Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chipembedzo Chasanduka Bizinezi Yotentha?

Kodi Chipembedzo Chasanduka Bizinezi Yotentha?

 Kodi mwaona kuti cholinga chachikulu cha atsogoleri azipembedzo zambiri ndi kupeza ndalama m’malo mothandiza anthu kuti azilambira Mulungu? Iwo amagulitsa zinthu zosiyanasiyana komanso amalipiritsa anthu kuti awathandize m’njira zosiyanasiyana. Atsogoleri ambiri amalandira ndalama zambiri komanso amakhala moyo wofewa. Zitsanzo zina ndi izi:

  •   Kafukufuku wina anasonyeza kuti pa zaka 13, bishopu wina wa Chikatolika ankagwiritsa ntchito ndalama za tchalitchi polipira maulendo 150 pandege zapamwamba komanso maulendo 200 pamagalimoto apamwamba. Anawononganso ndalama zokwana madola 4 miliyoni a ku United States pokonza nyumba yake yapamalo a tchalitchi.

  •   M’busa wina wa ku Africa amapanga misonkhano yachipembedzo yomwe anthu masauzande ambiri amapezeka. Kutchalitchi chake amagulitsa zinthu zosiyanasiyana monga mafuta amene amati amachiritsa komanso mataulo ndi matisheti okhala ndi chithunzi chake. Anthu ambiri amene amapezeka pamisonkhano yake ndi osauka, pomwe iye ndi wolemera kwambiri.

  •   Kumapiri awiri opatulika a chipembedzo cha Chibuda kumakhalanso makampani. Komanso kukachisi wotchuka kwambiri wotchedwa Shaolin, kuli mabizinezi osiyanasiyana ndipo mtsogoleri wa kachisiyo amadziwika kuti ndi bwana wa mabizineziwo.

  •   Masiku ano, kumakampani ena a ku United States kuli anthu amene amagwira ntchito yothandiza ena pa nkhani zachipembedzo. Lipoti lina linanena kuti anthuwa amakonzera makasitomala awo miyambo yachipembedzo ndi zina zotere.

 Kodi mumaona bwanji zipembedzo zimene zimapanganso mabizinezi? Kodi mukuganiza kuti Mulungu amaona bwanji anthu amene amafuna kupeza phindu pochita zinthu zachipembedzo?

Kodi Mulungu amaona bwanji zipembedzo zimene zimapanganso mabizinezi?

 Mulungu sasangalala ndi zimenezi. Baibulo limasonyeza kuti m’mbuyomu, iye anadandaula kwambiri chifukwa ansembe, omwe ankati ankamuimira, ‘ankaphunzitsa kuti apeze malipiro.’ (Mika 3:11) Mulungu anadzudzula anthu adyera omwe ankapanga malonda n’kuchititsa kuti malo ake olambirira akhale “phanga la achifwamba.”​—Yeremiya 7:11.

 Nayenso Yesu Khristu ankanyansidwa ndi anthu amene ankagwiritsa ntchito chipembedzo kuti azipeza phindu. Pamene anali padzikoli, atsogoleri achipembedzo ankapeza phindu kwa amalonda adyera omwe atsogoleriwo ankawalola kuti azipanga malonda m’kachisi ku Yerusalemu. Iwo ankadyera masuku pamutu anthu amitima yabwino omwe ankabwera kudzalambira Mulungu. Yesu anathamangitsa molimba mtima amalonda achinyengowo kukachisi powauza kuti: “Mulekeretu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!”​—Yohane 2:14-16.

 Yesu anatsatiranso maganizo a Mulungu pochita zinthu pa utumiki wake. (Yohane 8:28, 29) Mwachitsanzo, sankalipiritsa anthu kuti awaphunzitse za Mulungu. Sankafunanso ndalama kuti azichita zozizwitsa monga kudyetsa anjala, kuchiritsa odwala komanso kuukitsa akufa. Yesu sankagwiritsa ntchito utumiki wake kuti azipeza chuma. Paja analibe ngakhale nyumba.​—Luka 9:58.

Kodi Akhristu oyambirira ankachita bwanji kuti kulambira kwawo kusakhudzane ndi kupeza ndalama?

 Yesu anauza otsatira ake kuti asamapeze ndalama pothandiza anthu kuti alambire Mulungu. Iye anati: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Otsatira oyambirirawo, amene anakhala Akhristu, anatsatira malangizo a Yesuwa. Zitsanzo pa nkhaniyi ndi izi:

  •   Mtumwi Petulo, yemwe ankayenda ndi Yesu pa utumiki wake, anakumana ndi Simoni yemwe ankafuna kumupatsa ndalama kuti apeze udindo ndi mphamvu. Nthawi yomweyo, Petulo anakana ndalamazo n’kudzudzula Simoni pomuuza kuti: “Siliva wakoyo awonongeke nawe limodzi, chifukwa ukuganiza kuti mphatso yaulere ya Mulungu ungaipeze ndi ndalama.”​—Machitidwe 8:18-20.

  •   Mtumwi Paulo anali Mkhristu wodziwika amene ankayendera mipingo ya Chikhristu. Ngakhale kuti ankagwira ntchito mwakhama pothandiza mipingo yambiri, sanapemphe ngakhale kamodzi kuti apatsidwe ndalama. Iye ndi Akhristu anzake ‘sankachita nawo mawu a Mulungu malonda ngati mmene ambiri ankachitira.’ (2 Akorinto 2:17) M’malomwake, Paulo analemba kuti: “Mwa kugwira ntchito usiku ndi usana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza, tinalalikira uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu.”​—1 Atesalonika 2:9.

 N’zoona kuti Akhristu oyambirirawo ankafunikira ndalama kuti azigwira ntchito zawo zolalikira kumadera osiyanasiyana komanso zothandiza anthu m’njira zina. Koma sankalipiritsa anthu kuti awathandize kulambira Mulungu. Anthu akanatha kupereka ndalama ngati ankafuna mogwirizana ndi malangizo otsatirawa:

  •   2 Akorinto 8:12: “Mphatso yochokera pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwera nayo, chifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apereke zimene angathe, osati zimene sangathe.”

     Mfundo yake: Cholinga cha munthu popereka zinthu n’chofunika kwambiri kuposa kuchuluka kwa zimene wapereka.

  •   2 Akorinto 9:7: “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”

     Mfundo yake: Mulungu safuna kuti munthu akakamizike kupereka. Koma amasangalala munthu akasankha kupereka mwa kufuna kwake.

N’chiyani chidzachitikira zipembedzo zadyera posachedwapa?

 Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti pali zipembedzo kapena njira zolambirira zomwe Mulungu savomereza. (Mateyu 7:21-23) Mu ulosi wina wochititsa chidwi, Baibulo limayerekezera zipembedzo zonyenga ndi hule chifukwa choti zimachita zinthu mogwirizana ndi maboma kuti zizipeza ndalama kapena mapindu ena. Zimadyeranso masuku pamutu anthu am’mayiko osiyanasiyana. (Chivumbulutso 17:1-3; 18:3) Ulosi umenewu umasonyezanso kuti Mulungu adzawononga zipembedzo zonyengazi posachedwapa.​—Chivumbulutso 17:15-17; 18:7.

 Koma asanaziwononge safuna kuti zochita zoipa za zipembedzozi zizipusitsa anthu kapena kuwasiyanitsa ndi iye. (Mateyu 24:11, 12) Iye amauza anthu kuti achoke m’zipembedzo zonyenga ndipo aphunzire zimene angachite kuti azimulambira movomerezeka.​—2 Akorinto 6:16, 17.