Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?

Tchulani zinthu zitatu pa chithunzichi zomwe sizikugwirizana ndi nkhani ya m’Baibulo ya pa Genesis 7:1-9, 13-16, 23; 8:15-19.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Yerekezerani Levitiko 11:3 ndi Deuteronomo 14:4.

3. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Yerekezerani ndi Deuteronomo 14:7-19.

KAMBIRANANI:

Kodi Nowa anathandizidwa bwanji ndi ana ake komanso azipongozi ake? Kodi mungatsanzire bwanji ana a Nowa?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 6 Kodi munthu wokonda ndalama sangakhale ndi chiyani? Mlaliki 5:․․․

TSAMBA 9 Kodi ndi anthu otani amene angakhale osangalala? Mateyo 5:․․․

TSAMBA 18 Kodi munthu sayenera kuchita chiyani popemphera? Mateyo 6:․․․

TSAMBA 28 Kodi tizitani tikakhala ndi nkhawa? 1 Petulo 5:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?

Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenako lembani mayina olondola pa mizereyi.

4. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ngakhale kuti bambo anga anali ndi khalidwe loipa, ine ndinali mfumu imene ‘inaumirira Yehova.’

Werengani 2 Mafumu 18:1-6.

5. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinagwiritsa ntchito molakwika mphamvu zanga mwa kupha anthu ambiri osachimwa.

Werengani 2 Mafumu 21:16.

6. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinatengera khalidwe loipa la bambo anga ndipo ndinaphedwa ndi anyamata anga.

Werengani 2 Mafumu 21:19-23.

▪ Mayankho ali pa tsamba  22

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1.  Chingalawa sichinali chosongoka kumbuyo ndi kutsogolo.

2. Nowa analowetsa m’chingalawa nyama 7 “zoyera,” monga nkhosa.

Nowa analowetsa m’chingalawa nyama ziwiri zokha pamtundu uliwonse wa nyama ‘zodetsedwa.’

Hezekiya.—Mateyo 1:9.

5. Manase.—Mateyo 1:10.

6. Amoni.—Mateyo 1:10.