Pitani ku nkhani yake

Kodi Kukhala Woyera Kumatanthauza Chiyani?

Kodi Kukhala Woyera Kumatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Kukhala woyera kumatanthauza kupewa chodetsa chilichonse. Mawu a Chiheberi omwe anawamasulira kuti “kuyera” anachokera ku mawu otanthauza “kupatula.” Choncho chinthu chomwe ndi choyera chimapatulidwa kuti chizigwiritsidwa ntchito pa zinthu zapadera zokha.

 Mulungu ndi woyera kuposa wina aliyense komanso chilichonse. Baibulo limati: “Palibe woyera ngati Yehova.” a (1 Samueli 2:2) Choncho Mulungu ndiye woyenera kutiikira mfundo zoyenera kutsatira pa nkhani ya zinthu zofunika kuziona kukhala zoyera.

 Mawu akuti “woyera” amagwiritsidwa ntchito pa chilichonse chokhudzana ndi kulambira Mulungu. Mwachitsanzo Baibulo limanena za zinthu monga:

  •   Malo oyera: Mose ali pafupi ndi chitsamba choyaka moto, Mulungu anamuuza kuti: “Malo waimawo ndi malo oyera.”—Ekisodo 3:2-5.

  •   Misonkhano yopatulika: Nthawi zambiri Aisiraeli ankalambira Yehova pa nthawi ya zikondwerero zomwe zinkadziwika ndi dzina loti “misonkhano yopatulika.”—Levitiko 23:37.

  •   Ziwiya zopatulika: Zinthu zomwe zinkagwiritsidwa ntchito polambira Yehova pa kachisi wa ku Yerusalemu zinkatchulidwa kuti “ziwiya . . . zopatulika.” (1 Mafumu 8:4) Ngakhale kuti Aisiraeli ankaona ziwiyazi kukhala zapadera kwambiri, sankafunika kuzilambira. b

Kodi n’zotheka kuti anthu ochimwafe tikhale oyera?

 Inde. Mulungu analamula Akhristu kuti: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.” (1 Petulo 1:16) Ndi zoona kuti anthu ochimwa sangathe kukhala oyera ngati mmene Mulungu alili. Komabe anthu omwe amamvera malamulo olungama a Mulungu, amaonedwa kuti ndi ‘oyera ndi ovomerezeka kwa Mulungu.’ (Aroma 12:1) Ndipo munthu amakhala woyera chifukwa cha zomwe amalankhula ndi kuchita. Mwachitsanzo, amatsatira malangizo a m’baibulo akuti “mukhale oyera mwa kupewa dama” komanso akuti “khalani oyera m’makhalidwe anu onse.”​—1 Atesalonika 4:3; 1 Petulo 1:15.

Kodi zingatheke kuti munthu amene poyamba anali woyera, Mulungu asiye kumukonda?

 Inde. Ngati munthu satsatira mfundo za makhalidwe abwino, Mulungu amasiya kumuona kuti ndi woyera. Mwachitsanzo, buku la Aheberi lili ndi malangizo opita kwa “abale . . . oyera.” Komabe limachenjezanso abalewa kuti “wina asachoke kwa Mulungu wamoyo n’kukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.”​—Aheberi 3:1, 12.

Maganizo olakwika pa nkhani ya kukhala woyera

 Maganizo olakwika: Munthu akhoza kukhala woyera ngati atamadzimana zinthu zabwino.

 Zoona zake: Baibulo limanena kuti ‘kuzunza thupi,’ kapena kudzikana, ‘n’kosathandiza’ kwa Mulungu. (Akolose 2:23) Ndipotu Mulungu amafuna kuti tizisangalala ndi zinthu zabwino. N’chifukwa chake amanena kuti “munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.”​—Mlaliki 3:13.

 Maganizo olakwika: Munthu akasankha kuti asakhale pabanja amakhala woyera.

 Zoona zake: Ngakhale kuti Mkhristu akhoza kusankha kuti asakhale pabanja, kuchita zimenezi sikungamupangitse kukhala woyera kwa Mulungu. N’zoona kuti munthu amene sali pabanja sasokonezeka kwambiri akamatumikira Mulungu. (1 Akorinto 7:32-34) Koma Baibulo limasonyeza kuti ngakhale anthu omwe ali pabanja akhoza kukhala oyera. Ndipotu Petulo yemwe anali mmodzi wa ophunzira a Yesu anali wokwatira.​—Mateyu 8:14; 1 Akorinto 9:5.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. Mabaibulo ambiri amaphatikiza dzina la Mulunguli ndi mawu akuti “woyera” kapena “wopatulika.”

b Baibulo limaletsa kupembedza ziwiya zakalezi zomwe zinkagwiritsidwa ntchito polambira Mulungu. 1 Akorinto 10:14.