Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wokaona Munda wa Nthochi

Ulendo Wokaona Munda wa Nthochi

Ulendo Wokaona Munda wa Nthochi

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA

KUYAMBIRA kale nthochi ndimazikonda kwambiri. Ndikukhulupirira kuti anthu ena ambirinso amazikonda. Nthochi zimakoma kwambiri komanso zili ndi zinthu zambiri zofunikira m’thupi. Kodi mungafune kuti mudziŵe zambiri zokhudza chipatso chopatsa thanzi chimenechi? Chaposachedwapa mlimi winawake ndi mkazi wake anandionetsa mmene nthochi zimaberekerana.

Tony ndi Marie (amene ali pamwambawo) amalima m’dera lina lotchedwa Levubu lomwe lili m’chigawo cha Limpopo, m’dziko la South Africa. Iwo ali ndi famu ya maekala okwana 140 imene amalimamo mbewu zosiyanasiyana. Koma mbali yaikulu ndi ya nthochi. Tony ndi wokonzeka kuti atiuze bwino za chipatso chomwe anthu ambiri amachikondachi.

Madera Amene Zimakula Bwino

Tony anati: “Dothi labwino kwambiri paulimi wa nthochi limakhala lonyata ndipo silikhala lamchenga kapena lamiyala kwambiri. Lizikhala m’madera amene miyala ili pansi kwambiri komanso lisamachite loŵe msanga. Nthochi zimakula bwino m’madera osazizira kwambiri. Tingoti zimakonda kumadera otentherapo ndithu. Nthaŵi zambiri pachaka, ku Levubu kumakhala kotentha ndithu.” Nditafunsa za mvula, Tony anayankha kuti: “Nthochi zimakula bwino ndi mvula basi kapena pozithirira kamodzi kokha pa mlungu.”

Nthochi si mtengo ayi ngakhale kuti imaoneka choncho. Nthochiyo ikamakula masamba ake amathithikizana kwambiri n’kuchititsa kuti izioneka ngati mtengo. Chithime cha nthochi chimakhala pansi panthaka. Mizu yake imapita pansi kuchokera pachithimepo ndipo masamba amaphukira pamenepo kenaka pamadzatuluka chiduŵa chofiirira. Mphukira zimatulukanso pomwepo kenaka n’kudzasanduka mbewu ina ya nthochi.

Mbewu ya nthochi ikaphuka n’kukula imaphukanso paŵiri ndipo alimi a kumeneko amatcha mbewuzo kuti ndi “agogo, mwana, ndi chidzukulu.” (Onani chithunzicho.) Agogo amabereka chaka chino, ndipo mwana chaka cha maŵa, kenaka chidzukulu, chaka cha mkuja. Zidzukulu zimakhala zambirimbiri ndipo zimakhala moyandikana ndi mayi wawo. Tiana timeneti tikakula kufika cham’mawondomu, amatidula n’kungosiya tomwe tikukula bwino.

Chiduŵa chofiirira chija, chomwe chimadzakhala mkoko wa nthochi chimachokera pachithime chija n’kudutsa pakatikati pa nthochiyo. Chimadzatulukira pakati pa masamba aŵiri a kunsonga kenaka chimadzazondoka. Chiduŵacho chikamakungunuka, pamayamba kuoneka timaphava ting’onoting’ono tokwana 10 kapena 15 tomwe timapanga mkoko ndipo munthu wosadziŵa amaona ngati tazondoka. Pa phava limodzi pamatha kukhala tinthochi 20 kapena kuposapo.

Nthaŵi Yodula Nthochi

Chitulukireni chiduŵa chija, pamatenga miyezi itatu kapena isanu ndi umodzi kuti anthu adule nthochizo malingana ndi nyengo imene chinatulukira m’chaka chimenecho. Nthochizo amazidula zili zosapsa, koma amaonetsetsa kuti zakhwima. Kaŵirikaŵiri mkoko wa nthochi umene ungayende malonda umakhala wolemera makilogalamu 35. Podula nthochizo amakuta mkokowo ndi pulasitiki kuti zisakandikekandike popita nazo kunyumba yozisungiramo, pa lole. Zikafika m’nyumba imeneyi nthochizo amazichotsa pa mkoko wake n’kuzidula m’timaphava mwina tanthochi zitatu kapena zisanu ndi imodzi kenaka n’kuziwaza mankhwala oti zisawonongeke.

Ku South Africa amati akatero, nthochizo amakaziika m’makatoni enaake opita mphepo n’kukawaika m’chipinda chovundikiramo nthochi. M’menemu amapemereramo mpweya womwe umathandizira kuti nthochizo zipse. * Nthochizo amazitsekera m’chipindamu kwa tsiku lonse kapena masiku aŵiri kenaka amakazigulitsa.

Tony ananena mosereula kuti: “Kaya, mwina ineyo ndikukokera kwathu, koma ndimaona kuti nthochi za kuno ku Levubu n’zokoma kwambiri kuposa za kwina, mwina chifukwa cha dothi la kwathu kunoli. Koma timadaundaula chifukwa sitili kufupi ndi mzinda uliwonse wogulitsirako zinthu kumayiko akunja, motero ndi anthu a m’dziko muno okha amene amadya nthochizi.”

N’zopatsa Thanzi

Nthochi zili ndi mavitameni ofunika m’thupi. “Kafukufuku wosiyanasiyana amasonyeza kuti mavitameni ameneŵa amathandiza kulimbitsa mafupa ndiponso kuti munthu apeŵe matenda a kuthamanga kwa magazi ndi opuwalitsa ziwalo,” inatero nkhani ina yonena za nthochi m’magazini yotchedwa Health. Magaziniyo inafotokozanso kuti: “Nthochi zilinso ndi mavitameni othandiza kuti ana azibadwa opanda chirema, ndipo mavitameniŵa ngofunika kwambiri kwa azimayi onse oyembekezera kapena amene afika msinkhu wobereka.” Nthochi zilinso ndi zinthu zina zofunika kwambiri zothandiza kuti mafupa azikhala olimba nthaŵi zonse.

Nthochi zili ndi mitundu yokwana 18 ya timadzi tinatake tomanga thupi, ndipo pamitunduyi palinso timadzi tina tofunika kwambiri m’thupi mwathu tomwe thupi lathuli silingathe kutipanga palokha. Nthochi zimam’patsa munthu mphamvu mwamsanga chifukwa chakuti sizichedwa kupukusika m’mimba. Pothirirapo ndemanga, Marie ananena mokondwera kuti: “Nthochi zimatipatsa mavitameni A, B, ndi C ambiri.” Komanso nthochi zimaoneka kuti zimakola msanga chifukwa chakuti anthu ambiri sakonda kudya zambiri pa nthaŵi imodzi.” Ndiye bwanji osalaŵako imodzi chabe, chifukwatu njothandiza m’thupi komanso sikukoma kwake!

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Nthochi zikamapsa zokha, zimatulutsa mpweya woterewu umene umapangitsa kuti zipse msanga. Apa ndiye kuti njira ina yoti nthochi zosapsa zipse ndiyo kuziika pamodzi ndi nthochi zingapo zakupsa.

[Chithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Tsamba

Nthochi ndi chiduŵa

Chikhungwa chake

Pansi

Chithime

Muzu

[Mawu a Chithunzi]

Sketch: Based on drawing from The Complete Encyclopedia of Illustration/J. G. Heck

[Chithunzi patsamba 27]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Agogo

Mwana

Chidzukulu

[Zithunzi patsamba 27]

Chiduŵa chofiirira chimadzasanduka mkoko wa nthochi

[Mawu a Chithunzi]

Photo by Kazuo Yamasaki

[Zithunzi patsamba 28]

Nthaŵi yodula (kumanzereku); nthochi zomwe zidakali zazing’ono (pamwambapa)