Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUMVETSA ZIMENE BAIBULO LIMANENA?

Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena

Mukhoza Kumvetsa Zimene Baibulo Limanena

Tiyerekeze kuti mwapita kudziko lachilendo. Muli kumeneko, mukuona kuti anthu ake ndi osiyana kwambiri ndi a kwanu. Zakudya zimene amakonda, chikhalidwe chawo komanso ndalama zimene amagwiritsa ntchito, n’zosiyana kwambiri ndi zimene munazolowera. N’zosakayikitsa kuti zingakuvuteni kuzolowera kukhala m’dziko limenelo. Ndipo sitikukayikira kuti mungakonde kuti munthu wina azikuthandizani.

Nanunso mukhoza kumva chimodzimodzi ngati n’koyamba kuwerenga Baibulo. Zimenezi zikhoza kuchitika chifukwa Baibulo limafotokoza zinthu zimene zinachitika kale kwambiri, zomwenso mwina zingakhale zosiyana ndi zimene zimachitika kwanuko. Mwachitsanzo Baibulo limanena za anthu ena otchedwa Afilisiti, chakudya chotchedwa mana, ndalama zotchedwa madalakima komanso chikhalidwe chachilendo ‘chong’amba zovala’ munthu akakhumudwa ndi zinazake. (Yoswa 13:2; Ekisodo 16:31; Luka 15:9; 2 Samueli 3:31) Monga taonera m’chitsanzo chija, munthu ukapita ku dziko lachilendo umafuna kuti wina azikuthandiza. Ndiye kodi simungakonde kuti munthu wina yemwe amadziwa bwino Baibulo akuthandizeni kumvetsa zimene limanena?

ANTHU AKALE ANKATHANDIZIDWA KUMVETSA MALEMBA

Kungochokera pamene Malemba Opatulika anayamba kulembedwa mu 1513 B.C.E., Mulungu wakhala akuthandiza anthu kumvetsa bwino Malemba. Mwachitsanzo, Mose yemwe ankatsogolera mtundu wa Isiraeli ‘anayamba kufotokozera’ anthu zimene zinalembedwa.—Deuteronomo 1:5.

Kungochokera nthawi imeneyo, Aisiraeli ankakhala ndi anthu oyenerera amene ankawaphunzitsa Malemba. Mwachitsanzo mu 455 B.C.E. gulu la Ayuda, kuphatikizaponso ana, linasonkhanitsidwa pabwalo lina mumzinda wa Yerusalemu. Ndiyeno aphunzitsi a Mawu a Mulungu anayamba “kuwerenga bukulo [Malemba Opatulika aja] mokweza.” Koma si kuti ankangowawerengera, basi n’kusiya. ‘Ankawathandizanso kumvetsa tanthauzo la zimene anali kuwerengazo.’—Nehemiya 8:1-8.

Patapita zaka zambiri, Yesu ankathandiza anthu kumvetsa Mawu a Mulungu ndipo anthu ankamutchula kuti mphunzitsi. (Yohane 13:13) Nthawi zina Yesu ankaphunzitsa anthu monga gulu, koma nthawi zina ankaphunzitsa munthu payekhapayekha. Pa nthawi ina, Yesu anaphunzitsa khamu la anthu pa ulaliki wina womwe unachitikira paphiri. Anthuwo atamva zimene Yesu ananena ‘anakhudzidwa moti anadabwa ndi kaphunzitsidwe kake.’ (Mateyu 5:1, 2; 7:28) Ndiponso m’chaka cha 33 C.E., ophunzira awiri a Yesu ankapita kumudzi wina womwe unali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu. Kenako Yesu anawapeza n’kuyamba ‘kuwafotokozera Malemba momveka bwino.’—Luka 24:13-15, 27, 32.

Nawonso ophunzira a Yesu ankaphunzitsa ena Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, pa nthawi inayake nduna ya ku Itiyopiya inkawerenga mbali ina ya Malemba Opatulika. Kenako wophunzira wa Yesu, dzina lake Filipo, anafika kwa ndunayi n’kuifunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” Ndunayo inayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Ndiye Filipo anaifotokozera tanthauzo la zimene inali kuwerengazo.—Machitidwe 8:27-35.

NANUNSO MUKHOZA KULIMVETSA BAIBULO

Mofanana ndi anthu akale omwe ankaphunzitsa ena mfundo za m’Malemba, a Mboni za Yehova masiku ano amaphunzitsa anthu Baibulo m’mayiko 239. (Mateyu 28:19, 20) Mlungu uliwonse, amaphunzira Baibulo ndi anthu oposa 9 miliyoni. Ambiri mwa anthuwa amakhala oti si Akhristu. A Mboniwa samalipiritsa kalikonse akamaphunzira Baibulo ndi munthu ndipo amachita zimenezi kunyumba kapena malo ena amene munthu angasankhe kuti aziphunzirirako. Phunziroli limathanso kuchitika munthu ali kwina. Mwachitsanzo, ena amaphunzira kudzera pa foni, kompyuta kapena pa tabuleti.

Kodi nanunso mukufuna kumvetsa zimene Baibulo limanena? Tikukupemphani kuti mufunse wa Mboni za Yehova aliyense kuti akuthandizeni. Ngati mutaphunzira Baibulo ndi a Mboni, mudzaona kuti Baibulo ndi buku ‘lopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’chilungamo.’ Ndi lothandizanso “kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira kuchita ntchito iliyonse yabwino.”—2 Timoteyo 3:16, 17.