Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchotsa Anthu Osalapa Kumathandiza

Kuchotsa Anthu Osalapa Kumathandiza

M’BALE wina dzina lake Julian anati: “Nditangomva chilengezo choti mwana wanga wachotsedwa, ndinkangomva ngati dziko latha basi. Anali mwana wanga woyamba ndipo tinkakondana kwambiri. Tinkachitira limodzi zinthu zambiri. Anali mwana wabwino kwambiri koma kenako anayamba kuchita zosayenera. Mkazi wanga ankangokhalira kulira ndipo sindinkatha kumutonthoza. Tinkaona kuti talephera kumulera bwino.”

Kunena zoona, mnzathu akachotsedwa zimatipweteka kwambiri. Ndiyeno n’chifukwa chiyani tikunena kuti kuchotsa anthu osalapa kumathandiza? Kodi ndi zifukwa ziwiri ziti za m’Malemba zimene zimachititsa kuti munthu achotsedwe?

ZIFUKWA ZIWIRI ZIMENE ZIMACHITITSA KUTI MUNTHU ACHOTSEDWE

Kuti munthu wobatizidwa achotsedwe, choyamba amakhala kuti wachita tchimo lalikulu. Chachiwiri amakhala kuti sakulapa tchimo lakelo.

Ngakhale kuti Yehova sayembekeza kuti tikhale angwiro, iye amafuna kuti tiziyesetsa kutsatira malamulo ake. Mwachitsanzo, Yehova amafuna kuti tizipewa machimo aakulu monga dama, kulambira mafano, kuba, kulanda, kupha munthu ndiponso kuchita zamizimu.—1 Akor. 6:9, 10; Chiv. 21:8.

Yehova amapereka malamulo onsewa n’cholinga chotiteteza. Kodi alipo amene safuna kukhala ndi anthu amakhalidwe abwino omwe tingawadalire? Timakhala bwino ndi abale ndi alongo athu chifukwa cha zimene tinalonjeza nthawi yomwe tinkabatizidwa. Paja tinalonjeza kuti tidzatsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu.

Nanga bwanji ngati Mkhristu wobatizidwa wachita tchimo lalikulu chifukwa chofooka? Kumbukirani kuti atumiki a Yehova akale anachitaponso machimo aakulu komabe Mulungu sanawasiye. Mwachitsanzo, Davide atachita chigololo ndiponso kupha munthu, mneneri Natani anamuuza kuti: “Yehova wakukhululukira tchimo lako.”—2 Sam. 12:13.

Mulungu anakhululukira Davide chifukwa chakuti analapa ndi mtima wonse. (Sal. 32:1-5) Masiku anonso munthu amachotsedwa ngati sakulapa kapena akupitirizabe kuchita zoipa. (Mac. 3:19; 26:20) Ngati munthu sakuonetsa kulapa kwenikweni, akulu amene ali pa komiti yachiweruzo amamuchotsa.

Ngati ndife achibale a munthu wochotsedwayo, mwina tingaone kuti m’bale wathuyo wapatsidwa chilango chokhwima kwambiri. Komabe Baibulo limasonyeza kuti kuchotsa munthu kumathandiza.

KODI KUCHOTSA MUNTHU WOSALAPA KUMATHANDIZA BWANJI?

Yesu ananena kuti “nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mat. 11:19) Munthu wosalapa akachotsedwa, zotsatira zake zimakhala zabwino. Tiyeni tikambirane mfundo zitatu izi:

Dzina la Yehova limalemekezedwa. Akhristufe timadziwika ndi dzina la Mulungu choncho zimene timachita zimakhudza dzina lakelo. (Yes. 43:10) Anthu amatha kulemekeza makolo kapena kuwanyoza chifukwa cha zochita za mwana wawo. N’chimodzimodzi ndi ifeyo. Zochita zathu zingachititse kuti anthu alemekeze Yehova kapena amunyoze. Dzina la Mulungu limalemekezedwa kwambiri ngati anthu amene akudziwika ndi dzinalo ali ndi khalidwe labwino. Ndi mmene zinalilinso m’nthawi ya Ezekieli. Zochita za Ayuda zinkakhudza dzina la Mulungu.—Ezek. 36:19-23.

Munthu akachita chiwerewere amadetsa dzina la Mulungu. Paja mtumwi Petulo anauza Akhristu kuti: “Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. Koma khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse, chifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.’” (1 Pet. 1:14-16) Kunena zoona, khalidwe labwino limalemekeza dzina la Mulungu.

M’bale kapena Mlongo akachita tchimo, anthu ena amadziwa. Ndiyeno akachotsedwa, zimasonyeza kuti anthu a Yehova ndi oyera ndipo amatsatira mfundo za m’Malemba kuti asadetsedwe. Chitsanzo ndi zimene zinachitika ku Nyumba ya Ufumu ya ku Switzerland. Munthu wina anangofika n’kunena kuti akufuna kukhala wa Mboni za Yehova. Mchemwali wake anali atachotsedwa chifukwa cha chiwerewere. Ndiyeno munthuyo anati akufuna kukhala m’gulu “limene sililekerera makhalidwe oipa.”

Mpingo umatetezedwa ndiponso kuyeretsedwa. Mtumwi Paulo anachenjeza Akorinto kuti sayenera kulekerera anthu osalapa mumpingo. Iye anasonyeza kuti anthu osalapawo akhoza kusokoneza mpingo wonse ndipo anati: “Kodi simukudziwa kuti chofufumitsa chaching’ono chimafufumitsa mtanda wonse?” Kenako ananena kuti: “M’chotseni pakati panu munthu woipayo.”—1 Akor. 5:6, 11-13.

N’kutheka kuti ‘munthu woipa’ amene ankamunenayo ankachita chiwerewere ndipo sankalapa. Mwina anthu ena mumpingo ankaona kuti zimene akuchitazo zilibe vuto lililonse. (1 Akor. 5:1, 2) Koma kulekereraku kukanachititsa kuti Akhristu ena ayambe kutengera khalidwe lachiwerewere limene linali lofala mumzindawo. Kulekerera anthu osalapa kumachititsa kuti anthu asiye kutsatira mfundo zimene Mulungu amatipatsa. (Mlal. 8:11) Vuto lina ndi lakuti anthu ochimwa amene sakulapa amakhala ngati “miyala ikuluikulu yobisika m’madzi” imene imaswa chikhulupiriro cha anthu ena mumpingo.—Yuda 4, 12.

Wolakwayo amatha kusintha maganizo. Yesu anapereka fanizo la mwana amene anachoka pakhomo n’kukayamba khalidwe loipa limene linamuwonongetsa chuma chake chonse. Koma kenako anazindikira kuti kumene anapitako zinthu zinamusokonekera ndipo ankazunzika. Ndiyeno maganizo atamubwerera, analapa n’kubwerera kunyumba kwawo. (Luka 15:11-24) Yesu ananena kuti bambo ake anasangalala kwambiri ataona kuti mwanayo wabwerera. Apatu anasonyeza kuti Yehova amasangalalanso anthu ochimwa akabwerera. Paja Yehova amatiuza kuti: “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa, koma ndimafuna kuti munthu woipa abwerere kusiya njira zake n’kukhala ndi moyo.”—Ezek. 33:11.

Zimene zimachitika munthu akachotsedwa zimafanana ndi zimene zinachitika mu fanizo la Yesu. Wochotsedwayo amakhala ngati wachoka m’banja lake ndipo amazindikira kuti zinthu zamusokonekera. Akakumana ndi mavuto aakulu, amakumbukira mmene ankasangalalira pamene anali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Zimenezi zingachititse kuti asinthe maganizo.

Koma kuti izi zitheke pamafunika chikondi komanso kulimba mtima. Paja Davide ananena kuti: “Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima kosatha, ndipo akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga.” (Sal. 141:5) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi munthu amene watsamwidwa ndi chakudya. Anthu akafuna kumuthandiza kuti chakudyacho chichoke amamumenya kumsana. Kupanda kutero akhoza kukomoka kapena kufa. Womenyedwayo amamva kupweteka koma zimamuthandiza. Izi zikufanana ndi zimene Davide ankatanthauza pamene ananena kuti munthu wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza kukoma mtima.

Munthu wosalapa akachotsedwa amakhala kuti walandira chilango choyenera. Mwana wa Julian amene tamutchula kumayambiriro uja anasintha maganizo pambuyo pa zaka 10 ndipo anabwerera mumpingo. Panopa akutumikira monga mkulu. Iye ananena kuti: “Munthune ndinayeneradi kuchotsedwa ndipo zitachitika ndinazindikira kuipa kwa zimene ndinkachita.”—Aheb. 12:7-11.

KODI TINGATHANDIZE BWANJI ANTHU OCHOTSEDWA?

Kunena zoona kuchotsedwa kumakhala kopweteka kwambiri. Ngakhale zili choncho, tonse tingathandize kuti cholinga chimene amuchotsera chikwaniritsidwe.

Akulu amathandiza ochotsedwa kuti abwerere kwa Yehova

Akulu amene ali pa komiti yachiweruzo amayesetsa kusonyeza chikondi cha Yehova. Akamamuuza kuti wachotsedwa, iwo amamufotokozera mwachikondi zimene angachite kuti adzabwezeretsedwe. Kamodzi pachaka, akulu amapeza mpata wokaona anthu ochotsedwa amene akusonyeza kuti akufuna kukonza ubwenzi wawo ndi Yehova. Iwo amafuna kuwakumbutsa zomwe angachite kuti abwerere kwa Yehova. *

Achibale angasonyeze kuti amakonda abale ndi alongo mumpingo ndiponso wochotsedwayo pothandiza kukwaniritsa cholinga chimene amuchotsera. M’bale Julian tamutchula kumayambiriro uja anati: “N’zoona kuti ndi mwana wanga koma zochita zake n’zimene zinatisiyanitsa.”

Mpingo wonse ungasonyeze kuti umakonda munthu wochotsedwayo popewa kucheza naye. (1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10, 11) Akamachita zimenezi amasonyeza kulemekeza chilango chimene Yehova wapereka kudzera mwa akulu. Koma ayenera kupeza mpata wolimbikitsa abale ake a wochotsedwayo. Izi zingawathandize kuona kuti abale ndi alongo amawakondabe.—Aroma 12:13, 15.

M’bale Julian anamaliza ndi mawu akuti: “Kuchotsa munthu wosalapa kumathandiza kuti tizitsatira malangizo a Yehova. Munthu akachotsedwa zimapweteka, koma zotsatira zake n’zothandiza. Kunena zoona mwana wanga sakanabwerera zikanakhala kuti ndinalekerera makhalidwe ake oipa.”

^ ndime 24 Onani Nsanja ya Olonda ya April 15, 1991, tsamba 21 mpaka 23.