Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yehova Ndi Mnzanu Weniweni?

Kodi Yehova Ndi Mnzanu Weniweni?

“Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—YAK. 4:8.

1. N’chifukwa chiyani tiyenera kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova?

KODI munadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa? Ngati ndi choncho ndiye kuti muli pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Ubwenziwu ndi chinthu cha mtengo wapatali zedi. Koma ukhoza kusokonekera chifukwa choti tili m’dziko la Satana ndipo ndife ochimwa. Zimenezi zimakhudza mtumiki wa Mulungu wina aliyense. Choncho tiyenera kuyesetsa kuti ubwenzi wathu ndi Yehova uzikhala wolimba.

2. Malinga ndi lemba la Yakobo 4:8, kodi tingalimbitse bwanji ubwenzi wathu ndi Yehova?

2 Kodi mungatani kuti Yehova akhale mnzanu weniweni ndipo ubwenzi wanu ukhale wolimba kwambiri? Lemba la Yakobo 4:8, limanena mmene mungachitire zimenezi. Paja limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” Lembali likusonyeza zinthu ziwiri zimene zimachitika. Tikamayesetsa kuyandikira Mulungu nayenso amachita chimodzimodzi. Kuchita zimenezi mobwerezabwereza kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Zotsatira zake n’zakuti Yehova amakhala mnzathu weniweni. Nafenso tingalankhule ngati Yesu amene anati: “Alipo ndithu amene anandituma . . . Ine ndikumudziwa.” (Yoh. 7:28, 29) Kodi mungachite zotani kuti muyandikire Yehova?

Njira zotithandiza kulankhulana ndi Mulungu (Onani ndime 3)

3. Kodi tingachite zotani kuti tizilankhulana ndi Yehova?

3 Kulankhula ndi Yehova nthawi zonse kumalimbitsa ubwenzi wathu. Kodi tingalankhule naye bwanji? Tikhoza kulankhula naye mmene timachitira ndi mnzathu wapamtima amene amakhala kutali. Mwina nthawi zonse timatumizirana mameseji kapena kulankhula naye pafoni. Koma Yehova tingalankhule naye nthawi zonse popemphera. (Werengani Salimo 142:2.) Yehova amalankhula nafe nthawi zonse tikamawerenga mawu ake ndiponso kuwaganizira mozama. (Werengani Yesaya 30:20, 21.) Tsopano tiyeni tikambirane zinthu ziwiri zimene zimatithandiza kuti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Yehova.

TIZIPHUNZIRA MAWU A YEHOVA NTHAWI ZONSE

4, 5. Kodi Yehova amalankhula bwanji ndi munthu aliyense payekha? Perekani chitsanzo.

4 M’Baibulo muli uthenga umene Yehova walembera anthu onse. Koma kodi Baibulo limasonyeza zimene munthu aliyense payekha angachite kuti ayandikire Yehova? Inde. Tikutero chifukwa chakuti munthu akamaphunzira Baibulo n’kumatsatira zimene likunena zimakhala ngati Yehova akumulankhula. Izi zimathandiza kuti ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova ulimbe.—Aheb. 4:12; Yak. 1:23-25.

5 Tiyerekeze kuti munthu wawerenga mawu a Yesu akuti: “Lekani kudziunjikira chuma padziko lapansi.” Ngati munthuyo amatsatiradi mfundoyi n’kumaika patsogolo zinthu zokhudza Ufumu amadziwa kuti akusangalatsa Yehova. Koma ngati akuona kuti ali ndi vuto pa nkhaniyi, amadziwa kuti Yehova wamuuza zinthu zimene ayenera kusintha n’cholinga choti akhale naye pa ubwenzi wabwino.—Mat. 6:19, 20.

6, 7. (a) Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamaphunzira Mawu a Mulungu? (b) Kodi cholinga chathu tikamaphunzira Baibulo chiyenera kukhala chiyani?

6 Koma sikuti munthu akamaphunzira Malemba amangoona zimene ayenera kusintha. Kuphunzirako kumathandizanso munthuyo kumvetsa makhalidwe abwino a Yehova n’kuyamba kumukonda kwambiri. Ndiyeno munthuyo akayamba kukonda kwambiri Yehova, Yehovayo amayambanso kumukonda kwambiri. Zikatere Yehova amakhala mnzake weniweni.—Werengani 1 Akorinto 8:3.

7 Koma kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ulimbe, tiyenera kuwerenga Mawu ake ndi zolinga zoyenera. Lemba la Yohane 17:3 limati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” Choncho tiyenera kuphunzira osati kuti tingodziwa zinthu koma kuti tidziwe bwino Yehova n’kumamukonda.—Werengani Ekisodo 33:13; Sal. 25:4.

8. (a) N’chifukwa chiyani ena angade nkhawa akamva zimene Yehova anachitira Azariya pa 2 Mafumu 15:1-5? (b) Kodi kudziwa bwino Yehova kungatithandize bwanji kuti tisamamukayikire?

8 Munthu akayamba kukonda kwambiri Yehova sadandaula ngati sakumvetsa nkhani zina za m’Malemba. Mwachitsanzo, kodi mumamva bwanji mukaganizira zimene Yehova anachitira mfumu ya Yuda dzina lake Azariya. (2 Maf. 15:1-5) Baibulo limati “Azariya anapitiriza kuchita zolungama pamaso pa Yehova” ngakhale kuti ‘anthu anali kufukizabe ndi kupereka nsembe yautsi m’malo okwezeka.’ Koma “Yehova anaichititsa khate mfumuyo moti inakhalabe yakhate mpaka tsiku limene inamwalira.” Baibulo silinena chifukwa chake Yehova anachita zimenezi. Kodi nkhaniyi iyenera kutidetsa nkhawa n’kumaona kuti Yehova analanga Azariya popanda chifukwa? Ngati timadziwa bwino mmene Yehova amachitira zinthu, sitingade nazo nkhawa. Tikutero chifukwa chakuti tidzakumbukira mfundo yoti nthawi zonse Yehova amalanga anthu “pa mlingo woyenera.” (Yer. 30:11) Choncho ngakhale kuti sitidziwa zimene zinachititsa Yehova kulanga Azariya, timakhulupirira kuti zimene anachitazo zinali zachilungamo.

9. Fotokozani nkhani imene ingatithandize kumvetsa chimene chinachititsa Yehova kulanga Azariya.

9 M’Baibulo muli mfundo zina zimene zingatithandize kumvetsa nkhaniyi. Mfumu Azariya ankatchedwanso Mfumu Uziya. (2 Maf. 15:7, 32) Ndiyeno pa 2 Mbiri 26:3-5, komanso vesi 16 mpaka 21, timawerenga kuti Uziya ankachita zolungama pamaso pa Yehova koma “atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa.” Iye sanali wansembe koma anasonyeza kukula mtima n’kuyamba kugwira ntchito ya ansembe. Ansembe 81 anamudzudzula koma iye anachita makani mpaka ‘anakwiyira kwambiri’ ansembewo. Izi zinachititsa kuti Yehova amulange pomuchititsa khate.

10. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuda nkhawa ngati sitikumvetsa zinthu zina zimene Yehova wachita? (b) Kodi tingatani kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova?

10 Koma kodi tiyenera kuda nkhawa ngati sitikumvetsa nkhani ina ndipo m’Baibulo mulibe mfundo zina zotithandiza kumvetsa? Kodi zikatero tiyenera kukayikira zoti Mulungu amachita zinthu mwachilungamo? Sitiyenera kuda nkhawa chifukwa chakuti mfundo zimene zili m’Baibulo n’zokwanira kutithandiza kudziwa kuti Yehova ndi wolungama ndiponso woyenera kutiuza kuti izi n’zabwino izi n’zoipa. (Deut. 32:4) Kudziwa bwino Yehova kungatithandize kumukhulupirira kwambiri moti sitingade nkhawa ngati sanatiuze zifukwa zimene amachitira zinthu zina. Koma kuti munthu afike pomukhulupirira chonchi ayenera kuchita khama kwambiri pophunzira Mawu a Mulungu ndiponso kuwaganizira mozama. (Sal. 77:12, 13) Zikatero, ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova umalimba kwambiri.

TIZIPEMPHERA NTHAWI ZONSE

11-13. Kodi mumadziwa bwanji kuti Yehova amamva mukamapemphera? (Onani chithunzi patsamba 19.)

11 Pemphero limatithandiza kuyandikira Yehova. Tikamapemphera tikhoza kutamanda Yehova, kumuthokoza ndiponso kumupempha kuti azititsogolera. (Sal. 32:8) Kuti Yehova akhale mnzanu weniweni, muyenera kutsimikizira kuti amamva mukamapemphera.

12 Anthu ena amanena kuti pemphero limangothandiza kuti maganizo akhale m’malo. Ndipo iwo amati tisamaganize kuti mapemphero amayankhidwa ayi koma kungoti munthu akatchula zimene zili mumtima mwake, amazindikira mavuto ake n’kupeza njira yowathetsera. Ngakhale anthu amanena zimenezi, kodi inuyo mumadziwa bwanji kuti Yehova amayankha mapemphero?

13 Kuti timvetse zimenezi, tiyeni tiganizire za Yesu. Iye ali kumwamba ankaona Yehova akuyankha mapemphero a atumiki ake padziko lapansi. N’zosadabwitsa kuti Yesuyo ali padziko lapansi ankapemphera kwa Atate wake n’kumawauza za mumtima mwake. Tsiku lina anachezera usiku wonse akupemphera. Kodi iye akanachita izi zikanakhala kuti Yehova samvetsera munthu akamapemphera? (Luka 6:12; 22:40-46) Kodi iye akanalimbikitsa ophunzira ake kuti azipemphera? Yesu ankadziwa kuti pemphero limathandiza kuti anthu azilankhulana ndi Yehova. Pa nthawi ina akupemphera, Yesu anati: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse.” Nafenso tikhoza kukhala ndi chikhulupiriro chakuti Yehova ndi “wakumva pemphero.”—Yoh. 11:41, 42; Sal. 65:2.

14, 15. (a) Kodi chimachitika n’chiyani tikamauza Yehova zonse za mumtima mwathu? (b) Kodi pemphero linathandiza bwanji mlongo wina?

14 Mukamamuuza Yehova zonse zimene zili mumtima mwanu, simudzavutika kudziwa kuti wakuyankhani. Mapemphero anu akamayankhidwa, m’pamene Yehova amakhala mnzanu weniweni. Choncho kuti muyandikire kwambiri Yehova, muyenera kumuuza zonse za mumtima mwanu.

15 Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina dzina lake Kathy. * Ngakhale kuti ankalalikira nthawi zonse, utumikiwo sunkamusangalatsa. Iye anati: “Kunena zoona kulalikira sikunkandisangalatsa. Nditapuma pa ntchito, mkulu wina anandiuza kuti ndiyambe upainiya ndipo anandipatsa fomu kuti ndisaine. Ndinaganizadi zoyamba upainiyawo ndipo ndinkapempha Yehova tsiku lililonse kuti andithandize kukonda ntchito yolalikira.” Kodi Yehova anamuyankhadi mlongoyu? Iye anapitiriza kunena kuti: “Chaka chino n’chachitatu ndikuchita upainiya. Popeza ndimalalikira nthawi yaitali pamodzi ndi alongo ena, zandithandiza kuti ndiziphunzitsa mwaluso. Panopa ndimakonda kwambiri kulalikira komanso ubwenzi wanga ndi Yehova walimba kwambiri kuposa kale.” Apa n’zoonekeratu kuti mlongoyu ubwenzi wake ndi Yehova unalimba chifukwa cha pemphero.

TIZIYESETSA KUCHITA MBALI YATHU

16, 17. (a) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ubwenzi wathu ndi Yehova uzilimba? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

16 Tiyenera kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova kwa moyo wathu wonse. Ngati tikufuna kuti Yehova atiyandikire, tiyenera kuyamba ifeyo. Choncho tiyeni tiziyesetsa kulankhulana ndi Yehova powerenga Mawu ake komanso popemphera nthawi zonse. Tikatero ubwenzi wathu ndi Yehova udzalimba kwambiri ndipo tidzatha kupirira vuto lililonse limene tingakumane nalo.

Tiyenera kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova kwa moyo wathu wonse (Onani ndime 16 ndi 17)

17 Koma mavuto ena satha ngakhale kuti tawapempherera kwa nthawi yaitali. Izi zikachitika chikhulupiriro chathu chikhoza kuyamba kuchepa. Tikhoza kuyamba kukayikira zoti Yehova amamva mapemphero athu komanso zoti tili naye pa ubwenzi wabwino. M’nkhani yotsatira tidzakambirana zimene tingachite kuti tisamakayikire zoti Yehova ndi mnzathu weniweni ngakhale pamene tikuona kuti mavuto athu sakutha.

^ ndime 15 Dzina lasinthidwa.