Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

Kunja Kukutentha Modetsa Nkhawa—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kunja Kukutentha Modetsa Nkhawa—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 M’mwezi wa July 2022, manyuzipepala ambiri analemba malipoti otsatirawa onena za kutentha koopsa komwe kukuchitika:

  •    “Kwa maulendo awiri m’mwezi uno wokha, akuluakulu a boma la China achenjeza anthu kuti m’mizinda pafupifupi 70 mukhala nyengo yotentha koopsa.”​—July 25, 2022, CNN Wire Service.

  •    “M’mayiko ambiri ku Europe, kukuyambika moto wam’nkhalango chifukwa cha nyengo yotentha kwambiri.”​—July 17, 2022, The Guardian.

  •    “Lamlungu lapitali, m’mizinda yambiri ku United States kunatentha koopsa zomwe zinali zachilendo kwambiri. Kutenthaku kunakhudza madera a ku East Coast komanso mbali zina za ku South komanso Midwest.”​—July 24, 2022, The New York Times.

 Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kodi nthawi ina padzikoli sipadzapezekanso chamoyo chilichonse? Nanga Baibulo limanena zotani?

Kodi Kutenthaku kukukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo?

 Inde. Kutentha koopsa komwe kukuchitika padziko lonse kukugwirizana ndi zomwe Baibulo linaneneratu zokhudza masiku athu ano. Mwachitsanzo, Yesu ananeneratu kuti tidzaona “zoopsa.” (Luka 21:11) Kutentha komwe kukuchitika padzikoli chifukwa cha zochita za anthu, kukupangitsa kuti anthu ambiri azida nkhawa kuti nthawi ina padzikoli sipasadzapezekanso chamoyo chilichonse.

Kodi nthawi ina padzikoli sipadzapezekanso chamoyo chilichonse?

 Ayi. Mulungu analenga dziko lapansili kuti anthu azikhalapo mpaka kalekale. (Salimo 115:16; Mlaliki 1:4) Mulungu sadzalola kuti anthu apitirize kuwononga dzikoli. Koma iye analonjeza kuti, ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’​—Chivumbulutso 11:18.

 Tiyeni tikambirane maulosi awiri awa omwe akusonyeza zinthu zinanso zomwe Mulungu analonjeza:

  •    “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi” (Yesaya 35:1) Mulungu sadzalola kuti dzikoli lidzawonongeke n’kukhala lopanda zamoyo. Koma iye adzakonzanso malo onse omwe anawonongeka.

  •    “Mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka.” (Salimo 65:9) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu adzasandutsa dziko lapansili kuti likhale paradaiso.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene kusintha kwa nyengo kukukwaniritsira maulosi a m’Baibulo, werengani nkhani yakuti, “Zomwe Baibulo Limanena pa Nkhani Yakusintha Kwa Nyengo Komanso Tsogolo Lathu.”

 Kuti mudziwe zambiri zomwe Baibulo limalonjeza pa nkhani yobwezeretsa chilengedwe, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?