Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzichita Zinthu Mwadongosolo

Muzichita Zinthu Mwadongosolo

Munthu akamayesetsa kuchita zinthu mwadongosolo, zinthu zimamuyendera bwino. Mwachitsanzo, amakhala ndi nthawi yambiri, sakhala ndi nkhawa komanso amakhoza bwino ku sukulu.

AYEREKEZANI kuti mukufuna kugula chinachake musitolo, koma mutangolowa mwapeza kuti katundu sanalongedzedwe mwadongosolo. N’zachidziwikire kuti zingakutengereni nthawi yaitali kuti mupeze chimene mukufunacho. Koma simungavutike ngati katunduyo walongedzedwa mwadongosolo komanso ngati aika zikwangwani. N’chimodzimodzinso ndi sukulu. Kuti zinthu zizikuyenderani bwino, chinthu chimodzi chofunika ndi kuchita zinthu mwadongosolo. Ndiye kodi mungachite bwanji zimenezi?

Muzikhala ndi ndandanda.

Mnyamata wina wazaka 18 wa ku United States, dzina lake Zachary, ananena kuti: “Nthawi ina ndinakagona kwa mnzanga Loweruka ndi Lamlungu moti ndinaiwala zoti ndili ndi homuweki komanso kuti ndinkafunika kugwira ntchito zina zapakhomo. Nditapita kusukulu ndinachita kupempha aphunzitsi kuti andilole kubweretsa homuweki yanga mochedwa. Panopa ndimachita zinthu mwadongosolo chifukwa ndili ndi ndandanda ya zimene ndiyenera kuchita.”

Kukhala ndi ndandanda kwathandizanso mtsikana wina wa ku Papua New Guinea, dzina lake Celestine. Pofotokoza zimene ankachita ali pa sukulu, iye anati: “Ndinkakhala ndi ndandanda ya zonse zimene ndikufunika kuchita monga kulemba homuweki komanso mayeso. Ndandandayi inandithandiza kuti ndikafuna kuchita zinthu, ndiziyamba ndi zofunika kwambiri komanso kuti ndizizichita pa nthawi yake.”

Mfundo yothandiza: Lembani ndandanda yanu m’kope kapena mufoni yanu.

Musamazengereze pochita zinthu.

Anthu ali ndi chizolowezi chonena kuti: “Aa, ndipangabe.” Koma ndibwino kumachita zinthu nthawi yomweyo, makamaka ikakhala homuweki.

Mfundo yothandiza: Muzilemberatu homuweki yanu mukangofika kunyumba. Musamaonere TV kapena kuchita zinthu zina musanalembe homuweki.

Muzilongedzeratu za ku sukulu.

Kodi zinayamba zakuchitikiranipo kuti mwafika m’kalasi n’kuona kuti mwaiwala kope, cholembera kapena mabuku? Kodi mungatani kuti zimenezi zisamakuchitikireni? Mnyamata wina wa ku Myanmar, dzina lake Aung Myo Myat, ananena zimene amachita kuti asamaiwale zinthu. Iye anati: “Nthawi zonse ndimalongedzeratu chikwama cha ku sukulu.”

Mfundo yothandiza: Muzionetsetsa kuti mwalongedza chikwama chanu mwadongosolo kuti musamavutike kupeza zinthu.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Mukamachita zinthu mwadongosolo mumapewa mavuto amene amabwera chifukwa choiwala zinthu, kuchedwa komanso kusowa nthawi yochitira zinthu zina zofunika.

Yambani kutsatira malangizo amenewa. Ganizirani chinthu chimodzi chimene mukuona kuti mufunika kumachichita mwadongosolo. Kenako mothandizana ndi kholo lanu kapena mnzanu, fufuzani njira zina zimene zingakuthandizeni kuti muyambe kuchita zinthu mwadongosolo.