Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 YANDIKIRANI MULUNGU

“Mulungu Amakonda Munthu Wopereka Mokondwera”

“Mulungu Amakonda Munthu Wopereka Mokondwera”

Tiyerekeze kuti munthu wina wakupatsani mphatso chifukwa chakuti wachita kukakamizidwa, pomwe wina wakupatsani mphatso chifukwa amakukondani. Kodi mungasangalale ndi mphatso iti? N’zosakayikitsa kuti mukhoza kusangalala ndi munthu amene wakupatsani mphatso chifukwa choti amakukondani. Munthu akamatichitira chinachake, timatha kusangalala kapena kukhumudwa tikadziwa cholinga chimene akuchitira zinthuzo. Ndi mmenenso Mulungu amamvera. Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tikambirane mawu amene mtumwi Paulo analemba pa 2 Akorinto 9:7.

N’chifukwa chiyani Paulo analemba mawu amenewa? Ankafuna kulimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti athandize Akhristu anzawo a ku Yudeya komwe kunali njala. Kodi Paulo ankakakamiza Akhristu a ku Korinto kuti athandize anzawowo? Ayi, chifukwa analemba kuti: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” Tiyeni tione zimene Paulo ankatanthauza.

“Achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake.” Paulo anasonyeza kuti Mkhristu akamapereka mphatso amakhala kuti wasankha “mumtima mwake” kuchita zimenezo. Kuwonjezera pamenepo, Mkhristuyo amaganiziranso zimene okhulupirira anzakewo akufunikira. Munthu wina wolemba mabuku ananena kuti mawu oyambirira amene anawatanthuzira kuti “watsimikizira” amatanthauza kuti “munthuyo amayamba waganizira kaye.” Choncho, Mkhristu amayamba waganizira kaye zimene Akhristu anzake akufunikira kenako amaganizira zimene angachite kuti awathandize.—1 Yohane 3:17.

“Osati monyinyirika kapena mokakamizika.” Paulo ananenanso zinthu ziwiri zimene Akhristu ayenera kupewa, zomwe ndi kunyinyirika komanso kuchita zinthu mokakamizidwa. Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “monyinyirika” amatanthauza “kuchita zinthu mokhumudwa.” Buku lina linanena kuti munthu amene amachita zinthu monyinyirika kapena mokakamizika “amakhala kuti wakhumudwa chifukwa amaganiza kuti kupereka mphatsoyo n’kuwononga ndalama.” Komanso amapereka mphatsoyo chifukwa amaona kuti n’zimene ayenera kuchita, afune asafune. Kodi inuyo mungasangalale munthu atakupatsani mphatso monyinyirika kapena mokakamizika?

“Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” Paulo ananena kuti Mkhristu akasankha kuti apereke mphatso kwa Mkhristu mnzake, ayenera kuchita zimenezo mokondwera kapena kuti mosangalala. Zimenezi n’zoona chifukwa munthu akamapereka mphatso ali ndi zolinga zabwino amakhala wosangalala. (Machitidwe 20:35) Ndipo aliyense amaona kuti munthuyo ndi wosangalala. Mawu akuti “mokondwera” amasonyeza mmene munthuyo akumvera mumtima komanso mmene akuonekera. Zimenezi zimachititsanso kuti munthu wolandira mphatsoyo akhale wosangalala. Mulungunso amasangalala. Baibulo lina linamasulira lembali kuti: “Mulungu amakonda anthu amene amakonda kupereka mphatso.”—Contemporary English Version.

“Mulungu amakonda anthu amene amakondanso kupereka mphatso”

Mawu ouziridwa amene mtumwi Paulo analemba angathandize Akhristu kudziwa zimene ayenera kuchita akafuna kupereka mphatso kwa Akhristu anzawo. Ndiye kaya tikupereka nthawi yathu, mphamvu zathu kapena zinthu zina, tizichita zimenezo mwakufuna kwathu komanso chifukwa chakuti timasangalala kuthandiza ena, makamaka amene akuvutika. Tikamachita zimenezi tidzakhala osangalala komanso tidzakhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu chifukwa “Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”

Mavesi amene mungawerenge mu September

1 Akorinto ndi 2 Akorinto