Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Makolo Angathandizire

Mmene Makolo Angathandizire

“Kalasi imodzi inkakhala ndi ana ambirimbiri. Munalibe mafani ndipo munkatentha kwambiri.”​—Anatero Luis, wa ku Bolivia.

“Pasukulu pathu panali aphunzitsi ochepa moti ana sankathandizidwa mokwanira. Tinalibe zipangizo zophunzirira ngati mapu, laibulale komanso zipangizo za kulabu.”​—Anatero Dorcus, wa ku Myanmar.

“Nthawi zina ana a sukulu ankachita zopulupudza moti aphunzitsi ankalephera kuwaletsa. Zimenezi zinkachititsanso kuti tizilephera kuphunzira.”​—Anatero Nina, wa ku South Africa.

ZIMENE zafotokozedwa pamwambapa zikusonyeza kuti m’masukulu ena zimakhala zovuta kuti ana aphunzire bwino. Monga makolo, kodi mungatani kuti muthandize ana anu kuti aphunzire bwino ngakhale kuti amakumana ndi mavuto ngati amenewa? Taonani zina zimene mungachite.

Muzisonyeza chidwi.

M’malo moganizira kwambiri za mavuto amene mwana wanu akukumana nawo, omwenso mwina simungathe kuwathetsa, muziganizira zimene mungathe kuchita. Ngati mwana wanu akulephera phunziro linalake kapena akumakhala ndi homuweki yambiri, kambiranani naye njira zimene mungatsatire kuti athane ndi vutolo. Mwachitsanzo, ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti mwanayo azitha kuwerenga pakhomo? Kodi mwana wanu akufunika kumuthandiza kupanga ndandanda yoti azichita zinthu zofunikira choyamba? Kodi angafunike kumupezera munthu wina woti azimuphunzitsa? Mungafunse aphunzitsi a mwana wanu kuti mudziwe zina zomwe mungachite kuti mumuthandize. Muziona aphunzitsi a mwana wanu ngati anthu amene angakuthandizeni osati adani anu.

Muzimuthandiza kuti asaiwale cholinga cha sukulu.

Sukulu ingathandize mwana wanu kuti adzakhale wodalirika akadzakula. Choncho, mwana wanu akamapita ku sukulu cholinga chake chisakhale choti adzakhale wolemera. Kafukufuku akusonyeza kuti, achinyamata ambiri amapita ku sukulu n’cholinga choti adzakhale olemera. Koma Baibulo limachenjeza kuti sitiyenera kukonda chuma. Ngakhale kuti limanena kuti “ndalama zimatetezera,” limachenjezanso kuti “anthu ofunitsitsa kulemera” sakhala osangalala.​—Mlaliki 7:12; 1 Timoteyo 6:9.

Musamawaikire kumbuyo akalakwa.

Aziphunzitsi ambiri amanena kuti makolo ena ndi ovuta kuposa ana awo. Makolo ena sachedwa kulowerera kapena kulalatira aphunzitsi mwana wawo akalakwa kapena akalephera mayeso. Mwachitsanzo, magazini ina inanena zimene mphunzitsi wina wa pa yunivesite ananena. Iye anafotokoza kuti waphunzitsapo ana ena omwe “amaimbira makolo awo foni ali m’kalasi n’kuwauza kuti aphunzitsi awalepheretsa mayeso. Akatero makolowo amauza mwanayo kuti akufuna kulankhula ndi aphunzitsiwo m’kalasi momwemo. Ndipo makolo ena amalalatira aphunzitsi powauza kuti akulipira ndalama zambiri kuti ana awo aphunzire, choncho amafuna kuti mwana wawo azikhoza bwino kwambiri kuti ndalama zawo zisalowe m’madzi.”​—Time.

Makolo amene amachitira ana awo zimenezi sakuwafunira zabwino. Mayi wina wolemba mabuku, dzina lake Polly Young-Eisendrath, analemba buku lomwe anafotokozamo kuti, makolo amene amaikira ana awo kumbuyo amachititsa kuti anawo azilephera kusankha zochita pawokha, azilephera kudziwa zochita akalakwitsa komanso azilephera kuzindikira kuti nthawi zina angalakwitse. Iye ananenanso kuti: “Ngati nthawi zonse makolo amaikira ana awo kumbuyo, makolowo ndi amene amadziwa njira zothetsera mavuto koma anawo amavutika akakula chifukwa satha kuthetsa okha mavuto.”​—The Self-Esteem Trap.

Muziona bwino nkhani ya maphunziro.

Monga tanenera kale, sukulu ingadzathandize mwana wanu akadzakula. (Genesis 2:24) Koma kodi ayenera kuphunzira kufika pati?

Musamaganize kuti mwana wanu afunika kupita ku yunivesite kuti adzapeze ntchito yabwino. Pali zinthu zina zimene mungachite komanso zosawonongetsa ndalama zambiri. Ndipotu nthawi zina anthu amene amaphunzira ntchito zamanja amapeza ndalama zambiri ngati kuti anapita ku yunivesite.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Masiku ano, m’masukulu muli mavuto ambiri ndipo ana amakumana ndi mavuto amene m’mbuyomu kunalibe. Koma ngati mutamuthandiza, zinthu zikhoza kumuyendera bwino kusukulu. Mungachite bwino kukambirana ndi banja lanu nkhani zimene zili patsamba 3 mpaka 7 ya magazini ino.