Pitani ku nkhani yake

AUGUST 16, 2019
DENMARK

A Mboni za Yehova Atsegula Malo Atsopano Osungirako Mabaibulo Akale ku Denmark

A Mboni za Yehova Atsegula Malo Atsopano Osungirako Mabaibulo Akale ku Denmark

Mu July 2019, malo osungirako Mabaibulo akale anatsegulidwa pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya Scandinavia, yomwe ili m’tawuni ya Holbæk ku Denmark. Ofesi ya nthambiyi ili pamtunda wa makilomita pafupifupi 65 kuchokera mumzinda wa Copenhagen. Mutu wofotokoza za malowa ndi wakuti “Dzina la Mulungu M’Mabaibulo a ku Scandinavia.”

Ku malo osungira Mabaibulo akalewa kuli Mabaibulo ambiri omwe sapezekapezeka komanso ofunika a zinenero za Chidanishi, Chifaeroe, Chigirinilandi, Chiayisilandi, Chinorowe, Chisaami, ndi Chiswidishi. Ku malowa kuli Mabaibulo oposa 50.

Limodzi mwa Mabaibulo ofunika ndi Baibulo lakuti Gustav Vasa Bible lomwe linapangidwa mu 1541. Linali Baibulo loyamba lathunthu kupezeka m’zinenero zonse za ku Scandinavia. Galamala komanso mawu ambiri a chinenero cha Chiswidishi anachokera m’Baibulo la Gustav Vasa Bible. Baibulo la Gustav Vasa Bible ndi lomwe linkagwiritsidwa ntchito kwambiri pomasulira Mabaibulo ena a Chiswidishi kwa zaka 300.

Baibulo la Gustav Vasa Bible lomwe linapangidwa mu 1541 likusonyezedwa ku malo osungira Mabaibulo akalewa

Baibulo linanso lomwe lili ku malowa limene silipezekapezeka ndi la Christian III Bible lomwe linapangidwa mu 1550. Limeneli linali Baibulo lathunthu loyamba la Chidanishi. Baibuloli linathandiza popanga malamulo a chinenero cha Chidanishi, komanso linathandiza kwambiri m’madera ambiri a kumpoto kwa Europe.

Baibulo la Christian III Bible lomwe linapangidwa mu 1550

A Erik Jørgensen a ku ofesi ya nthambi ya Scandinavia anati: “Malo osungirako Mabaibulo akalewa akusonyeza mmene anthu a ku Scandinavia akhala akulemekezera kwambiri Mawu a Mulungu komanso dzina lake lalikulu lakuti Yehova kwa zaka mahandiredi ambiri.”