Pitani ku nkhani yake

N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?

N’chiyani Chingakuthandizeni Kumvetsa Baibulo?

Yankho la m’Baibulo

 M’Baibulo muli mfundo zotithandiza kuti tilimvetse. Kaya ndife anthu otani, uthenga wa Mulungu umene uli m’Baibulo ‘si wovuta kutsatira, ndipo si wapatali.’—Deuteronomo 30:11.

Mfundo zimene zingakuthandizeni kumvetsa Baibulo

  1.   Muzikhala ndi maganizo oyenera. Muziona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu. Muzikhala ndi mtima wodzichepetsa popeza Mulungu amatsutsa odzikweza. (1 Atesalonika 2:13; Yakobo 4:6) Koma musamangokhulupirira zinthu popanda umboni chifukwa Mulungu amafuna kuti muzigwiritsa ntchito “luntha la kuganiza.”—Aroma 12:1, 2.

  2.   Muzipempha nzeru. Pa Miyambo 3:5, Baibulo limati: “Usadalire luso lako lomvetsa zinthu.” M’malomwake, ‘tizipempha kwa Mulungu’ kuti atipatse nzeru zotithandiza kumvetsa Baibulo.—Yakobo 1:5.

  3.   Muziphunzira nthawi zonse. Kuphunzira Baibulo kungakuthandizeni kwambiri ngati mumaliphunzira nthawi zonse osati modumphadumpha.—Yoswa 1:8.

  4.   Muziphunzira mwadongosolo. Njira yabwino kwambiri yophunzirira Baibulo n’kufufuza zimene Malemba amanena pa nkhani inayake. Muziyamba ndi nkhani zosavuta kenako n’kufufuza nkhani zovutirapo. (Aheberi 6:1, 2) Mukamayerekezera lemba lina ndi linzake mudzaona kuti Baibulo limafotokoza lokha zinthu, ngakhale “zinthu zina zovuta kuzimvetsa.”—2 Petulo 3:16.

  5.   Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipempha anthu ena kutithandiza kumvetsa Baibulo. (Machitidwe 8:30, 31) A Mboni za Yehova amaphunzitsa anthu Baibulo mwaulere. Mofanana ndi zimene Akhristu oyambirira ankachita, iwo amagwiritsa ntchito malemba pothandiza anthu kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsa kwenikweni.Machitidwe 17:2, 3.

Zinthu zimene si zofunika

  1.   Nzeru kapena maphunziro apamwamba. Atumwi 12 a Yesu ankamvetsa Malemba ndiponso kuwaphunzitsa ngakhale kuti anthu ena ankawaona kuti ndi “osaphunzira ndiponso anthu wamba.”—Machitidwe 4:13.

  2.   Ndalama. Mukhoza kuphunzira Baibulo popanda kulipira chilichonse. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.”—Mateyu 10:8.