Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Mateyu 11:28-30—“Bwerani Kwa Ine . . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

Mateyu 11:28-30—“Bwerani Kwa Ine . . . . Ndipo Ndidzakutsitsimutsani”

 “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”—Mateyu 11:28-30, Baibulo la Dziko Latsopano.

 Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.—Mateyo 11:28-30, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Mateyu 11:28-30

 Yesu anaitana anthu omwe ankamumvetsera kuti abwere kwa iye. Anawatsimikizira kuti ngati ataphunzira kwa iye, akhoza kutsitsimulidwa ndi kupeza mpumulo.

 “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa.” Anthu omwe Yesu ankawaitanawa, anali “olemedwa” ndi malamulo komanso miyambo ya anthu yomwe atsogoleri achipembedzo ankawapanikiza nayo. (Mateyu 23:4; Maliko 7:7) Anthu wamba ankalemedwanso chifukwa cha nkhawa komanso chifukwa chotopa ndi kugwira ntchito kwa nthawi yaitali kuti apeze zinthu zofunika zosamalira mabanja awo.

 “Ndidzakutsitsimutsani.” Yesu analonjeza anthu omwe anamvera atawaitana, kuti adzawapumitsa kapena kuwathandiza kuti apepukidwe. Iye anachita zimenezi, powathandiza kumvetsa zimene Mulungu amafuna kuti iwo azichita. (Mateyu 7:24, 25) Kudziwa zimenezi kunawathandiza kuti amasuke ku ukapolo wa ziphunzitso ndi miyambo yachipembedzo yomwe inali yopondereza. (Yohane 8:31, 32) Ngakhale kuti kuphunzira ndi kutsatira zomwe Yesu ankaphunzitsa kunkafunika khama, koma zomwe ankaphunzitsa zinkatsitsimula anthu.

 “Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine.” Kale, anthu ankagwiritsa ntchito goli, lomwe linali mtengo womwe ankawuyika pamapewa akafuna kunyamula katundu wolemera. Choncho mawu akuti “goli,” akutanthauza kutsatira kapena kugonjera malamulo operekedwa ndi munthu waudindo. (Levitiko 26:13; Yesaya 14:25; Yeremiya 28:4) Ndipo mawu akuti “phunzirani kwa ine,” angatanthauzenso kuti “mukhale ophunzira anga.” Pamenepa Yesu ankalimbikitsa anthu omwe ankamumvetsera kuti akhale ophunzira ake poyamba kumutsatira ndi kutengera chitsanzo chake.—Yohane 13:13-15; 1 Petulo 2:21.

 “Ndipo mudzatsitsimulidwa.” Yesu sanalonjeze kuti adzathetsa mavuto a anthuwo nthawi yomweyo. Komabe, anatonthoza ndi kupereka chiyembekezo kwa anthu omwe ankamumvetsera. (Mateyu 6:25-32; 10:29-31) Anthu omwe anadzakhala ophunzira ake komanso kuvomereza zomwe ankaphunzitsa, anaona kuti kutumikira Mulungu sikunali kotopetsa koma kunawathandiza kukhala osangalala.—1 Yohane 5:3.

 “Goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” Mosiyana kwambiri ndi atsogoleri achipembedzo a nthawi imeneyo, Yesu anali wodzichepetsa ndi wofatsa. (Yohane 7:47-49) Yesu sankachita zinthu mwankhanza kapenanso kupondereza anthu. Koma anali wokoma mtima ndipo anthu ankamasuka naye. Ankachita zinthu moganizira ophunzira ake. (Mateyu 7:12; Maliko 6:34; Luka 9:11) Yesu anathandiza anthu kudziwa mmene angapindulire ndi chifundo cha Mulungu. Komanso anawatsitsimula powathandiza kukhala ndi chikumbumtima chabwino. (Mateyu 5:23, 24; 6:14) Makhalidwe abwino omwe Yesu anali nawo, anathandiza kuti anthu akopeke naye ndi kuyamba kumutsatira komanso kuti avomere kusenza goli lake pokhala ophunzira ake.

Nkhani yonse ya pa Mateyu 11:28-30

 Yesu analankhula mawu omwe ali pa Mateyu 11:28-30, pa nthawi yomwe ankalalikira ku Galileya m’chaka cha 31 C.E. Mateyu, ndi mtumwi yekhayo amene analemba mawu amenewa. Chifukwa chakuti mtumwiyu anali Myuda komanso poyamba anali wokhometsa msonkho, ankaona mmene anthu wamba ankazunzikira kuti apereke msonkho kuboma la Roma. Ankaonanso mmene atsogoleri achipembedzo achiyuda omwe anali achinyengo ankaponderezera anthuwa. N’zosakayikitsa kuti analimbikitsidwa kwambiri ataona kuti Yesu akugwiritsa ntchito mphamvu zomwe Atate wake Yehova a anamupatsa, poitana anthu odzichepetsa komanso omwe ankaponderezedwa kuti abwere kwa iye.—Mateyu 11:25-27.

 Uthenga wabwino wa Mateyu umafotokoza bwino za makhalidwe omwe Yesu ankasonyeza monga Mesiya wolonjezedwa komanso monga mfumu yam’tsogolo yodzalamulira mu Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 1:20-23; Yesaya 11:1-5.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti muone mfundo zokhudza buku la Mateyu.

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werenganinso nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?