Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mumasangalala Mukamayambitsa Nkhani

Mumasangalala Mukamayambitsa Nkhani

Kucheza ndi imodzi mwa njira zosangalatsa komanso zothandiza kwambiri zomwe tingagwiritse ntchito kuti tilalikire. Komabe, tikhoza kuchita mantha kuti tiyambitse nkhani ngati timangoganizira kwambiri za mmene tingayambire kukambirana nkhani ya m’Baibulo. M’malo momaganizira kwambiri za mmene mungalalikirire, muzimusonyeza chidwi munthuyo. (Mt 22:39; Afi 2:4) Ngati pamene mukucheza mwayi wapezeka woti mufotokoze za chikhulupiriro chanu, pali zinthu zambiri zomwe zingakuthandizeni.

Kodi zinthu zotsatirazi zingakuthandizeni bwanji kulalikira zokhudza nkhani imene yangobwera pamene mukucheza?

ONERANI VIDIYO YAKUTI “CHITSULO CHIMANOLA CHITSULO CHINZAKE”​—MMENE MUNGAYAMBIRE KUCHEZA NDI ANTHU, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

Kodi ndi mfundo zitatu ziti zimene zingatithandize kuwonjezera luso lathu loyamba kucheza ndi anthu?