Pitani ku nkhani yake

Kodi Tchimo Loyambirira Linali Chiyani?

Kodi Tchimo Loyambirira Linali Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Adamu ndi Hava anali anthu oyambirira kuchimwa. Iwo sanamvere Mulungu ndipo anadya “zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.” Anthu ambiri amanena kuti limeneli ndi limene linali tchimo loyambirira. a (Genesis 2:16, 17; 3:6; Aroma 5:19) Adamu ndi Hava sankayenera kudya zipatso za mtengowo chifukwa unkaimira mphamvu zimene Mulungu ali nazo, zopatsa anthu ufulu wosankha zabwino kapena zoipa. Choncho iwo atadya zipatsozo, anasonyeza kuti adzipatsa okha ufulu wosankha zabwino ndi zoipa ndipo akukana kuti Mulungu aziwalamulira.

 Kodi “tchimo loyambirira” linakhudza bwanji Adamu ndi Hava?

 Popeza kuti Adamu ndi Hava anachimwa, iwo anakalamba ndipo kenako anafa. Anawononga ubwenzi wawo ndi Mulungu ndiponso anataya mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha.—Genesis 3:19.

 Kodi “tchimo loyambirira” limatikhudza bwanji?

 Adamu ndi Hava anapatsira ana awo onse uchimo. Zimenezi n’zofanana ndi zomwe zimachitika ndi makolo omwe apatsira ana awo matenda. (Aroma 5:12) N’chifukwa chake tonse timabadwa tili ‘ochimwa,’ b kutanthauza kuti ndife opanda ungwiro ndipo timalakwitsa zinthu.—Salimo 51:5; Aefeso 2:3.

 Popeza kuti tinatengera uchimo kapena kuti kupanda ungwiro, timadwala, timakalamba ndipo timafa. (Aroma 6:23) Komanso timavutika ndi zotsatirapo za zomwe ifeyo kapena anthu ena asankha.—Mlaliki 8:9; Yakobo 3:2.

 Kodi n’zotheka kukhala popanda mavuto omwe amabwera chifukwa cha tchimo loyambirira?

 Inde. Baibulo limanena kuti Yesu anafa “monga nsembe yophimba machimo athu.” (1 Yohane 4:10) Nsembe ya Yesu ingatipumulutse ku zotsatirapo za uchimo womwe tinatengera ndipo ingatithandize kudzapeza mwayi wokhala ndi moyo wosatha, womwe Adamu ndi Hava anataya.—Yohane 3:16. c

 Maganizo olakwika okhudza “tchimo loyambirira”

 Maganizo olakwika: Tchimo loyambirira linachititsa kuti zikhale zovuta kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu.

 Zoona zake: Mulungu samatiimba mlandu chifukwa cha zimene Adamu ndi Hava anachita. Amadziwa kuti ndife anthu opanda ungwiro ndipo sayembekezera kuti tichite zinthu zimene sitingakwanitse. (Salimo 103:14) Ngakhale kuti timavutika chifukwa cha zotsatirapo za uchimo omwe tinatengera, tili ndi mwayi wokhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu.—Miyambo 3:32.

 Maganizo olakwika: Ubatizo ndi umene umachotsa uchimo, choncho ana akhanda ayenera kubatizidwa.

 Zoona zake: Sikuti timangofunika kubatizidwa kokha kuti tidzapulumuke, timafunikanso kukhulupirira nsembe ya Yesu kuti machimo athu ayeretsedwe. (1 Petulo 3:21; 1 Yohane 1:7) Popeza kuti chikhulupiriro chimabwera kuchokera pa zimene munthu waziphunzira, n’zosatheka kuti ana akhanda akhale ndi chikhulupiriro. Choncho Baibulo silimanena kuti ana akhanda azibatizidwa. Ndipo nawonso Akhristu oyambirira sankabatiza ana akhanda, koma “amuna ndi akazi” omwe akhulupirira Mawu a Mulungu.—Machitidwe 2:41; 8:12.

Maganizo olakwika: Mulungu anatemberera akazi chifukwa Hava ndi amene anayambirira kudya chipatso choletsedwa.

 Zoona zake: M’malo motemberera akazi, Mulungu anatemberera “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana,” amene ananyengerera Hava kuti achimwe. (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:14) Komanso Mulungu ananena kuti amene ali ndi mlandu pa tchimo loyambirira ndi Adamu, osati mkazi wake.—Aroma 5:12.

 N’chifukwa chani Mulungu ananena kuti Adamu adzalamulira mkazi wake? (Genesis 3:16) Apa sikuti Mulungu ankafuna kuti amuna azipondereza akazi awo. Koma anangoneneratu zotsatirapo za uchimo. Mulungu amafuna kuti mwamuna azikonda komanso kulemekeza mkazi wake, tingoti azilemekeza akazi onse.—Aefeso 5:25; 1 Petulo 3:7.

 Maganizo olakwika: Tchimo loyambirira linali kugonana.

 Zoona zake: Tchimo loyambirira silinali kugonana pa zifukwa izi:

  •   Pamene Mulungu ankauza Adamu kuti asadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa, n’kuti Adamuyo alibe mkazi.—Genesis 2:17, 18.

  •   Mulungu anauza Adamu ndi Hava kuti “muberekane, muchuluke” zomwe zikutanthauza kuti ankafunika kukhala ndi ana. (Genesis 1:28) Choncho zikanakhala nkhanza ngati Mulungu akanalanga banjali chifukwa choti lachita zinthu zomwe analilamula.

  •   Adamu ndi Hava anachimwa pa nthawi zosiyana, anayamba ndi Hava ndipo kenako Adamu.—Genesis 3:6.

  •   Baibulo limavomereza kugonana kwa pakati pa mwamuna ndi mkazi wake.—Miyambo 5:18, 19; 1 Akorinto 7:3.

a M’Baibulo mulibemo mawu akuti “tchimo loyambirira.” Ndipo tchimo loyamba kutchulidwa m’Baibulo ndi zomwe Satana ananena ponamiza Hava.—Genesis 3:4, 5; Yohane 8:44.

b M’Baibulo, mawu akuti “tchimo” samangotanthauza kuchita zinthu zolakwika. Koma amanenanso za kupanda ungwiro komwe tinatengera kwa makolo athu.

c Kuti mudziwe zambiri zokhudza nsembe ya Yesu komanso mmene ingatithandizire, werengani nkhani yakuti “Kodi Yesu Amatipulumutsa Bwanji?