Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngati Zinthu Sizikuyenda Bwino

Ngati Zinthu Sizikuyenda Bwino

Ngati Zinthu Sizikuyenda Bwino

Mtsikana wina anakhala katswiri woimba ali ndi zaka za m’ma 20 ndipo anali wolemera kwambiri. Anthu ambiri sakhala otchuka komanso olemera ali pa msinkhu umenewu. Koma kenako zinthu zinayamba kusokonekera pamoyo wake. Atakwatiwapo kawiri konse koma banja n’kutha, anakakhala kumalo othandizirako anthu omwa mowa kwambiri ndiponso ogwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Moyo wake wonse unasokonezeka.

N’ZOMVETSA chisoni kuti nkhani ngati zimenezi ndi zofala kwambiri. Nthawi zambiri, nkhani zomvetsa chisoni za anthu otchuka zimalembedwa m’manyuzipepala. Ngakhale anthu ena amalonda amene amaoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino, nthawi zambiri amakumana ndi mavuto. Ponena za anthu a mu mzinda wa New York, nyuzipepala ina inati: “Maganizo ofuna kupeza phindu lalikulu kwambiri amawononga ntchito, amasokoneza mabanja ndipo amachititsa anthu ambiri kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. . . . Ngakhale kuti ogwira ntchito ku mabanki a ku msika wa makampani wa Wall Street amalandira ndalama zambiri zimene zimawapangitsa kuona kuti ndi ochita bwino, ena amakhala osasangalala ndipo sagwira bwino ntchito.”

Kodi mavuto amenewa amachitika chifukwa chakuti anthu akufuna kuti zinthu ziziwayendera bwino ndiponso azisangalala koma m’njira yolakwika? N’zoona kuti ndalama n’zofunika kuti tipeze zinthu zina pamoyo. Koma kodi munthu akakhala ndi ndalama zambiri ndiye kuti zinthu zizimuyendera bwino? Kafukufuku wasonyeza kuti zimenezi sizoona. Mwachitsanzo, kafukufuku wina yemwe wachitika chaposachedwapa ku China wasonyeza kuti ndalama zimene anthu ambiri amapeza zitawonjezereka kwambiri, anthu anakhalabe osasangalala.

Motero, kuyenda bwino kwa zinthu kumadalira chinachake chapadera kwambiri osati ntchito, mtengo wa nyumba, galimoto kapena wotchi. Kuyenda bwino kwa zinthu kumaoneka ndi mmene munthuyo alili, mfundo zimene akutsatira ndiponso cholinga cha moyo wake. Mwachitsanzo, munthu angakhale wanzeru ndiponso wamphamvu, koma ali wamakhalidwe oipa, wopanda chikondi ndiponso wopanda mabwenzi enieni. Wina angakhale wotchuka ndiponso wolemera koma akaganizira za moyo wake angamadzifunse kuti, ‘Kodi ndimadzivutiranji? Kodi cholinga cha moyo wanga n’chiyani?’

Motero, m’pomveka kunena kuti anthu amene zinthu zimawayendera bwino ndi amene amachita zinthu zofunika kwambiri pamoyo ndiponso amene amatsatira mfundo zabwino. Iwo amakhala ndi mtendere wa m’mtima, amadzilemekeza ndipo amalemekezedwanso ndi anthu ena. Moyo wa anthu oterewa umakhala ndi cholinga ndipo amakhala osangalala. Iwo samangofuna kuchita zinthu zokomera iwo okha. Komabe, anthu ena angafunse kuti, ‘Kodi mfundo zake n’ziti ndipo cholinga chake n’chotani?’ Koma kodi patokha tingapeze mayankho a mafunso ngati amenewa, kapena tingawapeze kwinakwake? Nkhani yotsatira ifotokoza zimenezi.

[Bokosi patsamba 3]

MAGANIZO OLAKWIKA PANKHANI YOPAMBANA

Malinga ndi zomwe ochita kafukufuku wa zamankhwala apeza, achinyamata ambiri ochita masewera othamanga amamwa mankhwala amene angawononge thanzi lawo n’cholinga choti apambane pa masewerawo. Magazini ina ya pa Intaneti inati: “Pakafukufuku waposachedwapa, ophunzira ena apakoleji anafunsidwa kuti: ‘Kodi mungatani ngati mutadziwa kuti mukamwa mankhwala owonjezera mphamvu mupambana masewera kapena musankhidwa kukhala m’gulu lochita nawo masewerawo koma pambuyo pa zaka zisanu, mankhwalawo akudwalitsani?’ Pafupifupi ophunzira onse anayankha kuti angamwebe mankhwalawo. Ndipo atafunsidwanso kuti ‘angatani atadziwa kuti afa pasanathe zaka zisanu,’ achinyamata oposa theka la ofunsidwawo anayankha kuti angamwebe mankhwalawo.”—Education Update.