira kuti akufa adzauka. * (Yohane 5:28, 29) Komabe zimenezi sizinathetse mavuto amene Mariya anali nawo. Iye anakumana ndi mavuto amenenso amayi ambiri amasiye amakumana nawo masiku ano, monga kulera ana popanda bambo awo.

Yesu ayenera kuti ndiye ankasamalira banja lawo, Yosefe atamwalira. Koma pamene ang’ono ake amakula nawonso anali ndi udindo wosamalira banjalo. Yesu ali ndi “zaka pafupifupi 30” anachoka pa banjapo n’kuyamba utumiki wake. (Luka 3:23) Mwana akachoka panyumba, makolo ambiri amasangalala komanso amakhumudwa. Amakhala atamuchitira zinthu zambiri kwa nthawi yaitali ndipo akachoka amamva kuti chinachake chikusoweka pamoyo wawo. Kodi nanunso mwana wanu anachoka panyumba n’kukayamba kukhala payekha? Kodi mumasangalala nazo koma n’kulakalakanso akanakhala pafupi? Ngati zili choncho, mutha kumvetsa mmene Mariya anamvera Yesu atachoka panyumba.

Anakumana ndi Mavuto Osayembekezereka

Mariya anakumananso ndi mavuto ena osayembekezereka. Pamene Yesu ankalalikira, anthu ambiri anamutsatira koma azing’ono ake sanamutsatire. Malemba amati: “Abale akewo sanali kukhulupirira mwa iye.” (Yohane 7:5) Mariya ayenera kuti anali atauza ana akewo zimene mngelo anamuuza zakuti Yesu anali “Mwana wa Mulungu” (Luka 1:35) Komabe, Yakobe, Yosefe, Simoni, ndi Yudasi, ankangomuona Yesu monga mkulu wawo basi. Choncho, panyumba pa Mariya panali anthu azikhulupiriro zosiyana.

Kodi Mariya anafooka n’kusiya kuphunzitsa ana akewo? Ayi. Panthawi ina, Yesu akulalikira ku Galileya, anapita panyumba ina kukadya, ndipo anthu ambiri anabwera kudzamvetsera ulaliki wake. Mariya ndi azing’ono ake a Yesu anamutsatiranso ku nyumbayo. Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu akamalalikira pafupi ndi kwawo, Mariya ankamutsatira pamodzi ndi ana ake, n’cholinga chakuti mwina anawo angasinthe maganizo awo.​—Mateyo 12:46, 47.

Mwina inunso mumayesetsa kutsatira Yesu pamene ena m’banja mwanu safuna kumutsatira. Ngati ndi choncho, musakhumudwe komanso musasiye kuthandiza banja lanu. Mofanana ndi Mariya, anthu ambiri ayesetsa kwa nthawi yaitali kuthandiza anthu a m’banja mwawo. Mulungu amayamikira kwambiri khama lathu, ngakhale kuti anthu amene tikuwathandizawo sakusintha.​—1 Petulo 3:1, 2.

Anakumana ndi Vuto Lalikulu Kwambiri

Vuto lalikulu kwambiri komanso lomaliza limene Malemba amasonyeza kuti Mariya anakumana nalo linali lokhudza imfa ya mwana wake. Iye analipo pamene mwana wake ankaphedwa mwankhaza atakanidwa ndi anthu a mtundu wake. Makolo ambiri amaona kuti imfa ya mwana, kaya akhale wamkulu kapena wamng’ono, imakhala yowawa kwambiri. Mofanana ndi mmene Malemba anali atanenera kale, Mariya anamva ngati kuti wapyozedwa ndi lupanga, chifukwa cha imfa ya mwana wake.​—Luka 2:34, 35.

Kodi Mariya analola kuti mayesero amenewa afooketse chikhulupiriro chake mwa Yehova? Ayi chifukwa Baibulo limasonyeza kuti Yesu atafa, Mariya “analimbika kupemphera” limodzi ndi ophunzira a Yesu. Ndipo panthawi imene ankapempherayi, Mariya anali limodzi ndi ana ake omwenso anali atayamba kukhulupirira Yesu. Zimenezi ziyenera kuti zinamusangalatsa kwambiri Mariya. *​—Machitidwe 1:14.

Mariya anali wokhulupirika pamoyo wake wonse kuyambira pamene anali mtsikana, mkazi wokwatiwa, ndiponso kholo. Iye anapeza madalitso auzimu ambiri pamoyo wake. Komanso anapirira mavuto ndi mayesero ambiri. Ifenso tingatsatire chitsanzo cha Mariya tikamakumana ndi mavuto osayembekezereka kapena tikakhala ndi nkhawa zokhudza anthu a m’banja lathu.​—Aheberi 10:36.

Komabe, kodi ndi bwino kupembedza Mulungu kudzera mwa Mariya? Kodi nkhani za m’Baibulo zonena za udindo wapadera wa Mariya zimalimbikitsa kuti tizimulambira?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Imodzi mwa njiwazo inaperekedwa monga nsembe yauchimo. (Levitiko 12:6, 8) Mariya anapereka nsembe imeneyi chifukwa ankadziwa kuti iye, mofanana ndi anthu onse opanda ungwiro, anatengera uchimo kwa munthu woyamba, Adamu.​—Aroma 5:12.

^ ndime 26 Panthawi imene Yesu ankayamba utumiki wake, Yosefe ayenera kuti anali atamwaliradi, chifukwa mabuku a uthenga wabwino amangotchula za amayi, ang’ono, ndi alongo ake a Yesu okha basi. Mwachitsanzo, paukwati wa ku Kana, Mariya analipo ndipo ankagwira nawo ntchito zina, koma palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti Yosefe analipo. (Yohane 2:1-11 ) M’nkhani ina, anthu a m’tawuni ya kwawo kwa Khristu sanatchule Yesu kuti ndi mwana wa Yosefe, koma anamutchula kuti “mwana wa Mariya.”​—Maliko 6:3.

^ ndime 28 Kuti mudziwe zambiri zimene Baibulo limalonjeza pankhani yakuti akufa adzauka, onani mutu 7 wa buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

 Kodi Yesu Anali Ndi Ang’ono Ake Ndiponso Alongo Ake?

Inde anali nawo. Komabe, akatswiri ena amaphunziro a zaubusa amatsutsa zimenezi ngakhale kuti nkhani za m’mabuku a uthenga wabwino zimatsimikizira kuti mfundoyi ndi yoona. (Mateyo 12:46, 47; 13:54-56; Maliko 6:3) Koma akatswiri ena amaphunziro a Baibulo aona kuti pali zifukwa ziwiri zimene zimachititsa anthu kunena kuti Mariya analibe ana ena. Chifukwa choyamba ndi chakuti, matchalitchi ena amafuna kulimbikitsa chiphunzitso chakuti Mariya anali namwali woti sanagonepo ndi mwamuna moyo wake wonse. Chifukwa chachiwiri n’chakuti, anthuwo amaona kuti palibe umboni wosonyeza kuti Mariya anali ndi ana ena.

Mwachitsanzo, matchalitchi ena amanena kuti amene amatchedwa kuti abale ake a Yesu, anali ana amene Yosefe anabereka asanakwatirane ndi Mariya. Koma zimenezi si zoona, chifukwa zikanakhala zoona Yesu sakanakhala woyenera kulowa ufumu wa Davide monga mwana woyamba wa Yosefe.​—2 Samueli 7:12, 13.

Anthu enanso amanena kuti, amene amatchedwa kuti ang’ono ake a Yesu, anali asuweni ake. Koma zimenezi si zoonanso, chifukwa Malemba Achigiriki amagwiritsa ntchito mawu osiyanasiyana potchula “mchimwene,” “msuwani” ndi “wachibale.” N’chifukwa chake katswiri wina wamaphunziro a Baibulo, dzina lake Frank E. Gaebelein, ananena kuti mfundo yakuti abale ake a Yesu anali asuweni ake ndi yosamveka. Pomaliza iye anati: “Mawu akuti ‘abale’ . . . amanena za ana a Mariya ndi Yosefe, omwe ndi ang’ono ake a Yesu a mayi mmodzi.

[Bokosi patsamba 7]

 Mariya Sanaope Kusintha Chipembedzo Chake

Mariya anabadwira m’banja la Chiyuda ndiponso anali m’chipembedzo cha Chiyuda. Nthawi zambiri ankapita kukalambira Mulungu ku sunagoge komanso kukachisi wa ku Yerusalemu. Ataphunzira zambiri zokhudza Mulungu, anazindikira kuti chipembedzo cha makolo ake chaleka kukondweretsa Mulungu. Atsogoleri achipembedzo a Chiyuda anapha Mwana wake, Mesiya. Koma asanamuphe, Yesu anauza atsogoleri achipembedzowo kuti: “Tsopano tamverani! Nyumba yanu akunyanyalirani.” (Mateyo 23:38) Mulungu anasiya kudalitsa chipembedzo chimene Mariya anabadwira.​—Agalatiya 2:15, 16.

Panthawi imene mpingo wachikhristu unkayamba, Mariya ayenera kuti anali ndi zaka 50. Kodi iye anaganiza kuti wakula moti sangasinthe chipembedzo chake? Kapena kodi iye anaona kuti sangasinthe chipembedzo cha makolo ake? Ayi. Mariya anazindikira kuti Mulungu wayamba kudalitsa mpingo wachikhristu, choncho iye sanaope kusintha chipembedzo chake.

[Chithunzi patsamba 5]

Akuthawira ku Iguputo

[Chithunzi patsamba 8]

Imfa ya mwana imakhala yowawa kwambiri kwa mayi