Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mutha Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni

Mutha Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni

Mutha Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni

Sarah Jayne anadziŵa zoti ali ndi matenda a kansa ya m’chibelekero ali ndi zaka 19. Atam’chita opaleshoni, anali kupeza bwino moti ankayembekezera tsogolo labwino. Analitu wotsimikiza kwambiri za tsogolo lake moti atafika zaka 20 anapeza mwamuna ndipo anayamba kukonzekera ukwati wake. Chaka chomwecho kansa ija inayambanso ndipo anamuuza kuti adzakhala ndi moyo milungu yochepa chabe. Sarah Jayne anamwalira mu June 2000 litangotsala tsiku limodzi kuti akwanitse zaka 21.

CHOMWE chinkachititsa chidwi anthu amene anali kudzamuona Sarah Jayne kuchipatala chinali kusadera nkhaŵa kwake za m’tsogolo komanso chikhulupiriro chake mwa Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo. Ngakhale anali pangozi yoopsa, anali wotsimikiza za chiyembekezo choti adzauka ndipo kuti adzaonananso ndi anzake onse. (Yohane 5:28, 29) Iye anati, “nonsenu tidzaonana m’dziko latsopano la Mulungu.”

Ena amanena kuti chikhulupiriro choterocho n’chonyenga. Ludovic Kennedy anafunsa kuti, “Kodi si anthu ovutika okha amene amakhulupirira kuti akamwalira adzakhalanso ndi moyo ndi kuti palipenga lotsiriza adzasangalala ndi zinthu zabwino ndi nyimbo zamalipenga komanso kukhala m’dziko lokongola ngati Edene komwe akasangalale ndi anzawo amene anamwalira kale ndiponso amene adzamwalire pambuyo pawo?” Ngati zili choncho, tingatsutse mwakufunsa kuti: Kodi chanzeru n’chiyani​—“kukhulupirira kuti moyo uno ndiwo wokha womwe ulipo, ndipo kuti n’kofunika kuugwiritsa ntchito mokwanira,” monga momwe Kennedy ananenera, kapena kukhulupirira Mulungu ndi lonjezo lake lakuti anthu akufa adzauka? Sarah Jayne anakhulupirira mfundo yomalizayi. Kodi chikhulupiriro chimenechi anachipeza bwanji?

‘Funafunani Mulungu . . . ndi Kum’peza’

Kuti mukhulupirire ndi kudalira munthu wina, mufunika kumudziŵa bwino ndi kuphunzira mmene amaganizira ndiponso zochita zake. Mtima ndi maganizo zimathandizana pochita zimenezi. N’chimodzimodzinso ndi kukulitsa chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu. Muyenera kumudziŵa bwino, kuphunzira mikhalidwe ndi umunthu wake, kuti muone kukhulupirika ndi kudalirika kwake m’zonse zomwe wanena ndi kuchita.​—Salmo 9:10; 145:1-21.

Ena amaganiza kuti zimenezi n’zosatheka. Amanena kuti ngati Mulungu aliko ndiye kuti ali kutali kwambiri ndipo ndi wosadziŵika. Anthu okayikira amafunsa kuti: “Ngati Mulungu ali weniweni monga momwe Akristu ngati Sarah Jayne amanenera, bwanji sakufuna kuti enafe timudziŵe?” Koma kodi Mulungu ali kutali kwambiri ndi kuti ndi wosadziŵika? Polankhula ndi afilosofi ndiponso anthu ophunzira kwambiri a ku Atene, mtumwi Paulo anati “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo,” waperekanso zonse zofunika kuti ‘tim’funefune [Iye] . . . ndi kum’peza.’ Ndiponsotu Paulo ananena kuti: “[Mulungu] sakhala patali ndi yense wa ife.”​—Machitidwe 17:24-27.

Ndiyeno, kodi ‘Mulungu mungam’funefune . . . ndi kum’peza’ motani? Ena achita zimenezo mwa kungoyang’ana zomwe analenga. Anthu ambiri amaona kuti chilengedwe pachokha chimapereka umboni wokwanira ndi wogwira mtima woti kuli Mlengi. * (Salmo 19:1; Yesaya 40:26; Machitidwe 14:16, 17) Anthu oterowo amaganiza monga momwe mtumwi Paulo ankaganizira kuti “chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake [za Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.”​—Aroma 1:20; Salmo 104:24.

Mufunika Baibulo

Komabe, kuti mukulitse chikhulupiriro chenicheni mwa Mlengi, mufunika chinachake chimene iye wapereka. Kodi chinachakecho n’chiyani? Ndicho Baibulo​—Mawu ouziridwa a Mulungu. M’Baibulo Mulungu amavumbula zomwe amafuna ndi zolinga zake. (2 Timoteo 3:16, 17) Komabe ena anganene kuti: “Kodi munthu angakhulupirire bwanji zomwe Baibulo limanena ngati akuona anthu amene amati amalitsatira akuchita zinthu zoipa?” N’zoonadi, Matchalitchi Achikristu ali ndi mbiri yoipa ya chinyengo, nkhanza, ndi chiwerewere. Komabe munthu woganiza bwino atha kuona kuti Matchalitchi Achikristu amangonamizira kuti amatsatira mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo.​—Mateyu 15:8.

Baibulo lenilenilo linachenjeza kuti anthu ambiri adzanena kuti amalambira Mulungu koma pamene kwenikweni ‘akukana Ambuye amene adawagula.’ Ndipo “chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano,” anatero mtumwi Petro. (2 Petro 2:1, 2) Yesu Kristu ananena kuti anthu oterowo ali “akuchita kusayeruzika” omwe angadziŵike mosavuta mwa kuona ntchito zawo zoipa. (Mateyu 7:15-23) Kukana Mawu a Mulungu chifukwa cha mbiri yoipa ya Matchalitchi Achikristu kuli ngati kutaya kalata ya bwenzi lodalirika chabe chifukwa chakuti munthu amene wabweretsa kalatayo ali ndi mbiri yoipa.

Kukulitsa chikhulupiriro chenicheni sikungatheke popanda Mawu a Mulungu. Yehova amapereka malingaliro ake kudzera m’Baibulo basi. Amavumbula mayankho a mafunso osatha monga akuti, n’chifukwa chiyani Mulungu walola anthu kuvutika ndipo kodi iye adzachitapo chiyani? (Salmo 119:105; Aroma 15:4) Sarah Jayne anakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu ouziridwa a Mulungu. (1 Atesalonika 2:13; 2 Petro 1:19-21) Motani? Osati chifukwa chakuti makolo ake anamuuza kukhulupirira zimenezo, koma chifukwa chakuti ankapeza nthaŵi kupenda moona mtima maumboni onse amene amasonyeza kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu. (Aroma 12:2) Mwachitsanzo, iye ankaonetsetsa kwambiri zomwe mphamvu ya mfundo zachikhalidwe za m’Baibulo yachita pa miyoyo ya anthu amene amatsatira mfundozo. Mabuku monga lakuti Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, * linam’thandiza kwambiri kupenda mosamalitsa maumboni ochuluka omwe amasonyeza kuti Baibulo linauziridwa ndi Mulungu.

“Chikhulupiriro Chidza ndi Mbiri”

Komabe, kukhala ndi Baibulo chabe kapena kukhulupirira kuti Mulungu ndiye analiuzira n’kosapindula kanthu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri.” (Aroma 10:17) Kumvera zomwe Baibulo limanena ndiko kumakulitsa chikhulupiriro osati kungokhala nalo chabe. ‘Mumamvera’ zomwe Mulungu akunena mwa kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu ake. Ngakhale ana atha kuchita zimenezi. Paulo ananena kuti, Timoteo “kuyambira ukhanda” wake, anaphunzira “malemba opatulika” kwa amayi ake ndi agogo ake aakazi. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti ankachita kumukakamiza? Iyayi! Timoteo sanam’kakamize kapena kumunyenga m’njira iliyonse. ‘Anatsimikiza mtima’ kukhulupirira zomwe anamva ndi kuŵerenga.​—2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.

Sarah Jayne nayenso anatsimikiza mtima m’njira yomweyo. Mofanana ndi Abereya a m’zaka za zana loyamba, Sarah “analandira mawu [kwa makolo ake ndi kwa aphunzitsi ena] ndi kufunitsa kwa mtima wonse.” Ali mwana, iye mosakayika ankakhulupirira kwambiri zomwe makolo ake anali kum’phunzitsa. Kenako atakula, sanali kungokhulupirira m’chimbulimbuli zilizonse zomwe ankam’phunzitsa. Iye ‘anasanthula m’malembo masiku onse kuti aone ngati zinthu zinali zotero.’​—Machitidwe 17:11.

Mutha Kukhala ndi Chikhulupiriro Chenicheni

Inunso mutha kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni​—chikhulupiriro chomwe mtumwi Paulo anatchula m’kalata yake yopita kwa Akristu achihebri. Iye anati, chikhulupiriro choterocho ndicho ‘chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.’ (Ahebri 11:1) Mutakhala ndi chikhulupiriro choterocho, ndiye kuti mudzakhala wotsimikiza kwambiri kuti zonse zomwe mukuyembekezera kuphatikizapo lonjezo la Mulungu lakuti akufa adzauka, zidzakwaniritsidwa. Mudzakhala wotsimikiza kuti ziyembekezo zoterozo n’zochokera pamaziko odalirika osati kungolakalaka zitachitika. Ndipo mudzadziŵa kuti Yehova sanalepherepo kukwaniritsa malonjezo ake. (Yoswa 21:45; 23:14; Yesaya 55:10, 11; Ahebri 6:18) Lonjezo la Mulungu la dziko latsopano lidzakhala lenileni ngati kuti muli kale m’dzikolo. (2 Petro 3:13) Mudzaona bwinobwino ndi maso anu achikhulupiriro kuti Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi Ufumu wa Mulungu ndi zinthu zenizeni osati zachinyengo.

Kuti mukhale ndi chikhulupiriro chenicheni sikuti ndi ntchito ya inu nokha. Kuwonjezera pa kupereka Mawu ake, Yehova waperekanso mpingo wachikristu wapadziko lonse womwe uli wodzipereka kuthandiza anthu oona mitima kukhulupirira Mulungu. (Yohane 17:20; Aroma 10:14, 15) Landirani thandizo lonse lomwe Yehova akupereka kudzera m’gulu limeneli. (Machitidwe 8:30, 31) Popeza kuti chikhulupiriro ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, pempherani nthaŵi zonse kuti mzimu umenewu ukuthandizeni kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni.​—Agalatiya 5:22.

Musagwe ulesi ndi anthu okayikira omwe amanyoza aliyense amene amakhulupirira Mulungu ndi Mawu ake. (1 Akorinto 1:18-21; 2 Petro 3:3, 4) Ndiponsotu chikhulupiriro chenicheni n’chofunika kwambiri polimbana ndi anthu otsutsa ngati ameneŵa. (Aefeso 6:16) Sarah Jayne anaona kuti zimenezi n’zoona ndipo ankalimbikitsa anthu amene anali kudzamuona kuchipatala kuti akhale ndi chikhulupiriro chawochawo. Iye ankanena kuti: “Pangani choonadi kukhala chanuchanu. Phunzirani Mawu a Mulungu. Khalanibe m’gulu la Mulungu. Pempherani nthaŵi zonse. Pitirizani kuchita changu potumikira Yehova.”​—Yakobo 2:17, 26.

Ataona chikhulupiriro chake mwa Mulungu ndi chiukiriro, nesi wake wina ananena kuti: “Umakhulupiriradi zimenezi, si choncho kodi.” Atamfunsa chomwe chinam’chititsa kukhala ndi chiyembekezo chabwino chimenecho ngakhale kuti anali m’mayesero, iye anayankha kuti: “Chinsinsi chake ndi kukhulupirira Yehova basi. Iye ndi bwenzi langa lenileni, ndipo ndimam’konda kwambiri.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onani buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 12 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 6]

Timoteo “kuyambira ukhanda” wake anaphunzira “malemba opatulika” kwa amayi ake ndi agogo ake aakazi

[Chithunzi patsamba 6]

Abereya anawayamikira chifukwa chosanthula Malemba tsiku ndi tsiku

[Mawu a Chithunzi]

Kuchokera pa “Seŵero la Pakanema la Chilengedwe,” mu 1914

[Zithunzi patsamba 7]

Kumvera ndi kutsatira zomwe Baibulo limanena ndiko kumakulitsa chikhulupiriro osati kukhala nalo chabe

[Chithunzi patsamba 7]

“Nonsenu tidzaonana m’dziko latsopano la Mulungu”