Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI UFUMU WA MULUNGU UDZAKUCHITIRANI CHIYANI?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzakuchitirani Chiyani?

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzakuchitirani Chiyani?

Monga taonera m’nkhani zapitazi, a Mboni za Yehova amaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri. N’kutheka kuti mwachita chidwi ndi zinthu zabwino zimene Ufumu wa Mulungu udzachite, zomwe zanenedwa m’nkhani zimenezi. Koma mwina mukukayikira ngati zimenezi zidzachitikedi.

Zimenezi n’zomveka, chifukwa si bwino kumangokhulupirira chilichonse. (Miyambo 14:15) Ndipotu Baibulo limanena za anthu ena a ku Bereya * amene sankangokhulupirira chilichonse. Atauzidwa uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, anthuwa sanafulumire kungokhulupirira zimene anamvazo. Iwo anafufuza kaye mosamala m’Malemba “kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona.” (Machitidwe 17:11) Kunena kwina tingati, anthu a ku Bereya ankayerekeza zimene amva ndi zimene Malemba amanena. Ataona kuti zimene anamvazo n’zoona, anayamba kukhulupirira kuti uthenga wabwino unalidi wochokera m’Mawu a Mulungu.

Tikukulimbikitsani kuti nanunso muchite zofanana ndi zimenezi. A Mboni za Yehova amaphunzira ndi anthu Baibulo kwaulere ndipo zimenezi zimathandiza anthuwo kuti aone ngati zimene a Mboni amakhulupirira zokhudza Ufumu, zilidi zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

Kuwonjezera pa kudziwa zokhudza Ufumu wa Mulungu, kuphunzira Baibulo kungakuthandizeninso kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri awa:

Komanso kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni ‘kuyandikira Mulungu’ kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi. (Yakobo 4:8) Ubwenzi wanu ndi Yehova ukamalimba, mumayamba kudziwa kuti pali zambiri zimene Ufumu wa Mulungu ungakuchitireni panopa komanso m’tsogolo. Yesu anauza Atate wake m’pemphero kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”—Yohane 17:3.

 

^ ndime 4 Bereya unali mzinda wa ku Makedoniya wakale.