Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Pafupifupi hafu ya anthu omwe amapezeka ndi khansa ku [United Kingdom] chaka chilichonse, omwe ndi anthu oposa 130,000, amayamba kudwala matendawa chifukwa cha zinthu zimene akanatha kuzipewa, monga kusuta, kumwa mwauchidakwa komanso kudya zakudya zosayenera.”​—BBC NEWS, BRITAIN.

“Anthu amene amachita malonda ogulitsa ziwalo za nyama zakutchire mozembera boma ndi omwe akuchititsa kuti mitundu ina ya nyama itheretu . . . kusiyana ndi mmene zinalili kale.”​—WILDLIFE CONSERVATION SOCIETY, U.S.A.

Anthu omwe amaonera TV kwa maola 6 pa tsiku amachepetsa moyo wawo ndi zaka pafupifupi 5, poyerekeza ndi anthu omwe saonera TV. Pamenepa tinganene kuti pa ola lililonse limene munthu wakhala akuonera TV amakhala kuti wachepetsa moyo wake ndi mphindi 22.​—BRITISH JOURNAL OF SPORTS MEDICINE, BRITAIN.

Ku Germany, amayi oyembekezera 90 pa 100 alionse akadziwa kuti adzabereka mwana wodwala matenda ozerezeka, amangochotsa mimbayo.​—DER TAGESSPIEGEL, GERMANY.

Anthu Am’tauni Amakhala ndi Nkhawa Kwambiri

Magazini ina ya ku Poland inanena kuti kafukufuku wasonyeza kuti “anthu am’tauni amakonda kuchita zachiwawa akakhala ndi nkhawa kuposa anthu akumudzi.” (Przekrój) Dokotala wina wa pa yunivesite ina m’dziko lomwelo, dzina lake Mieczysław Jaskulski ananena kuti: “Anthu amene amakhala m’tauni amakumana ndi zinthu zambiri zimene zimachititsa kuti azikhala ndi nkhawa. Komanso amavutika maganizo kwambiri kuposa akumudzi.” Kodi anthu am’tauni angathane bwanji ndi mavuto amenewa? Magazini yomwe taitchula ija inanena kuti: “Musamade nkhawa ndi zinthu zimene simungathe kuzipewa. Nkhawa za ku ntchito muzizisiya ku ntchito. Mukakhala ndi nkhawa muzipita kokapondaponda komanso muzitenga holide.”

Facebook Imasunga Zinthu kwa Nthawi Yaitali

Mnyamata wina wa ku Austria, yemwe akuphunzira zamalamulo anafufuza kuti adziwe ngati zinthu zimene iye ankalemba kwa zaka zitatu pa Facebook zinali zidakalipobe. Kampani ya Facebook inamutumizira CD yokhala ndi zinthu zonse zimene iye ankalemba pa Facebook. Nyuzipepala ina ya ku Germany inalemba zimene mnyamatayu ananena. Iye anati: “Mu CD imeneyi munali chilichonse chimene ndinkalemba, mameseji ngakhalenso zinthu zachinsinsi zomwe ndinkalemberana ndi anzanga.” Mu CD imeneyi munalinso zinthu zonse zimene mnyamatayu anazifufuta.