Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere?

Kodi mukufuna kudziwa zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu komanso zimene udzachite?

Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba. Yesu anauza otsatira ake kuti azipemphera kuti Ufumuwu ubwere, chifukwa ukadzabwera udzachititsa kuti padzikoli pakhale chilungamo komanso mtendere. Palibe boma la anthu limene lingathetseretu chiwawa, kupanda chilungamo kapena matenda. Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetseratu mavuto amenewa. Mulungu anasankha mwana wake, Yesu, kuti akhale Mfumu ya Ufumu umenewu. Mulungu wasankhanso otsatira ena a Yesu kuti adzalamulire naye limodzi.—Werengani Luka 11:2; 22:28-30.

Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu udzawononga onse amene amatsutsa ulamuliro wa Mulungu. Choncho tikamapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere, timakhala tikupempha kuti Ufumuwu udzalowe m’malo mwa maufumu omwe alipowa.—Werengani Danieli 7:13, 14; Chivumbulutso 11:15, 18.

N’chifukwa chiyani tingati Ufumu wa Mulungu ndi wabwino kwambiri?

Yesu ndi Mfumu yabwino kwambiri chifukwa ndi wachifundo. Popeza ndi Mwana wa Mulungu, iye ali ndi mphamvu zothandiza anthu onse amene amapempha Mulungu kuti awathandize.—Werengani Salimo 72:8, 12-14.

Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu onse amene amafunadi kuti Ufumuwu ubwere komanso amene amayesetsa kuchita zimene Mulungu amafuna. Mungapindule kwambiri ngati mutaphunzira zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu.—Werengani Luka 18:16, 17; Yohane 4:23.