Pitani ku nkhani yake

Mavidiyo Othandiza Kumvetsa Mfundo Zofunika za M’baibulo

Kodi Zinthu Zakumwamba ndi Padziko Lapansi Zinachita Kulengedwa?

Anthu ambiri samvetsa bwinobwino zimene Baibulo limanena zokhudza chilengedwe kapenanso amaganiza kuti ndi zongopeka. Kodi zimene Baibulo limanena zokhudza mmene chilengedwe chinayambira ndi zomveka?

Kodi Mulungu Ndi Weniweni?

Onani umboni wosonyeza kuti chikhulupiriro chakuti Mulungu alipo ndi chomveka.

Kodi Mulungu Ali Ndi Dzina?

Mulungu ali ndi maina ambiri audindo monga akuti Atate, Mlengi ndi Ambuye. Koma Dzina lake lenileni limapezeka m’Baibulo malo oposa 7000.

Kodi N’zotheka Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu?

Kwa zaka zambiri anthu akhala akufuna kudziwa amene anawalenga. Baibulo lingatithandize kuti tikhale mnzake wa Mulungu. Ubwenzi umenewu umayamba tikadziwa dzina la Mulungu.

Kodi Analemba Baibulo Ndi Ndani?

Ngati Baibulo linalembedwa ndi anthu, kodi n’zomveka kunena kuti ndi Mawu a Mulungu? Kodi m’Baibulo muli mawu a ndani?

Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Baibulo Limanena Zoona?

Ngati Baibulo linachokeradi kwa Mulungu, ndiye kuti liyenera kukhala losiyana kwambiri ndi mabuku ena onse.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

Padziko lapansili pali zinthu zambiri zokongola. Mulungu anaika dzikoli pamalo abwino kwambiri kuchokera pamene pali dzuwa ndipo limazungulira pa liwiro labwino. N’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansili mwanjira imeneyi?

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

Baibulo limanena kuti kutsogoloku anthu ambiri adzaukitsidwa ngati mmene zinakhalira ndi Lazaro.

Kodi Mulungu Amaotcha Anthu Kumoto?

Baibulo limatiuza kuti “Mulungu ndiye chikondi,” choncho sangazunze anthu chifukwa cha machimo amene anawachita kalekale.

Kodi Yesu Khristu Ndi Mulungu?

Kodi Yesu Khristu ndi Mulungu Wamphamvuyonse? Kapena ndi wosiyana ndi Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Yesu Anafa?

Baibulo limasonyeza kuti imfa ya Yesu ndi yofunika kwambiri. Kodi imfa ya Yesu ili ndi phindu lililonse?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

Ali padziko lapansi, Yesu anafotokoza kwambiri za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse. Kwa zaka zambiri otsatira ake akhala akupempherera Ufumu umenewu kuti ubwere.

Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulira mu 1914

Zaka zoposa 2,500 zapitazo, Mulungu anapatsa mfumu yamphamvu loto lonena za ulosi umene ukukwaniritsidwa panopa.

Zinthu Padzikoli Zinasintha Kuyambira mu 1914

Makhalidwe komanso zochitika zam’dzikoli zimene zakhala zikuchitika kuyambira mu 1914 zimasonyeza kuti maulosi a m’Baibulo okhudza ‘masiku otsiriza’ akukwaniritsidwa.

Kodi Mulungu Ndi Amene Amachititsa Ngozi Zam’chilengedwe?

Anthu awiri omwe anakhudzidwapo ndi ngozi zam’chilengedwe akufotokoza zimene anaphunzira m’Baibulo.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika?

Anthu ambiri amafuna kudziwa kuti n’chifukwa chiyani padzikoli pali mavuto ambiri. Baibulo limapereka yankho logwira mtima pa nkhaniyi.

Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?

Anthu amaganiza kuti palibe vuto ngati munthu atalowa m’chipembedzo chilichonse.

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Anthu Azigwiritsa Ntchito Zizindikiro Pomulambira?

Kodi zingatithandize kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu yemwe sitingamuone?

Kodi Mulungu Amamvetsera Mapemphero Onse?

Nanga bwanji ngati munthu akupempha zinthu zinazake chifukwa cha dyera? Bwanji ngati mwamuna atamenya mkazi wake, kenako n’kumapempha Mulungu kuti amudalitse?

Mmene Mulungu Amaonera Banja

Mulungu amafuna kuti banja lanu liziyenda bwino. Malangizo abwino a m’Baibulo athandiza mabanja ambiri.

Kodi Kuonera Zolaula Ndi Tchimo?

Kodi mawu akuti “zolaula” amapezeka m’Baibulo? Kodi tingadziwe bwanji mmene Mulungu amaonera nkhani yoonera zolaula?