Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi

 Kodi mwayamba kudwala mosayembekezereka? Ngati zili choncho, mukudziwa kuti zimenezi zingachititse kuti muzivutika maganizo komanso zingakubweretsereni mavuto azachuma. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupirira? Nanga kodi mungathandize bwanji wachibale kapena mnzanu amene akudwala? Ngakhale kuti Baibulo si buku lofotokoza za mankhwala, muli mfundo zimene zingakuthandizeni kupirira mavuto.

Zinthu zimene zingakuthandizeni ngati mukudwala

  •   Pitani kuchipatala

     Zimene Baibulo limanena: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.”—Mateyu 9:12.

     Mfundo yake: Pitani kuchipatala pakafunika.

     Tayesani izi: Pitani kuchipatala chabwino kwambiri chimene mungakwanitse kupita. Nthawi zina, mungachite bwino kukaona dokotala wina m’malo mongodalira zimene dokotala mmodzi wanena. (Miyambo 14:15) Muzikambirana bwinobwino ndi madokotala n’cholinga choti mumvetse bwino zimene iwo akunena komanso iwo amvetse bwino zizindikiro zanu. (Miyambo 15:22) Adziweni bwino matenda anu komanso mankhwala ake onse.. Mukamvetsetsa zimene zingachitike, mudzakhala wokonzeka mumtima mwanu komanso mudzatha kusankha mwanzeru zinthu zokhudza matenda anu.

  •   Muzichita zimene zingakuthandizeni kukhala wathanzi

     Zimene Baibulo limanena: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”—1 Timoteyo 4:8.

     Mfundo yake: Mukamachita zinthu monga masewera olimbitsa thupi, zingathandize kuti mukhale wathanzi.

     Tayesani izi: Muzichita masewera olimbitsa thupi, kudya chakudya chopatsa thanzi komanso kugona mokwanira. Ngakhale kuti zinthu zasintha pa moyo wanu chifukwa cha matenda anu, akatswiri amanena kuti kupeza nthawi yochita zimene tatchulazi kungakuthandizeni kwambiri. Koma muzisankha kuchita zinthu mogwirizana ndi matenda anu komanso chithandizo chamankhwala chimene mukulandira.

  •   Muzilola anzanu kuti azikuthandizani

    Zimene Baibulo limanena: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi  zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

     Mfundo yake: Anzanu angakuthandizeni kuti mupirire mavuto.

     Tayesani izi: Muzikambirana ndi mnzanu wodalirika amene mumamasuka naye kwambiri. Zimenezi zingakuthandizeni kuti musamadandaule kwambiri chifukwa cha matenda anu. Anzanu komanso achibale angafune kukuthandizani m’njira zambiri koma mwina sakudziwa zimene angachite. Choncho muziwauza zimene angachite. Koma musamayembekezere kuti azichita zambiri ndipo muzithokoza zimene akwanitsa kuchita pokuthandizani. Mwina mungafunikenso kuwauza anzanu nthawi zimene angabwere kudzakuonani komanso kuti ndi nthawi yaitali bwanji imene angacheze nanu. Zimenezi zingathandize kuti musamatope kwambiri.

  •   Muziganizira zinthu zabwino

     Zimene Baibulo limanena: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.”—Miyambo 17:22.

     Mfundo yake: Kukhala ndi maganizo abwino komanso kuyembekezera zinthu zabwino kungakuthandizeni kuti musamadandaule kwambiri chifukwa cha matenda anu.

     Tayesani izi: Muziganizira zimene mungakwanitse kuchita m’malo moganizira zimene simungachite. Musamadziyerekezere ndi anthu ena kapena ndi mmene inuyo munalili musanayambe kudwala. (Agalatiya 6:4) Muzikhala ndi zolinga zimene mungakwanitse. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muziyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. (Miyambo 24:10) Ngati zingatheke, muzithandiza anthu ena. Chimwemwe chimene chimabwera chifukwa chothandiza ena chingakuthandizeni kuti musamaganizire kwambiri mavuto anu.—Machitidwe 20:35.

Kodi Mulungu angakuthandizeni kuthana ndi matenda anu?

 Baibulo limasonyeza kuti Yehova Mulungu a angathandize munthu amene akudwala. Ngakhale kuti sitingayembekezere kuti atichiritse mozizwitsa, anthu amene amalambira Mulungu angathandizidwe m’njira zotsatirazi:

 Mtendere. Yehova angakupatseni “mtendere wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.” (Afilipi 4:6, 7) Mtendere wamumtima umenewu ungathandize munthu kuti asamade nkhawa kwambiri. Mulungu amapereka mtenderewu kwa anthu amene amapemphera kwa iye n’kumamuuza nkhawa zawo.—1 Petulo 5:7.

 Nzeru. Yehova angakupatseni nzeru zokuthandizani kusankha bwino zochita. (Yakobo 1:5) Munthu amapeza nzeru zoterezi akamaphunzira mfundo zothandiza za m’Baibulo n’kumazitsatira pa moyo wake.

 Zinthu zolimbikitsa zimene tingayembekezere m’tsogolo. Yehova walonjeza kuti m’tsogolo “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Lonjezoli limathandiza anthu ambiri kukhala ndi maganizo abwino ngakhale kuti akudwala matenda aakulu.—Yeremiya 29:11, 12.

a Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.—Salimo 83:18.