Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 128

Tipirire Mpaka Mapeto

Tipirire Mpaka Mapeto

(Mateyu 24:13)

  1. 1. Mawu a Mulungu wathu

    Amalimbikitsa.

    Zinthu zomwe waphunzira

    Zonse ndi zolondola.

    Uzikhulupirikabe

    Podikira mapeto.

    Usaope mayesero

    Udzakhala wolimba.

  2. 2. Chikondi chako kwa M’lungu

    Chisachepe mphamvu.

    Upirirebe ngakhale

    Mayesero akule.

    Kaya akhale otani

    Usamachite mantha.

    Yehova Mulungu wako

    Adzakupulumutsa.

  3. 3. Yemwe angapirirebe

    Adzapulumuka.

    Mayina akulembedwa

    Mubuku la moyo.

    Lola kuti kupirira

    Kugwire ntchito yake.

    Yehova adzachititsa

    Kuti usangalale.