Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 84

Tizilalikira Modzipereka

Tizilalikira Modzipereka

(Mateyu 9:​37, 38)

  1. 1. M’lungu wathu watipatsa

    Zomwe timafunikira

    Kuti tizisangalala

    Pomwe tikulalikira.

    (KOLASI)

    Tigwire ntchitoyi

    Modzipereka

    Ndipo kulikonse tipita

    Mofunitsitsa.

  2. 2. Padzikoli pali ntchito.

    Kosowa tidzapitako

    Tikatero tisonyeza

    Kuti timakonda anthu.

    (KOLASI)

    Tigwire ntchitoyi

    Modzipereka

    Ndipo kulikonse tipita

    Mofunitsitsa.

  3. 3. Kwathu kuno kuli ntchito.

    Tikuphunzira maluso.

    Taphunzira zinenero

    Ndipo tikulalikira.

    (KOLASI)

    Tigwire ntchitoyi

    Modzipereka

    Ndipo kulikonse tipita

    Mofunitsitsa.