Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mavuto Onsewa Atha Posachedwapa

Mavuto Onsewa Atha Posachedwapa

Tangoyerekezerani kuti muli m’dziko lopanda mavuto. Kulibe zachiwawa, nkhondo, matenda komanso ngozi zochitika mwadzidzidzi. Muli pa mtendere ndipo simukufunikanso kuda nkhawa ndi zinthu ngati mavuto a za chuma, tsankho kapena kuponderezana. Kodi mukuganiza kuti zimenezi zidzachitikadi? N’zoona kuti palibe munthu kapena bungwe lomwe lingathetse mavuto onse n’kuchititsa kuti padzikoli pakhale mtendere. Koma Mulungu walonjeza kuti adzathetsa zinthu zonse zomwe zimachititsa kuti anthu azikumana ndi mavuto, kuphatikizapo zimene takambirana m’nkhani yapita ija. Taonani ena mwa malonjezo amene ali m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu.

ULAMULIRO WA UFUMU WA MULUNGU

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.

Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe lili kumwamba. Yesu Khristu ndi amene anasankhidwa kuti adzalamulire Ufumu umenewu. Iye adzalowa m’malo mwa maboma onse a anthu ndipo adzaonetsetsa kuti chifuniro cha Mulungu chachitika, osati kumwamba kokha komanso padziko lapansi pano. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu umenewu sudzalowedwa m’malo ndi boma lina la anthu chifukwa ndi “ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.” Zimenezi zikutitsimikizira kuti Ufumuwu ukadzayamba kulamulira tidzakhala pa mtendere mpaka kalekale.—2 Petulo 1:11.

ZIPEMBEDZO ZONYENGA ZIDZATHA

“Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala. Choncho n’zosadabwitsa ngati atumiki ake nawonso amadzisandutsa atumiki a chilungamo. Koma mapeto awo adzakhala monga mwa ntchito zawo.”—2 Akorinto 11:14, 15.

Nthawi idzafika pamene anthu adzazindikira kuti zipembedzo zonse zonyenga zimatsogoleredwa ndi Mdyerekezi ndipo zidzawonongedwa. Sikudzakhalanso tsankho komanso kuphana komwe kumachitika chifukwa cha zipembedzo zonyenga. Zimenezi zidzachititsa kuti anthu onse amene amakonda “Mulungu wamoyo ndi woona” athe kumutumikira ‘m’chikhulupiriro chimodzi’ komanso “motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi.” Pa nthawiyi anthu onse adzakhala ogwirizana komanso azidzakhala mwamtendere.—1 Atesalonika 1:9; Aefeso 4:5; Yohane 4:23.

ANTHU ADZAKHALANSO ANGWIRO

“Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Yehova Mulungu adzathetsa mavuto onse pogwiritsa ntchito Mwana wake Yesu, amene anapereka moyo  wake kuti apulumutse anthu. (Yohane 3:16) Yesu akadzayamba kulamulira padziko lonse lapansi, anthu adzakhalanso angwiro. Sadzakumananso ndi mavuto chifukwa “Mulunguyo adzakhala nawo” ndipo “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.” Zoti anthu anali ochimwa komanso kuti ankakumana ndi mavuto idzakhala mbiri yakale. Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

SIKUDZAKHALANSO MIZIMU YOIPA

“Kenako [Yesu Khristu] anagwira chinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000. Ndipo anamuponyera m’phompho ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu.”—Chivumbulutso 20:2, 3.

Mavuto onse amene amabwera chifukwa cha Satana komanso ziwanda adzatha Satana ndi ziwandazo akadzaponyedwa ‘kuphompho,’ zomwe zikutanthauza kuti sadzatha kuchita chilichonse. Pa nthawiyi iwo sadzalamuliranso zochita za anthu. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala m’dziko popanda kusokonezedwa ndi Satana komanso ziwanda zake.

“MASIKU OTSIRIZA” ADZAKHALA ATATHA

Kumapeto kwa “masiku otsiriza” kudzachitika zimene Yesu anazitchula kuti “chisautso chachikulu.” Iye ananena kuti: “Pa nthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.”—Mateyu 24:21.

Chisautsochi chidzakhala chachikulu chifukwa kudzakhala mavuto ambiri omwe sanachitikepo. Mavuto amenewa adzafika pachimake pa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ yomwe imadziwika kuti “Aramagedo.”—Chivumbulutso 16:14, 16, mawu a m’munsi.

Anthu ambiri amene amakonda zinthu zabwino akuyembekezera mwachidwi kutha kwa dziko loipali. Taonani ena mwa madalitso amene anthu amenewa adzasangalale nawo mu Ufumu wa Mulungu.

MULUNGU ADZATICHITIRA ZABWINO ZAMBIRI

“Khamu lalikulu la anthu” lidzapulumutsidwa kuti likhale m’dziko latsopano lamtendere: Mawu a Mulungu amanena kuti “khamu lalikulu la anthu” limene palibe munthu aliyense amene angathe kuliwerenga ‘lidzatuluka m’chisautso chachikulu’ ndipo adzakhala m’dziko lapansi lolungama. (Chivumbulutso 7:9, 10, 14; 2 Petulo 3:13) Iwo adzaona kuti apulumuka chifukwa cha Yesu Khristu, yemwe ndi “Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko.”—Yohane 1:29.

Anthu adzapindula chifukwa chophunzitsidwa ndi Mulungu: M’dziko latsopano, “dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova.” (Yesaya 11:9) Maphunziro amenewa adzaphatikizapo malangizo a mmene tingadzakhalire mwamtendere ndi anthu a mitundu yonse ndiponso mosawononga chilengedwe. Mulungu walonjeza kuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.”—Yesaya 48:17.

Anzathu komanso abale athu adzaukitsidwa: Yesu ali padziko lapansi anaukitsa Lazaro, yemwe anali mnzake. (Yohane 11:1, 5, 38-44) Pochita zimenezi anasonyeza zimene adzachite Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira.—Yohane 5:28, 29.

Mtendere ndi chilungamo zidzakhalapo mpaka kalekale: Khristu akadzayamba kulamulira sikudzakhalanso zophwanya malamulo. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Chifukwa Yesu amatha kuona zimene zili mumtima mwa munthu ndipo adzagwiritsa ntchito mphamvu yakeyo kuweruza pakati pa olungama ndi oipa. Anthu amene sakufuna kusintha makhalidwe awo oipa sadzaloledwa kukhala m’dziko latsopano la Mulungu.—Salimo 37:9, 10; Yesaya 11:3, 4; 65:20; Mateyu 9:4.

M’nkhani ino tangokambirana ena mwa maulosi opezeka m’Baibulo onena za zinthu zabwino zimene tikuziyembekezera. Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi kudzakhala “mtendere wochuluka” mpaka kalekale. (Salimo 37:11, 29) Mavuto onse omwe anthu akhala akukumana nawo adzatheratu. Ndife otsimikiza kuti zimenezi zidzachitika chifukwa Mulungu anachita kulonjeza kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano. . . . Mawu awa ndi odalirika ndi oona.”—Chivumbulutso 21:5.