Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Miyambi ya Aakani Imasonyeza Chikhalidwe Chawo

Miyambi ya Aakani Imasonyeza Chikhalidwe Chawo

Miyambi ya Aakani Imasonyeza Chikhalidwe Chawo

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU GHANA

KODI mwambi n’chiyani? Buku lina lotanthauzira mawu limati mwambi ndi “mawu okhala ndi langizo kapena ofotokoza mfundo zina zofunika pamoyo amene anthu amawatchula kaŵirikaŵiri.” Ayoruba ku Nigeria ali ndi tanthauzo lochititsa chidwi kwambiri la mwambi chifukwa amati, mwambi ndi “kavalo amene angakam’fikitse munthu mofulumira kumene kumapezeka nzeru.”

Kufunika kwa miyambi kumafotokozedwa m’mwambi wina wotchuka pakati pa anthu a ku Ghana a mtundu wa Chiakani, wakuti: “Wanzeru umam’yankhula m’miyambi, osati m’mawu wamba.” Mfundo apa njakuti munthu wanzeru safunika kuchita kumulongosolera chinkhani kuti amvetse ubwino wa chinachake. Mwambi woyenerera umapangitsa munthu kuganiza, umam’patsa nzeru, ndipo ungam’limbikitse kuchita zinthu zoyenerera.

M’dziko la Ghana, miyambi amaigwiritsira ntchito kwambiri pa ukwati ndiponso pa maliro ndipo amaitchula m’nyimbo zosiyanasiyana za chikhalidwe chawo. Komanso amaigwiritsira ntchito kwambiri pa zokambirana za magulu osiyanasiyana. Nthaŵi zambiri pokambirana, nthumwi ya gulu linalake imangoyamba kupha miyambi inayake koma mwaluso kwambiri.

Aakani amaona kuti munthu ndi wanzeru akamagwiritsira ntchito miyambi mwaluso. N’zochititsa chidwi kuti m’Baibulo, Mfumu Solomo, yomwe inatchuka ndi nzeru, kudziŵa zambiri, ndiponso luso lake pokambirana ndi anthu, akuti inkadziŵa miyambi yokwana 3,000. Inde, miyambi ya m’Baibulo inauziridwa ndi Mulungu komanso ndi yoona nthaŵi zonse, ndipo njosiyana ndi miyambi imene anthu amanena kuchokera pa zimene aona ndiponso nzeru zawo. Miyambi ya anthu, ngakhale ikhale ya nzeru chotani, sitiyenera kuifananitsa ndi miyambi ya m’Baibulo. Komabe tatiyeni tione miyambi ina ya Chiakani.

Yokhudza Mulungu

Ku Ghana, miyambi yambiri imagwirizana ndi zoti kuli Mulungu, ndipo miyambi yambiri ya Chiakani imasonyeza mfundo imeneyi. Pachikhalidwe cha Aakani, anthu saganizako n’komwe zoti kulibe Mulungu. Mwachitsanzo, mwambi wina umati: “Mwana salira kuchita kum’lozera Mulungu.” Zoti kuli Mulungu n’zodziŵikiratu ngakhale kwa mwana wamng’ono. Mwambiwu amaugwiritsira ntchito nthaŵi zambiri pofotokoza chinachake chimene mwana angachiphunzire atangolangizidwa pang’ono chabe.

Mwambi wina wa Chiakani umati: “Mulungu amakuonabe, ungam’thaŵe motani.” Motero munthu amangodzinyenga ngati akunyalanyaza Mulungu. Kalekale, Baibulo linatchulaponso mfundo yangati imeneyi ponena kuti maso a Mulungu “ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.” (Miyambo 15:3) Wamphamvuyonseyo amaona zochita zathu tonsefe.

Ya Zachikhalidwe

Monga momwe zimakhalira ndi miyambi ya zikhalidwe zina, nayonso miyambi ya Chiakani ndi nkhokwe ya chikhalidwe. Mwachitsanzo, mwambi uwu umasonyeza bwino zimene zoyankhula za munthu zingachite: “Kuphuluza ndi lilime n’koopsa kuposa kuphuluza ndi phazi.” Mukapanda kusamala, pakamwa pangathe kukupweteketsani ngakhale kukuphetsani kumene.—Miyambo 18:21.

Komabe, tikagwiritsira ntchito lilime mosamala, lingatithandize kwambiri pokhazikitsa mtendere, malinga ndi mwambi winanso wakuti, “Pakakhala lilime, mano salimbana.” Mfundo apa njakuti anthu omwe akulimbana, kaya ndi mwamuna ndi mkazi wake, angathetse mkangano wawo mwamtendere pokambirana mwabata. Ndipo ngakhale atalephera kutero, kugwiritsira ntchito lilime mwaluso pofuna kuwagwirizanitsa anthuwo kungathandize kuthetsa mkanganowo.

Yopatsa Nzeru

Phindu la kukhala wozindikira ndiponso kukonzekereratu pochita zinthu limafotokozedwa bwino m’miyambi yambiri yosonyeza kufunika kochita zinthu mwanzeru. Munthu wamphulupulu, wochita zinthu mwamavuvu komanso mosaganizira kaye angaphunzireko m’mwambi wakuti, “Kuputa njoka ya mamba n’kulinga uli m’pothaŵira.”

Kholo limene laona kuti mwana wake wayamba khalidwe linalake loipa lingafunikire kutsatira mwambi wakuti, “Ukaona tsekera likukula moti likuloŵa m’maso, umalizula, sulisongola.” Inde, khalidwe lililonse loipa n’lofunika kulizula, kapena kulibudula nsonga, lisanafike pokhala vuto lalikulu.

Yosimba za Miyambo

Nthaŵi zina kuti munthu amvetse matanthauzo a miyambi amafunika kudziŵa chikhalidwe cha eni miyambiyo. Mwachitsanzo, kwa Aakani, kugwiritsira ntchito dzanja lamanzere poyankhula pamaso pa anthu, makamaka achikulire n’kupanda mwambo. Zimenezo n’zogwirizana ndi mwambi uwu, wakuti, “Manzere sulozera njira yakwanu.” Kutanthauza kuti munthu azilemekeza zinthu zomwe ali nazo, kuphatikizaponso kwawo.

Mwambi wonena za mwambo wa kadyedwe ka Aakani umati: “Mwana wodziŵa kusamba m’manja amadya ndi akulu.” Panthaŵi ya chakudya, banja amaligaŵa malinga ndi misinkhu. Koma mwana wakhalidwe labwino, makamaka akakhala waukhondo ndiponso waulemu, angathe kum’lola kumakadya ndi bambo ake ndiponso akuluakulu ena. Mwambiwu umaphera mphongo mfundo yakuti munthu amalandira ulemu makamaka chifukwa cha zochita zake osati chifukwa cha msinkhu wake.

Kodi mukuganiza zopeza banja? Ndiyetu ganizirani mwambi wa Chiakani wakuti, “Banja salaŵa ngati uchema.” Anthu ogulitsa uchema, mowa womwe amagoma ku mtengo wa mgwalangwa, nthaŵi zambiri amalola anthu omwe akufuna kugula kuti aulaŵe kaye. Koma banja sayamba alaŵa kaye. Mwambiwu umasonyeza kuti munthu akaloŵa m’banja, waloŵeratu ndiponso kuti ukwati woyesa ngosavomerezeka.

Kuphunzira pa Zinthu Zosiyanasiyana

Miyambi yawo yambiri imasonyeza kuti makolo akale a Chiakani ankaonetsetsa kwambiri zochitika za anthu ndiponso zinyama, n’kumaphunzirapo kanthu. Mwachitsanzo, chifukwa choonetsetsa zochita za nkhuku ndi anapiye ake, anapeka mwambi uwu, “Mwanapiye wofupikirana m’make ndiye amadya ntchafu ya chiwala.” Kodi mwambiwu umatanthauzanji? Munthu akamadzipatula pakati pa anzake, amaiŵalidwa anzakewo akamagaŵana zinthu zabwino.

Munthu aliyense amene anaonapo chule wakufa angathe kumvetsa chifukwa chomwe amanenera kuti, “Kuona utali wa chule n’kulinga atafa.” Mwambiwu amautchula kaŵirikaŵiri ponena za munthu amene saŵerengeredwa. Zikakhala choncho, munthu wosaŵerengeredwayo amalimbako mtima akamaganizira kuti anthu adzatha kuona zabwino zake zonse iye pakadzakhala palibe.

Chidule cha Miyambi

Ngakhale kuti miyambi ya Chiakani yadzafika mumbadwo uno mochita kuuzana m’pakamwa, miyambi yambiri yasungidwa pogwiritsira ntchito luso losema ndi lojambula. Miyambi imeneyi imapezeka m’ziboliboli, ndodo, miyala ya sikelo, ndiponso zovala za Aakani komanso makaka a nsalu zamakono. Anthu akapita ku Ghana ku zionetsero za zinthu zosiyanasiyana zopangidwa mwaukatswiri amatha kukaona zithunzi za munthu akuthandizidwa ndi mnzake kuti akwere mtengo. Chimenechi ndi chithunzi chosonyeza mwambi wakuti, “Ukamakwera mtengo waukulu bwino, okukankha amapezeka.” N’zosachita kufunsa kuti akufuna kutanthauza chiyani; munthu akamachita zinthu zaphindu, ena amatha kum’thandiza.

Makamaka pamaliro m’pamene pamakhala mpata woti ‘nsalu ziyankhule,’ malinga n’kunena kwa mkulu wina wa zolembalemba. Chisoni cha pamaliro chimapangitsa anthu kuuganizira mozama moyo. Motero, makaka a nsalu za pamaliro amakhala ndi uthenga wa nzeru zakuya kwambiri. Mwachitsanzo, nsalu ya makaka a makwerero kapena masitepe imachititsa anthu kuganizira mwambi wakuti, “Makwerero a imfa sukwera wekha.”  * Mwambiwu umakumbutsa anthu kuti asamadzikuze ndiponso asamakhale ngati sadzafa.—Mlaliki 7:2.

Kwa Aakani, nthumwi za mfumu zimadziŵa bwino kwambiri kupha miyambi komanso zimanyamula ndodo zachifumu zogobedwa mfundo inayake yaikulu pachikhalidwe chawo. Mwachitsanzo, chithunzi chosonyeza mbalame itapana mutu wa njoka n’chidule cha mwambi wakuti, “Ukagwira njoka kumutu kotsalako n’luzi lokhalokha.” Kodi uthenga wa m’mwambiwu ndi wotani? Osamakayikayika pofuna kuthetsa vuto, pamafunika kungolimba nazo basi.

Kugwiritsira Ntchito Bwino Miyambi

Mofanana ndi fanizo lililonse, mwambi umafunika kuti uzigwirizana ndi nkhani ndiponso anthu amene mukuwauzawo. Mfundo sizingamveke bwino chifukwa chogwiritsira ntchito miyambi molakwika. Komanso anthu amitundu ina akamayankhula, pa mwambo wawo amayenera kugwiritsira ntchito miyambi motero munthu akapha mwambi molakwika anthu samam’patsa ulemu.

Ku Ghana, amaona kuti eni miyambi ndi anthu achikulire. Motero pofuna kunena mwambi, munthu amayamba n’kuti, “Akuluakulu amati . . . ” Ndipo poyankhula ndi anthu achikulire kwambiri, n’chinthu chaulemu kuti munthu asananene mwambi ayambe ndi kuti, “Paja akuluakulunu mumati . . . ” Posonyeza ulemu, munthu wamng’ono amene akuyankhula ndi achikulire safunika kuoneka ngati akupatsa achikulirewo nzeru kudzera m’miyambi.

Zina Zofunika Kudziŵa Zokhudza Miyambi

Miyambi ingathe kutchulidwa munthu asanatchule mfundo yomwe akuifuna kapena ataitchula kale. Komanso, ingathe kuphatikizidwa bwinobwino m’mfundo inayake moti munthu angafunike kuganiza mozama kuti azindikire kuti muli mwambi. Mwachitsanzo, ponena za munthu wodzichepetsa komanso wokonda mtendere, munthu wa Chiakani anganene kuti: “Pakanakhala auje ndi auje okha, sibwenzi m’mudzi muno mukulira mfuti.” Izi zimawakumbutsa mwambi wakuti, “Pakanakhala nkhono ndi kamba basi, sibwenzi kuthengo kukulira mfuti.” Tinyama tiŵiriti amaona kuti n’todzichepetsa, tosakonda za mtopola, ndiponso sitikonda zandewu. Anthu amakhalidwe ameneŵa amapangitsa kuti pakhale mtendere.

Komabe, ngati mutapempha munthu wa Chiakani kuti angokuuzani miyambi yosiyanasiyana, iye angathe kungokuuzani umodzi wokha, wakuti, “Kulota n’kulinga uli mtulo.” Kapena kuti, miyambi sakamba popanda nkhani yake, monganso kuti munthu sangalote ali m’maso. Zimene zikuchitika n’zimene zimasonyeza mwambi woyenera kuutchula.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Tineneko apa kuti makakaŵa amapezeka pa nsalu zamitundumitundu osati pa nsalu zakuda zokha zomwe nthaŵi zambiri zimavalidwa pamaliro.