Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena

Kodi N’chifukwa Chiyani Akhristu Amabatizidwa?

Kodi N’chifukwa Chiyani Akhristu Amabatizidwa?

Nkhani ino ili ndi mafunso amene mwina mumafuna mutadziwa mayankho ake ndipo ikusonyeza mavesi a m’Baibulo amene mungapezeko mayankhowo. A Mboni za Yehova ndi okonzeka kukambirana nanu mafunso amenewa.

1. Kodi ubatizo wachikhristu umatanthauza chiyani?

Ubatizo ndi umboni woti munthu akufuna kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Choncho, Mkhristu aliyense ayenera kubatizidwa, osati ali mwana koma ali wamkulu moti angathe kuphunzira za Mulungu n’kukhala wophunzira wa Yesu. (Machitidwe 8:12; 1 Petulo 3:21) Timakhala ophunzira a Yesu tikamaphunzira ndi kuchita zinthu zimene Yesu anatilamula.​—Werengani Mateyu 28:19, 20.

M’nthawi ya atumwi, anthu ambiri akangomva za Mulungu ndi Yesu sankachedwa kuchitapo kanthu. Mwachitsanzo, munthu wina atangomva kuti imfa ya Yesu inatsegula njira yoti anthu apeze chipulumutso, nthawi yomweyo anakhala wophunzira wa Yesu. Masiku anonso pali anthu ambiri amitima yabwino amene asankha kukhala otsatira a Yesu.​—Werengani Machitidwe 8:26-31, 35-38.

2. Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anabatizidwa?

Pamene Yesu ankabatizidwa ndi Yohane M’batizi mumtsinje wa Yorodano n’kuti ali ndi zaka pafupifupi 30. Ubatizo wa Yesu unasonyeza kuti Yesuyo anasankha kuchita zimene Mulungu anafuna kuti iye achite. (Aheberi 10:7) Zimenezi zinaphatikizapo kuvomereza kupereka moyo wake monga nsembe kuti awombole anthu ku uchimo. Ngakhale asanabwere padziko lapansi, Yesu ankakonda Atate wake, Yehova, komanso ankawamvera.​—Werengani Maliko 1:9-11; Yohane 8:29; 17:5.

3. Kodi n’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kubatizidwa?

Mosiyana ndi Yesu amene anali wosachimwa, ifeyo ndi ochimwa. Koma nsembe ya Yesu imathandiza kuti tikhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. (Aroma 5:10, 12; 12:1, 2) Choncho n’zotheka kuti tikhale naye pa ubwenzi wapadera monga ana ake. (2 Akorinto 6:18) Kodi munthu amapeza bwanji mwayi umenewu? Munthu amayenera kudzipereka kwa Yehova ndipo amachita zimene mwa kupemphera payekha kwa Yehova n’kumulonjeza kuti adzachita chifuniro chake kwa moyo wake wonse. Kenako, amabatizidwa posonyeza kuti anadzipereka kwa Yehova.​—Werengani Mateyu 16:24; 1 Petulo 4:2.

4. Kodi muyenera kuchita chiyani kuti mubatizidwe?

A Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi aliyense amene akufuna kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Kuphunzira Baibulo komanso kupezeka pa misonkhano yachikhristu kungakuthandizeni kuti muzikonda kwambiri Mulungu komanso kuti muzimukhulupirira. Kungakuthandizeninso kuti mukhale ndi makhalidwe abwino. Kukhala ndi makhalidwe abwino monga chikondi, chikhulupiriro ndiponso makhalidwe ena amene Mulungu amasangalala nawo, kungatithandize kukwaniritsa lonjezo lathu lakuti tidzatumikira Yehova mpaka kalekale.​—Werengani Yohane 17:3; Aheberi 10:24, 25.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 18 m’buku ili, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.