Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumaphunzitsa Ena Kuti Akhalenso Akulu?

Kodi Mumaphunzitsa Ena Kuti Akhalenso Akulu?

“Chilichonse chili ndi nthawi yake.”—MLAL. 3:1.

1, 2. Kodi oyang’anira madera ambiri amafuna kuti akulu azichita chiyani?

PAMENE woyang’anira dera ankatsanzikana ndi akulu mumpingo wina anawayamikira kwambiri. Ankaona kuti ambiri anali akhama ngakhale kuti ena anali achikulire. Koma woyang’anira derayo anali ndi nkhawa ndipo anawafunsa kuti: “Kodi abale mwachita zotani pothandiza ena kuti akhalenso akulu?” Apa akuluwo anakumbukira kuti pa ulendo wapita anauzidwa kuti athandize anthu ena. Kenako mkulu wina anayankha kuti: “Kunena zoona sitinachite zambiri.” Ndiyeno akulu ena onse anavomereza zimene mnzawoyo ananena.

2 Ngati ndinu mkulu n’kutheka kuti zimenezi zinakuchitikirani. Oyang’anira madera ambiri amaona kuti m’pofunika kuphunzitsa abale achinyamata ndi achikulire omwe kuti athandize poweta nkhosa za Mulungu. Koma n’chifukwa chiyani kuchita zimenezi kumavuta nthawi zina?

3. (a) Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti kuphunzitsa ena n’kofunika? (b) N’chifukwa chiyani aliyense ayenera kuganizira bwino mfundo za m’nkhaniyi? (Onani mawu am’munsi.) (c) N’chifukwa chiyani akulu ena amavutika kuphunzitsa ena?

3 Ngati ndinu mkulu, mukudziwa kuti kuphunzitsa ena n’kofunika. * Mukudziwa kuti pakufunika akulu ambiri kuti mipingo ikhalebe yolimba ndiponso kuti mipingo yatsopano ikhazikitsidwe. (Werengani Yesaya 60:22.) Mukudziwanso kuti Mawu a Mulungu amakulimbikitsani kuphunzitsa anthu ena. (Werengani 2 Timoteyo 2:2.) Koma n’kutheka kuti nanunso zimakuvutani kupeza nthawi yophunzitsa ena. Mwina mumatanganidwa kwambiri kusamalira banja lanu, kugwira ntchito zina komanso za pampingo. Ngakhale kuti mumatanganidwa chonchi, kuphunzitsa ena n’kofunika kwambiri. Tiyeni tikambirane zifukwa zake.

KUPHUNZITSA ENA N’KOFUNIKA KWAMBIRI

4. N’chifukwa chiyani akulu ena amasiya kuphunzitsa ena?

4 N’chifukwa chiyani akulu ena zimawavuta kupeza nthawi yophunzitsa ena? Mwina amaganiza kuti kuphunzitsa ena n’kosafunika kwambiri poyerekezera ndi ntchito zina zofunika mwamsanga mumpingo. Ena amaganizanso kuti mpingo ukhoza kumayenda bwinobwino ngakhale atasiya kaye kuphunzitsa ena. N’zoona kuti ntchito zambiri pampingo zimafunika kuzigwira mwamsanga, koma kusiya kuphunzitsa ena kungayambitse mavuto.

5, 6. Kodi tikuphunzirapo chiyani pa chitsanzo cha kholo limene mwana wake wadwala malungo?

5 Taganizirani chitsanzo ichi: Tiyerekeze kuti mwana wadwala malungo ndipo makolo ake akuganiza zomupatsa panado m’malo mopita naye kuchipatala. Akuchita zimenezi n’cholinga choti agwire ntchito zina zofunika. Iwo akuganiza kuti mwanayo akhalabe ndi mphamvu ngakhale kuti sanapatsidwe mankhwala a malungo. Kodi zimenezi n’zoopsa bwanji? Ngati makolowo atapitirizabe kuchita zimenezi, matenda a mwanayo angakule kwambiri mwina kufika pokomoka. Zimenezitu zingadzachititse kuti awononge ndalama zambiri kuchipatala. Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa?

6 N’zoona kuti akulu amafunika kugwira ntchito zambiri mwamsanga. Kupanda kutero zikhoza kubweretsa mavuto aakulu mumpingo. Mofanana ndi makolo amene amakhala ndi ntchito zina zofunika, akulu amafunikanso ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’ (Afil. 1:10) Komabe akulu ena amatanganidwa ndi ntchito zofunika pampingo n’kufika posiya kuphunzitsa ena. Choncho zili ngati akupereka panado kwa mwana amene wadwala malungo n’cholinga choti agwire ntchito zina. Ngati izi zitachitika, ndiye kuti mpingowo m’tsogolo udzasowa akulu amene angayenerere kugwira ntchito zina.

7. Kodi tiyenera kuwaona bwanji akulu amene amayesetsa kuphunzitsa ena?

7 Izitu zikusonyeza kuti sitiyenera kuona mopepuka udindo wophunzitsa ena. Akulu amene amaphunzitsa ena kuti ayenerere maudindo ndi anzeru ndipo amaganizira zam’tsogolo. Zimene amachita zimathandiza kwambiri abale ndi alongo mumpingo. (Werengani 1 Petulo 4:10.) N’chifukwa chiyani tikunena choncho?

MUZIGANIZIRA ZAM’TSOGOLO

8. (a) Kodi akulu ayenera kuphunzitsa ena pa zifukwa ziti? (b) Kodi akulu amene akutumikira kudera limene kulibe ofalitsa ambiri ayenera kuchita chiyani? (Onani bokosi lakuti “ Ntchito Yofunika Kwambiri.”)

8 Akulu, ngakhale atakhala aluso kwambiri, ayenera kukhala odzichepetsa n’kumakumbukira kuti akadzakalamba sadzakwanitsa kuchita zinthu zina bwinobwino. (Mika 6:8) Ayenera kudziwanso kuti mavuto ogwa “mwadzidzidzi” angawalepheretse kuchita zinthu zina mumpingo. (Mlal. 9:11, 12; Yak. 4:13, 14) Choncho akulu amene amaganizira nkhosa amaphunzitsa anthu ena zinthu zimene iwo aphunzira kwa zaka zambiri.—Werengani Salimo 71:17, 18.

9. Kodi kuphunzitsa anthu ena kudzathandiza kwambiri pa nthawi iti?

9 Kodi akulu amene amaphunzitsa ena amathandizanso bwanji mpingo? Iwo amathandiza kuti mpingo ukhale wotetezeka. Kodi tikutanthauza chiyani pamenepa? Anthu ena akaphunzitsidwa ndiye kuti padzakhala abale ambiri othandiza kuti mpingo ukhale wolimba ndiponso wogwirizana panopa komanso makamaka pa chisautso chachikulu. (Ezek. 38:10-12; Mika 5:5, 6) Choncho ngati ndinu mkulu, tikukupemphani kuti muyambe panopa kuphunzitsa anthu ena mumpingo.

10. Kodi akulu ayenera kuchita chiyani kuti apeze nthawi yophunzitsa ena?

10 Tikudziwa kuti mumatopa chifukwa cha ntchito zina zofunika kwambiri mumpingo. Koma tikukupemphani kuti pa nthawi imene mumatanganidwayo muzipatulapo ina kuti muphunzitse ena. (Mlal. 3:1) Mukatero mudzasonyeza kuti mukuona zam’tsogolo.

CHOYAMBA, MUZIWATHANDIZA KUKHALA OMASUKA

11. (a) Kodi malangizo ofanana amene akulu ochokera madera osiyanasiyana ananena akusonyeza chiyani? (b) Malinga ndi Miyambo 15:22, kodi kukambirana zimene akuluwa ananena kungatithandize bwanji?

11 Chaposachedwapa, akulu ena amene amayesetsa kuphunzitsa abale kuti ayenerere maudindo mumpingo, anafunsidwa kuti afotokoze zimene amachita. * Ngakhale kuti akuluwa amakhala m’madera osiyanasiyana, malangizo amene ananena ndi ofanana. Izi zikusonyeza kuti kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo n’kothandiza ‘kulikonse ndiponso mumpingo uliwonse.’ (1 Akor. 4:17) Choncho mu nkhaniyi ndiponso yotsatira tikambirana malangizo amene akuluwa anapereka. (Miy. 15:22) Kuti nkhaniyi ikhale yosavuta kumva, akulu tiziwatchula kuti “aphunzitsi” ndipo amene akuwathandiza tiziwatchula kuti “ophunzira.”

12. Kodi mphunzitsi ayenera kuchita chiyani kuti athandize ophunzira?

12 Mphunzitsi amafunika kukhala womasuka kuti athandize ophunzira. Zimenezi n’zofanana ndi zimene mlimi amachita. Iye asanafese mbewu amakonza kaye munda wake. Choncho mphunzitsi ayenera kukonzekeretsa ophunzira ake kuti aphunzire zinthu zatsopano. Kodi mphunzitsi angachite chiyani kuti akonzekeretse ophunzira ake kuphunzira zinthu zatsopano? Chitsanzo cha mneneri Samueli chingathandize pa nkhaniyi.

13-15. (a) Kodi Samueli anapatsidwa ntchito yotani? (b) Kodi Samueli anagwira bwanji ntchito yake? (Onani chithunzi patsamba 3.) (c) N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuganizira bwino nkhaniyi?

13 Tsiku lina zaka zoposa 3,000 zapitazo, Yehova anauza Samueli kuti: “Mawa nthawi ngati ino ndikutumizira munthu kuchokera kudera la Benjamini, ndipo udzam’dzoze kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.” (1 Sam. 9:15, 16) Samueli anazindikira kuti udindo wake monga mtsogoleri wafika kumapeto ndipo Yehova akufuna kuti iye adzoze munthu wina wolowa m’malo mwake. Mwina Samueli ankadzifunsa kuti: ‘Kodi munthu ameneyo ndimuphunzitsa bwanji ntchito yakeyo?’ Koma kenako anadziwa zochita.

14 Tsiku lotsatira Samueli anaona Sauli ndipo Yehova anamuuza kuti: “Ameneyu ndiye munthu ndimakuuza uja.” Ndiyeno Samueli anaitana Sauli kuti akadye naye chakudya kumalo okwezeka. Atafika m’chipinda chodyera, Samueli anakonzera Sauli ndiponso mtumiki wake malo apamwamba n’kuwapatsa chakudya chabwino kwambiri. Ndipo Samueli anati: “Tenga, udye chifukwa anasungira iweyo kuti udzaidye pa nthawi ino.” Kenako ananyamuka kupita kunyumba ya Samueli ndipo popita ankacheza. Samueli anachita zonsezi pofuna kuti amasukirane ndi Sauli. Atafika kunyumbako, anapita padenga la nyumba ndipo Samueli “anapitiriza kulankhula ndi Sauli.” Ankachita zimenezi uku akupitidwa kamphepo kayeziyezi kenako anapita kukagona. Ndiyeno tsiku lotsatira Samueli anadzoza Sauli, kumupsompsona ndipo anam’patsa malangizo ena. Kenako Sauli ananyamuka ali wokonzeka kukhala mtsogoleri.—1 Sam. 9:17-27; 10:1.

15 N’zoona kuti kudzoza munthu kuti akhale mfumu n’kosiyana ndi kuthandiza abale kuti akhale atumiki othandiza kapena akulu mumpingo. Komabe akulu masiku ano angaphunzire zambiri pa zimene Samueli anachita. Tiyeni tikambirane zinthu ziwiri.

KHALANI APHUNZITSI KOMANSO ANZAWO

16. (a) Kodi Samueli anamva bwanji Aisiraeli atanena kuti akufuna mfumu? (b) Kodi Samueli anatani pamene Yehova anamuuza kuti adzoze Sauli?

16 Muzikhala ndi mtima wofuna kuphunzitsa. Poyamba, Samueli atamva zoti Aisiraeli akufuna mfumu, anakhumudwa ndipo ankaona kuti anthuwo asiya kumukonda. (1 Sam. 8:4-8) Iye sankafuna kuchita zimene anthu ananenazo. Ndiyeno Yehova anamuuza katatu kuti amvere zimene anthuwo akunena. (1 Sam. 8:7, 9, 22) Ngakhale zinali choncho, Samueli sankachitira nsanje munthu womulowa m’maloyo. Yehova atamuuza kuti adzoze Sauli, iye anachita zimenezi ndi mtima wonse osati monyinyirika.

17. (a) Kodi akulu angatsanzire bwanji Samueli? (b) Kodi chimachitika n’chiyani ngati akulu aphunzitsa bwino anthu ena?

17 Masiku anonso, akulu ayenera kukhala ndi mtima wofuna kuphunzitsa anthu. (1 Pet. 5:2) Sayenera kuopa kuphunzitsa ena poganiza kuti awalanda udindo. Aphunzitsi abwino amaona kuti anthu amene akuwaphunzitsa ndi antchito anzawo osati anthu amene akupikisana nawo. (2 Akor. 1:24) Iwo amadziwa kuti anthuwo ndi mphatso zamtengo wapatali mumpingo. (Aheb. 13:16) Kunena zoona aphunzitsi abwinowa amasangalala akaona anthu amene awaphunzitsa akuthandiza kwambiri mumpingo.—Mac. 20:35.

18, 19. (a) Kodi mkulu angathandize bwanji munthu amene akumuphunzitsa kuti amasuke? (b) Kodi kuchita zimenezi n’kothandiza bwanji?

18 Muzipeza mpata wocheza nawo. Kodi mukukumbukira zimene Samueli anachita atakumana ndi Sauli? Iye sanangotenga botolo la mafuta mwamsangamsanga n’kuthira pamutu pa Sauli kenako n’kumuuza kuti azipita. Akanatero sizikanayenda bwino chifukwa akanamudzidzimutsa. Samueli anachita zinthu mokoma mtima komanso mwapang’onopang’ono. Anapita naye kukadya, kenako kuyenda naye ndipo pambuyo poti apuma anamudzoza kukhala mfumu.

Muzipeza mpata wocheza ndi anthu amene mukufuna kuwaphunzitsa (Onani ndime 18 ndi 19)

19 Izi n’zimene mphunzitsi ayenera kuchita. Choyamba ayenera kupeza mpata wocheza ndi wophunzirayo n’cholinga choti amasuke. Zimene mkulu angachite kuti amasukirane ndi munthu zingakhale zosiyana malinga ndi kumene akukhala komanso chikhalidwe chawo. Koma kaya zili bwanji kwanuko, mkulu amene amatanganidwa ayenera kupeza nthawi yocheza ndi anthu amene akufuna kuwaphunzitsa. Akatero zimakhala ngati akuwauza kuti “Ndimaona kuti ndiwe munthu wofunika kwambiri.” (Werengani Aroma 12:10.) Zimenezi zingathandize kwambiri anthu amene mukuwaphunzitsawo ndipo sadzaiwala.

20, 21. (a) Kodi mphunzitsi wabwino amatani? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

20 Mfundo imene akulu ayenera kuikumbukira ndi yakuti: Mphunzitsi wabwino amakonda kuphunzitsa komanso amakonda anthu amene akuwaphunzitsawo. (Yerekezerani ndi Yohane 5:20.) Ophunzira amadziwa ngati mphunzitsi wawo amawakonda kapena ayi ndipo ngati aona kuti amawakonda amaphunzira mosavuta. Choncho ngati ndinu mkulu, chonde yesetsani kupeza mpata wocheza ndi anthu kuti muwaphunzitse bwino.—Miy. 17:17; Yoh. 15:15.

21 Munthu amene mukufuna kumuphunzitsayo akamasuka muyenera kuyamba kumuthandiza. M’nkhani yotsatira tidzakambirana njira zimene mungagwiritse ntchito pophunzitsa anthu.

^ ndime 3 Nkhaniyi ndiponso yotsatira kwenikweni alembera akulu koma aliyense mumpingo ayenera kuganizira bwino mfundo zake. Tikutero chifukwa chakuti nkhanizi zilimbikitsa m’bale aliyense wobatizidwa kuti aphunzitsidwe n’cholinga choti athandize pa ntchito za mumpingo. Zikatero, aliyense mumpingo adzapindula kwambiri.

^ ndime 11 Akulu amene anafunsidwa ndi a ku Australia, Bangladesh, Belgium, Brazil, France, French Guiana, Japan, Korea, Mexico, Namibia, Nigeria, Réunion, Russia, South Africa ndi ku United States.