Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Mapemphero Anga Azikhala Abwino?

Kodi Ndingatani Kuti Mapemphero Anga Azikhala Abwino?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Mapemphero Anga Azikhala Abwino?

“Ukakhala ndi zochita zambiri kusukulu, kuntchito, kunyumba, kaya ndi anzako, nthawi zina umaiwala kuti Mulungu ndiye wofunika kwambiri.”—Anatero Faviola, wazaka 15, wa ku United States.

“MUZIPEMPHERA mosalekeza.” (1 Atesalonika 5:17) “Limbikiranibe kupemphera.” (Aroma 12:12) “Zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6) Ngati ndinu Mkhristu, mosakayikira mumawadziwa bwino malemba amenewa. Ndiponso mumazindikira kuti pemphero ndi njira yolankhulirana yodabwitsa kwambiri. Tangoganizirani, mungalankhule ndi Mulungu Wamphamvuyonse nthawi ina iliyonse, kaya masana kapena usiku. Ndipo Baibulo limati: “Amatimvera.” *1 Yohane 5:14.

Komabe, mofanana ndi mtsikana amene tamugwira mawu pamwambapa, zingatheke kuti kupemphera kumakuvutani. Zimenezi tingaziyerekeze ndi chitseko chokhoma. Ngati mukuona choncho, kodi mungathetse bwanji vuto lanu? Nkhani ino ikuthandizani (1) kuzindikira zimene zimakulepheretsani kupemphera, (2) kukhala ndi cholinga popemphera, ndipo (3) kuthetsa vuto lanu pankhani yopemphera, komwe kuli ngati kutsegula ndi kiyi chitseko chokhoma.

Choyamba, zindikirani vuto limene muli nalo. Kodi n’chiyani kwenikweni chimene chimakuvutani popemphera? Lembani yankho lanu m’munsimu.

․․․․․

Chachiwiri, khalani ndi cholinga. M’munsimu, chongani cholinga chimene mukufuna kukwaniritsa, kapena lembani cholinga china chimene muli nacho pamzere umene uli pafupi ndi mawu akuti “China.”

□ Ndikufuna kumapemphera kawirikawiri.

□ Ndikufuna kuti ndisamanene zinthu zomwezomwezo nthawi zonse popemphera.

□ Ndikufuna kuti ndizipemphera mochokera pansi pa mtima.

□ China ․․․․․

Mmene Mungathetsere Vuto Lanu

Pemphero lili ngati chitseko chokhoma chimene mungatsegule nthawi ina iliyonse ndi kiyi. Komabe, achinyamata ambiri anganene kuti satsegulatsegula chitseko chimenechi ndipo ena satsegula momasuka mmene amayenera kuchitira. Ngati zili choncho kwa inu, musade nkhawa. Popeza mwazindikira vuto lanu komanso muli ndi cholinga, chatsala n’kudziwa mmene mungathetsere vutolo. Onani zinthu zina zimene zingakulepheretseni kupemphera, komanso zimene mungachite kuti muthetse zimenezo.

Cholepheretsa: KUNYALANYAZA. “Nthawi zina ndimanyalanyaza kupemphera chifukwa chotanganidwa.”—Anatero Preeti, wazaka 20, wa ku Britain.

Mmene Mungalithetsere: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru, podziwombolera nthawi yoyenerera chifukwa masikuwa ndi oipa.”—Aefeso 5:15, 16.

Yesani Kuchita Izi: Sankhani nthawi yabwino, imene mungamapemphere tsiku lililonse. Mukhoza kulemba pa pepala nthawiyo, monga mmene mungachitire ngati mukufuna kukumbukira chinachake. “Ngati sindinasankhiretu nthawi yeniyeni yopemphera, ndimatanganidwa ndi zinthu zina,” anatero mtsikana wa ku Japan, wazaka 18, dzina lake Yoshiko.

Cholepheretsa: KUGANIZA ZINA. “Sindichedwa kuyamba kuganiza zinthu zina, m’malo moganizira zimene ndikunena.”—Anatero Pamela, wazaka 17, wa ku Mexico.

Mmene Mungalithetsere: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.”—Mateyo 12:34.

Yesani Kuchita Izi: Ngati muli ndi vuto loti mumayamba kuganizira zinthu zina pamene mukupemphera, yesani kupemphera mapemphero afupiafupi mpaka pamene mudzayambe kuika maganizo pa zimene mukupemphera. China chimene mungachite n’chakuti, muzipempherera zinthu zimene zakukhudzani mtima kwambiri. Marina, wazaka 14, wa ku Russia anati: “Ndili ndi zaka 13 ndinayamba kuganizira mfundo yakuti tikamapemphera timakhala tikulankhulana ndi Mulungu. Mfundo imeneyi yandithandiza kuti ndizimuuza zakukhosi kwanga.”

Cholepheretsa: CHIZOLOWEZI. “Ndikamapemphera, ndimapezeka ndikungobwerezabwereza mawu.”—Anatero Dupe, wazaka 17, wa ku Benin.

Mmene Mungalithetsere: “Ndidzalingalira ntchito yanu yonse, ndi kulingalirabe zimene munazichita Inu.”—Salmo 77:12.

Yesani Kuchita Izi: Ngati mumapemphera mobwerezabwereza popanda kuganizira zimene mukunena, tsiku lililonse muzilemba chinthu chimodzi chimene Yehova wakuchitirani pamoyo wanu. Ndiyeno m’thokozeni Yehova chifukwa cha zimenezo. Chitani zimenezi mlungu wonse, ndipo mudzaona kuti mwapempherera zinthu 7 popanda kubwereza. Chitaninso zimenezi pa zochitika za tsiku lililonse. Mnyamata wazaka 21 wa ku Brazil, dzina lake Bruno, anati: “Ndikamapemphera, ndimayesetsa kutchula zinthu zimene zachitika tsiku limenelo.” Zimenezi n’zimenenso amachita mtsikana wina wazaka 18, wa ku United States, dzina lake Samantha. Iye anati: “Patsiku ndimayesetsa kukumbukira zimene zachitika zosiyana ndi masiku ena, ndipo ndimatchula zimenezo popemphera. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamabwerezebwereze mawu.” *

Cholepheretsa: KUKAYIKIRA. “Nthawi ina ndinapemphera za vuto linalake limene ndinali nalo kusukulu kwathu, koma silinathe. M’malo mwake panawonjezeka mavuto ena. Ndinaganiza kuti, ‘Ndiye ndizipempheranso chifukwa chiyani, popeza Yehova sakundiyankha?’”—Anatero Minori, wazaka 15, wa ku Japan.

Mmene Mungalithetsere: “Pamene mukukumana ndi mayeserowo [Yehova Mulungu] adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.”—1 Akorinto 10:13.

Yesani Kuchita Izi: Chodziwikiratu n’chakuti: Yehova ndi “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Choncho, mukapemphera za nkhani inayake, yesani kuimvetsa bwino nkhani yonseyo. M’malo moyembekeza kuti akuyankheni mmene mukufunira, onani ngati wakuyankhani kale m’njira inayake. Mfundo yakuti mukupirira monga Mkhristu ikutanthauza kuti n’kutheka kuti Yehova anayankhadi pemphero lanu, osati mwa kuthetsa vuto lanu koma pokupatsani mphamvu kuti mupirire.—Afilipi 4:13.

Cholepheretsa: MANYAZI. “Ndimachita manyazi ndikaganizira zoti anzanga akusukulu andiona ndikupemphera panthawi yachakudya.”—Anatero Hikaru, mnyamata wazaka 17, wa ku Japan.

Mmene Mungalithetsere: “Kanthu kali konse kali ndi nthawi yake.”—Mlaliki 3:1.

Yesani Kuchita Izi: Ngakhale kuti anthu ena angakuyamikireni atakuonani mukupemphera, musamapemphere kuti ena akuoneni. Mwachitsanzo, pemphero lalifupi limene Nehemiya anapemphera pamaso pa Mfumu Aritasasta linali la mumtima ndipo palibe umboni wakuti mfumuyo inadziwa kuti iye amapemphera. (Nehemiya 2:1-5) Inunso, mungapemphere chamumtima kwa Yehova popanda ena kuzindikira zimenezo.—Afilipi 4:5.

Cholepheretsa: KUDZIONA WOSAYENERA. “Yehova amawadziwa kale mavuto anga. Ndipo ngati ineyo ndatopa nawo, ndiye kuti iyenso amutopetsa. Ndipo nthawi zina ndimaganiza kuti ndine wosayenera kulankhula naye.”—Anatero Elizabeth, wazaka 20, wa ku Ireland.

Mmene Mungalithetsere: ‘Tulirani [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amasamala za inu.’—1 Petulo 5:7.

Yesani Kuchita Izi: Khalani ndi cholinga chowerenga malemba otsatirawa paphunziro lanu laumwini: Luka 12:6, 7; Yohane 6:44; Aheberi 4:16; 6:10; 2 Petulo 3:9. Malemba amenewa adzakuthandizani kudziwa kuti Yehova amafunadi kumva zonena zanu ndipo simufunikira kukhala munthu wauzimu kwambiri kuti akumvetsereni. Wamasalmo Davide yemwe panthawi ina anali ndi nkhawa komanso mavuto, ananena motsimikiza mtima kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” *Salmo 34:18.

Mfundo yakuti Yehova amamvetsera mapemphero anu imasonyeza kuti iye amakukondani. Mtsikana wazaka 17 wa ku Italy, dzina lake Nicole, anati: “Yehova sanapereke udindo womvetsera mapemphero athu kwa angelo. Popeza kuti iye ndi amene amamvetsera mapemphero athu, n’zoonekeratu kuti amawaona kukhala ofunika kwambiri.”

Nkhani zina zakuti Zimene Achinyamata Amafunsa, mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.ps8318.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Popeza kuti kumva kwa Mlengi sikudalira chipangizo chilichonse kapenanso kuti munthu achite kufuula, iye “amamva” ngakhale mawu amene talankhula chamumtima.—Salmo 19:14.

^ ndime 32 Ngati mukuona kuti Yehova sangamve mapemphero anu chifukwa munachita tchimo lalikulu, muyenera kuuza makolo anu. Ndiponso ‘itanani akulu a mpingo [kuti akuthandizeni].’ (Yakobe 5:14) Akulu angakuthandizeni kuti mukhalenso ndi ubwenzi wabwino ndi Yehova.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi ndi zinthu zina ziti zofunika kwa Yehova zimene mungapempherere?

▪ Kodi ndi nkhani ziti zokhudza anthu ena zimene mungamuuze Yehova?

[Bokosi/Zithunzi patsamba 28]

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU ANENA

“Pemphero lili ngati kabuku kolembamo zachinsinsi kamene ungakawerenge wekha ndi Yehova basi.”—Anatero Olayinka, wa ku Nigeria.

“Tayerekezerani kuti muli ndi mnzanu wapamtima ndipo munamupatsa mphatso zambiri. Kenako, tsiku lina mnzanuyo n’kusiya kukulankhulani. Yehova amamvanso chimodzimodzi tikasiya kupemphera kwa iye.”—Anatero Chinta, wa ku Australia.

“Nthawi zonse ndakhala ndikuona kuti n’kulakwa kunena zimene zili mu mtima mwanga. Koma mwayi wopemphera wandithandiza kuzindikira kuti sikulakwa kusangalala, kukwiya kapena kuvutika maganizo ndi zinazake. Ndiponso sikulakwa kum’fotokozera Yehova zimenezi. Tsopano ndikudziwa mmene ndingachitire ndikakhumudwa kapena kuvutika maganizo.”—Anatero Amber, wa ku United States.

[Chithunzi patsamba 27]

Ngati mukuona kuti pemphero lili ngati chitseko chokhoma, gwiritsani ntchito makiyi a m’Mawu a Mulungu, Baibulo