Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo ndi​—Buku la Maulosi Olondola, Gawo 6

“Masiku Otsiriza”

Baibulo ndi​—Buku la Maulosi Olondola, Gawo 6

Nkhani zokwanira 8 zimene zikhale zikutuluka mu Galamukani!, zizifotokoza maulosi osiyanasiyana a m’Baibulo. Nkhanizi zikuthandizani kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi maulosi a m’Baibulo analembedwa ndi anthu kapena pali umboni wakuti analembedwa ndi Mulungu? Kuwerenga nkhanizi kukuthandizani kudziwa zoona zenizeni.

TIKUKHALA m’nthawi yovuta kwambiri ndipo nthawi zambiri timamva nkhani za mavuto komanso ziwawa zimene zikuchitika padziko lonse. Kodi zimene zikuchitikazi zikutiuza chiyani za nthawi imene tikukhalayi?

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Baibulo linalosera kuti mavuto adzawonjezereka kwambiri padziko lonse m’nthawi ya “mapeto” ino. (Mateyu 24:3) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti dziko latsala pang’ono kutha m’njira imene anthu ena amaganizira. M’malomwake Baibulo linanena za zinthu, kapena zizindikiro, zimene zizidzachitika komanso makhalidwe amene anthu azidzasonyeza “m’masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Yesu anauza otsatira ake kuti akadzaona “zimenezi zikuchitika,” adzadziwe kuti atsala pang’ono kupulumutsidwa. (Luka 21:31) Tiyeni tione ena mwa maulosi amene akupangitsa kuti nthawi imene tikukhala ino ikhale yapadera.

Ulosi woyamba:

“Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina.”​—Mateyu 24:7.

Kukwaniritsidwa kwake: Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, anthu ambiri ankayembekezera kuti kuyambira nthawi imeneyo mpaka m’tsogolo, padzikoli pakhala mtendere. Koma anadabwa kwambiri nkhondo yoyamba ya padziko lonse itayamba ndipo zimenezi zinachititsa kuti pachitike nkhondo zosiyanasiyana. Baibulo linaneneratu m’buku la Chivumbulutso kuti mtendere udzachotsedwa “padziko lapansi, kuti anthu aphane.”​—Chivumbulutso 6:4.

Zimene umboni ukusonyeza:

  • “Nkhondo yoyamba yapadziko lonse itayambika mu 1914, zinthu zinasintha kwambiri padziko lonse.”​—Linatero buku lakuti, The Origins of the First World War, lomwe linafalitsidwa mu 1992.

  • Ngakhale kuti sitikudziwa chiwerengero chenicheni cha anthu amene anafa pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse, buku lina limanena kuti asilikali pafupifupi 8,500,000 anafa pa nkhondoyi.

  • Koma pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse ndi pamene anthu ambiri anafa. Anthu amakhulupirira kuti asilikali komanso anthu wamba pakati pa 35 miliyoni ndi 60 miliyoni anafa.

  • Kuyambira pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inatha kufika mu 2010, pachitika nkhondo zokwana 246, m’madera okwana 151 padziko lonse.

Ulosi wachiwiri:

“Kudzakhala njala.”​—Mateyu 24:7.

Kukwaniritsidwa kwake: M’zaka za m’ma 1900, anthu oposa 70 miliyoni anafa chifukwa cha njala ndipo vutoli lidakalipobe padziko lonse.

Zimene umboni ukusonyeza:

  • Bungwe la United Nations linanena kuti njala ndi imodzi mwa zinthu zazikulu zomwe zimayambitsa matenda padziko lonse ndipo munthu m’modzi pa anthu 7 alionse alibe chakudya chokwanira.

  • “Masiku ano njala ili padziko lonse chifukwa cha zinthu zambiri monga chilala, kuchuluka kwa anthu, kukokoloka kwa nthaka, kusowa kwa madzi komanso chifukwa choti padzikoli pakumatentha kwambiri.”​—Scientific American.

Ulosi wachitatu:

“Kudzachitika zivomezi zamphamvu.”​—Luka 21:11.

Kukwaniritsidwa kwake: Chifukwa chakuti anthu ambiri amakhala m’malo amene zivomezi zikhoza kuchitika, chiwerengero cha anthu amene aphedwa kapena kuvulala ndi zivomezi chawonjezereka.

Zimene umboni ukusonyeza:

  • Lipoti lina limene linatuluka mu 2010 linanena kuti: “Pa ngozi zachilengedwe zimene zachitika m’zaka zaposachedwapa, zivomezi ndi zimene zapha anthu ambiri.”​—World Disasters Report 2010.

  • Kuyambira mu 1970 mpaka mu 2001, pa avereji, chaka chilichonse pankachitika zivomezi * 19 zomwe zinapha anthu pafupifupi 19,547. Koma kuyambira mu 2002, pa avereji, chaka chilichonse pankachitika zivomezi 28 zomwe zinapha anthu 67,954.

Ulosi wachinayi:

“Kudzakhala miliri . . . m’malo osiyanasiyana.”​—Luka 21:11.

Kukwaniritsidwa kwake: Anthu mamiliyoni ambiri akufa chaka chilichonse chifukwa cha matenda opatsirana ngakhale kuti zachipatala zapita patsogolo kwambiri. Matenda sakuchedwa kufalikira chifukwa choti anthu akumapita m’madera ena mosavuta komanso chifukwa chakuti anthu ambiri akuchulukana m’matauni.

Zimene umboni ukusonyeza:

  • M’zaka za m’ma 1900, anthu pakati pa 300 miliyoni ndi 500 miliyoni anafa ndi matenda a nthomba.

  • Bungwe lina linanena kuti m’zaka 30 zapitazi, “matenda oposa 30 omwe poyamba sankadziwika, monga Ebola, Edzi, matenda ofalitsidwa ndi makoswe, ndi SARS akupha anthu ambiri masiku ano.”​—Worldwatch Institute.

  • Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse lachenjeza kuti tizilombo tosamva mankhwala tiyamba kuchuluka. Bungweli linati: “Kutsogoloku matenda omwe panopo ali ndi mankhwala, sazidzamva mankhwala ena alionse ndipo azidzapha anthu ambiri.”

Ulosi wachisanu:

Anthu “adzaperekana ndi kudana. . . . Chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.”​—Mateyu 24:10, 12.

Kukwaniritsidwa kwake: Anthu ambiri aphedwa chifukwa cha chidani. M’mayiko ena mumachitika nkhondo komanso anthu amaphwanya malamulo kwambiri, zomwe zachititsa kuti anthu azikhala mwamantha ndiponso kuti azichita zachiwawa.

Zimene umboni ukusonyeza:

  • Mu ulamuliro wa chipani cha Nazi, Ayuda pafupifupi 6 miliyoni komanso anthu a mitundu ina anaphedwa. Ponena za mmene anthu anaonera zimenezi, munthu wina wolemba mabuku, dzina lake Zygmunt Bauman, ananena kuti: “Anthu amenewa ataphedwa, anthu ankasonyeza kuti sizinkawakhudza ndipo ankaona kuti ndi mmene moyo ulili.”

  • Wailesi ya BBC inanena kuti: “Anthu pafupifupi 800,000 a mtundu wa Tutsi ndi a Hutu ena anaphedwa m’miyezi yochepa yokha.” Munthu wina wofufuza amanena kuti anthu pafupifupi 200,000 anapha nawo anthu amenewa.

  • Chaka chilichonse, anthu oposa 740,000 amafa chifukwa cha nkhondo ndi zachiwawa.

Ulosi wa 6:

“Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osakonda achibale awo.”​—2 Timoteyo 3:2, 3.

Kukwaniritsidwa kwake: Masiku ano anthu ndi odzikonda kwambiri ndiponso osadziletsa. Makhalidwe amenewa amabweretsa mavuto ambiri.

Zimene umboni ukusonyeza:

  • Lipoti lina linanena kuti makolo komanso ana a ku United Kingdom “amangokhalira kugula zinthu.” Iwo amakhala akugulira anthu ena zinthuzo n’cholinga choti “azikondedwa komanso kuti athetse mikangano m’banja mwawo.”​—UNICEF.

  • Ana pafupifupi 275 miliyoni padziko lonse amachitiridwa nkhanza kunyumba kwawo.

  • “Chaka chilichonse ku United States kokha, anthu oposa 500,000 amachitiridwa nkhanza kapena kunyalanyazidwa.”​—Centers for Disease Control and Prevention.

Ulosi wa 7:

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”​Mateyu 24:14.

Kukwaniritsidwa kwake: Baibulo limaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni lomwe mfumu yake ndi Yesu ndipo akulamulira ali kumwamba. Ufumu umenewu “udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [maboma a anthu] “ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”​—Danieli 2:44.

A Mboni za Yehova padziko lonse amathandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi chiyani komanso zimene udzachite.

Zimene umboni ukusonyeza:

  • A Mboni za Yehova oposa 7 miliyoni padziko lonse, akulalikira za Ufumu wa Mulungu m’mayiko oposa 230.

  • Pogwiritsa ntchito mabuku komanso Intaneti, a Mboni za Yehova afalitsa nkhani zofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 500.

Mmene Maulosi Amakhudzira Tsogolo Lanu

Poona zimene zikuchitika, anthu ambiri akukhulupirira kuti maulosi onse a m’Baibulo onena za masiku otsiriza akukwaniritsidwa panopa. Nkhani 6 zoyambirira za nkhani zino zinasonyeza kuti Baibulo ndi buku lolondola pa nkhani ya maulosi.

Zimenezi zingakuthandizeninso kuti muzikhulupirira zimene Baibulo linaneneratu za m’tsogolo. Mulungu walonjeza kuti adzathetsa mavuto onse m’masiku otsiriza. Maulosi amenewa ayenera kukulimbikitsani kwambiri. Nkhani ziwiri zotsatira zidzafotokoza mmene Mulungu athetsere mavuto “m’masiku otsiriza” ano, komanso madalitso amene anthu adzalandire padziko lapansi.

^ ndime 22 Bungwe lina lofufuza za ngozi zachilengedwe linanena kuti ngati kwachitika chivomezi chomwe chapha anthu oposa 10, chakhudza anthu oposa 100, ngati boma lapempha kuti mayiko ena alithandize kapena ngati layamba kugwiritsa ntchito malamulo amphamvu pofuna kuthandiza anthu, ndiye kuti chimenecho ndi chivomezi champhamvu kwambiri.​Centre for Research on the Epidemiology of Disasters.