Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Munthu Wapamtima pa Yehova

Munthu Wapamtima pa Yehova

Munthu Wapamtima pa Yehova

KODI n’chiyani chimabwera mumtima mwanu mukaganizira za Davide wotchulidwa m’Baibulo? Kodi mumakumbukira za nthawi imene iye anagonjetsa Goliati, chiphona chachifilisiti? Kapena nthawi imene iye anakabisala kuchipululu pothawa Mfumu Sauli imene inkafuna kumupha? Kodi mumakumbukira za tchimo lake ndi Bati-seba komanso mavuto amene anakumana nawo chifukwa cha tchimolo? Kapena kodi mumakumbukira za ndakatulo zake zouziridwa zimene zimapezeka m’Baibulo m’buku la Masalimo?

Pa moyo wake, Davide anachita zinthu zambiri potumikira Mulungu, anapambana pa zochitika zosiyanasiyana komanso anakumana ndi mavuto ambiri. Koma chimene chimatichititsa chidwi kwambiri ndi zimene mneneri Samueli anafotokoza zokhudza Davide, kuti anali kudzakhala “munthu wapamtima pa [Yehova].”​—1 Samueli 13:14.

Ulosi wa Samueli umenewu unakwaniritsidwa Davide adakali wamng’ono. Kodi inunso simungakonde kunenedwa kuti ndinu wapamtima pa Yehova? Ndiyeno kodi Davide ankachita chiyani pa moyo wake, makamaka pa nthawi imene anali wamng’ono, zimene zinathandiza kuti akhale wapamtima pa Yehova? Tiyeni tione zimene anachita, chifukwa zimenezi ndi zimenenso zingakuthandizeni.

Banja Limene Ankachokera Komanso Ntchito Imene Ankagwira

Jese, yemwe anali bambo ake a Davide komanso mdzukulu wa Rute ndi Boazi, ayenera kuti anali mtumiki wodzipereka wa Yehova. Pamene Davide ndi azichimwene ake 7 komanso azichemwali ake awiri anali ana, Jese anawaphunzitsa Chilamulo cha Mose. Mu salimo lina limene Davide analemba, anadzitchula kuti ndi mwana wa ‘kapolo wamkazi’ wa Yehova. (Salimo 86:16) Zimenezi zachititsa ena kukhulupirira kuti amayi ake a Davide, omwe sanatchulidwe m’Baibulo, nawonso anathandiza kwambiri kuti Davide akhale wokonda Yehova. Katswiri wina ananena kuti: “N’kutheka kuti amayi ake a Davide ndi amene anayamba kumufotokozera nkhani yochititsa chidwi ya mmene Mulungu anachitira zinthu ndi anthu ake m’mbuyomo,” kuphatikizapo nkhani ya Rute ndi Boazi.

Pa nthawi yoyamba imene Baibulo limatchula Davide, n’kuti iye ali kamnyamata komanso m’busa ndipo anali ndi udindo wosamalira nkhosa za bambo ake. N’kutheka kuti ntchito imeneyi inkachititsa kuti Davide azikhala kutchire yekhayekha kwa nthawi yaitali usana ndi usiku. Taganizirani mmene zinthu zinkakhalira pa nthawi imeneyo.

Davide ndi makolo ake komanso abale ake, ankakhala ku Betelehemu, tauni yaing’ono imene inali m’mapiri m’dziko la Yuda. Minda yambiri yozungulira Betelehemu, yomwe inali yamiyala, ankalimamo mbewu zosiyanasiyana. M’malo otsetsereka komanso m’zigwa munkalimidwa maolivi, mphesa, ndiponso zipatso zina. N’kutheka kuti m’nthawi ya Davide, malo onse okwera amene sankalimidwa ankawagwiritsa ntchito ngati malo odyetserako ziweto. Kupitirira minda ndi malo odyetsera ziwetowa, kunali chipululu cha Yuda.

Ntchito yoweta nkhosa imene Davide ankagwirayi inali ndi kuopsa kwake. Kumapiri kumeneku n’kumene Davide anakumana ndi mkango komanso chimbalangondo zimene zinkafuna kugwira nkhosa zake. * Davide anali wolimba mtima moti anathamangitsa zilombozo n’kuzipha ndipo analanditsa nkhosazo. (1 Samueli 17:34-36) N’kutheka kuti nthawi imeneyi ndi imene Davide anaphunzira luso loponya miyala pogwiritsa ntchito gulaye. Tauni yakwawo inali pafupi ndi dera la Abenjamini ndipo ena mwa anthu a m’fukoli anali odziwa kuponya miyala. Anthu amenewa anali ndi luso loponya miyala ndipo “sanali kuphonya.” Nayenso Davide anali ndi luso limeneli.​—Oweruza 20:14-16; 1 Samueli 17:49.

Ankagwiritsa Ntchito Bwino Nthawi

Nthawi zambiri m’busa ankakhala yekhayekha kutchire. Komabe Davide ankapeza zochita kuti asamatope ndi ntchitoyi. Iye ankagwiritsa ntchito nthawi imene ankakhala pamalo opanda zododometsa amenewa kuganizira mozama za Mulungu. Zikuoneka kuti mfundo zina zimene Davide anaziphatikiza mu masalimo amene analemba, ndi zimene ankaziganizira ali wachinyamata. N’kutheka kuti iye ankasinkhasinkha za kuchepa kwa munthu poyerekeza ndi zinthu za m’chilengedwe chonse komanso kudabwitsa kwa zinthu zakuthambo monga dzuwa, mwezi ndiponso nyenyezi, zimene ndi “ntchito ya zala [za Yehova].” Zikuoneka kuti nthawi imeneyi ndi imene anaganizira za nthaka yachonde, mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, mbalame komanso “zilombo zakutchire.”​—Salimo 8:3-9; 19:1-6.

N’zosakayikitsa kuti zimene Davide anakumana nazo monga m’busa zinamuthandiza kumvetsa chikondi cha Yehova kwa atumiki ake okhulupirika. Choncho Davide anaimba kuti: “Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasowa kanthu. Amandigoneka m’mabusa a msipu wambiri. Amandiyendetsa m’malo opumira a madzi ambiri. Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani, sindikuopa kanthu, pakuti inu muli ndi ine. Chibonga chanu ndi ndodo yanu ndi zimene zimandilimbikitsa.”​—Salimo 23:1, 2, 4.

Mwina mungadabwe kuti kodi zimenezi zikukukhudzani bwanji? Zikukukhudzani chifukwa chakuti, chimodzi mwa zinthu zimene zinachititsa kuti Davide akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso kuti atchedwe “munthu wapamtima pake,” n’chakuti iye ankaganizira mozama kwambiri za ntchito za Yehova komanso za ubwenzi wake ndi Mulungu. Kodi inunso mumachita zimenezi?

Kodi munayamba mwatamandapo Mlengi chifukwa choganizira mozama zina mwa zinthu zimene iye analenga? Nanga kodi kuganizira za makhalidwe a Yehova amene amasonyeza akamachita zinthu ndi anthu kunayamba kwakupangitsani kumukonda kwambiri? Kuti muchite zimenezi, muyenera kumapeza nthawi yopemphera komanso kuganizira mozama Mawu a Mulungu ndiponso zinthu zimene iye analenga. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kumudziwa bwino Yehova ndipo zimenezi zingachititse kuti muyambe kumukonda. Ana ndi akulu omwe angathe kuchita zimenezi kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova. Zikuoneka kuti Davide anakhala pa ubwenzi ndi Yehova kuyambira ali wamng’ono. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?

Davide Anadzozedwa Kuti Adzakhale Mfumu

Mfumu Sauli itasonyeza kuti siikuyenera kupitiriza kulamulira anthu a Mulungu, Yehova anauza mneneri Samueli kuti: “Kodi ulirira Sauli mpaka liti, pamene ine ndamukana kuti alamulire monga mfumu ya Isiraeli? Thira mafuta m’nyanga yako ndipo unyamuke. Ndikutumiza kwa Jese wa ku Betelehemu, chifukwa ndapeza munthu pakati pa ana ake aamuna woti akhale mfumu yanga.”​—1 Samueli 16:1.

Mneneri wa Mulunguyu atafika ku Betelehemu, Jese anasonkhanitsa ana ake aamuna. Kodi Samueli adzoza ndani pa gululi? Samueli ataona Eliyabu, yemwe anali wamkulu pa onse, anaganiza kuti: ‘Ndi ameneyu.’ Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake, pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera. Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” Yehova anakananso Abinadabu, Shama komanso abale awo ena anayi. Nkhaniyi imapitiriza kuti: “Pamapeto pake Samueli anafunsa Jese kuti: ‘Kodi anyamata ako onse ndi omwewa basi?’ Iye anayankha kuti: ‘Wamng’ono kwambiri sanabwerebe, pakuti akuweta nkhosa.’”​—1 Samueli 16:7, 11.

Poyankha zimenezi, mwina Jese ankaganiza kuti: ‘Koma Davide sangakhale munthu amene akufuna.’ Popeza Davide anali wamng’ono pa onse woti sankamuwerengera kwenikweni, anamupatsa ntchito yoweta nkhosa. Koma Mulungu anasankha iyeyo. Yehova amaona mmene mtima ulili ndipo n’zosakayikitsa kuti anaona chinachake cha mtengo wapatali mwa mnyamata ameneyu. Choncho Jese ataitanitsa Davide, Yehova anauza Samueli kuti: “‘Ndi ameneyu! Nyamuka umudzoze.’ Choncho Samueli anatenga nyanga ya mafuta ndi kum’dzoza pakati pa abale ake. Zitatero, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka m’tsogolo.”​—1 Samueli 16:12, 13.

Sizikudziwika kuti pa nthawiyi Davide anali ndi zaka zingati. Koma patapita nthawi, azichimwene ake atatu akuluakulu, omwe ndi Eliyabu, Abinadabu ndi Shama analowa m’gulu lankhondo la Sauli. Mwina achimwene ake ena asanu anali adakali ang’onoang’ono moti sakanakhala asilikali. N’kutheka kuti onsewa anali asanakwanitse zaka 20, zomwe ndi zaka zimene anyamata ankalowera usilikali ku Isiraeli. (Numeri 1:3; 1 Samueli 17:13) Mulimonsemo, pamene Yehova ankasankha Davide n’kuti Davideyo ali wamng’ono kwambiri. Koma ngakhale anali wamng’ono, zikuoneka kuti anali wokonda zinthu zauzimu. Iye ayenera kuti anali pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova chifukwa chokonda kuganizira kwambiri zinthu zimene ankadziwa zokhudza Mulungu.

Masiku anonso achinyamata ayenera kulimbikitsidwa kuchita zimenezo. Choncho, kodi makolonu mumalimbikitsa ana anu kuganizira mozama zinthu zauzimu, kuchita chidwi ndi zinthu zimene Mulungu analenga komanso kuphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza Mlengi? (Deuteronomo 6:4-9) Komanso achinyamatanu, kodi panokha mumayesetsa kuchita zimenezi? Mabuku othandiza kuphunzira Baibulo, monga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! * angakuthandizeni kuchita zimenezi.

Anali ndi Luso Loimba Zeze

Mawu a m’masalimo ambiri amene Davide analemba amatithandiza kudziwa kenakake kokhudza nthawi imene anali m’busa. N’chimodzimodzinso ndi mmene ankaimbira zeze. N’zoona kuti panopa palibe amene angadziwe kuti nyimbo zimenezi zinkaimbidwa bwanji. Komabe tikaona mawu a nyimbozi, timadziwa kuti Davide anali ndi luso loimba. Ndipotu chimene chinachititsa kuti iye aitanidwe kuchoka kubusa n’kupita kumakaimbira nyimbo Mfumu Sauli, n’chakuti anali ndi luso loimba zeze.​—1 Samueli 16:18-23. *

Kodi Davide anaphunzira kuti luso limeneli ndipo analiphunzira liti? Ayenera kuti anaphunzira luso limeneli pa nthawi imene ankaweta nkhosa kutchire. Choncho n’zoonekeratu kuti Davide anayamba kuimba nyimbo zotamanda Mulungu adakali wamng’ono. Ndipotu Yehova anamusankha chifukwa choti anali wokonda zinthu zauzimu komanso anali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.

Zimene Davide ankachita atakula zimasonyeza kuti anapitirizabe kukhala pa ubwenzi ndi Yehova. Komabe zikuoneka kuti zonse zimene ankachita atakula zinachokera pa zimene anaphunzira ali wamng’ono pa nthawi imene ankaweta nkhosa m’madera ozungulira Betelehemu. Davide anaimbira Yehova kuti: “Ndakumbukira masiku akale. Ndasinkhasinkha zochita zanu zonse, ndipo ndakhala ndikuganizira ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.” (Salimo 143:5) Mawu ochokera pansi pa mtima a mu salimo limeneli komanso amene amapezeka m’masalimo ena amene Davide analemba, ndi olimbikitsa kwambiri kwa anthu onse amene amafuna kukhala anthu apamtima pa Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Zimbalangondo zoderapo za ku Siriya, zimene zinkapezeka ku Palesitina, zinkakhala zikuluzikulu zolemera pafupifupi makilogalamu 140. Zimbalangondo zimenezi zinkatha kupha munthu kapena nyama ndi mapazi awo akuluakulu. M’dera limeneli munkapezekanso mikango yambiri. Lemba la Yesaya 31:4 limanena kuti ngakhale “abusa ambirimbiri” sakanatha kuthamangitsa “mkango wamphamvu” kuti usiye nyama imene wagwira.

^ ndime 20 Magazini amenewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 22 Munthu amene ankagwira ntchito kunyumba kwa Mfumu Sauli, yemwe anauza mfumuyo za Davide, ananenanso kuti Davideyo anali “wolankhula mwanzeru ndi wooneka bwino, komanso Yehova [anali] naye.”​—1 Samueli 16:18.