Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Muone

Muone

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndikatseka maso anga

    Ndimaona dziko labwino,

    Nanunso

    Onani,

    Muone.

  2. 2. Si maloto, m’khulupirire.

    Zimene M’lungu walonjeza

    N’zenizeni,

    Zidzachitikadi.

    (KOLASI)

    Onani—

    Anthutu akusangalala.

    Onani—

    Mmene M’lungu ankafuniradi.

  3. 3. Anthutu omwe anamwalira,

    Adzuka ndipo tikuwaona.

    Nanunso

    Onani,

    Muone.

  4. 4. Mavuto komanso kulira

    Zathatu zonse, pano ndi mbiri.

    Nanunso

    Onani,

    Muone.

    (KOLASI)

    Onani—

    Anthutu akusangalala.

    Onani—

    Mmene M’lungu ankafuniradi.

  5. 5. N’chikhulupiriro ndaona

    Zomwe Yehova walonjeza.

    (VESI LOKOMETSERA)

    Tiziganizira

    Madalitso

    Opandatu malire

    Ndiye—

  6. 6. Titseke maso athu

    N’kumaona dziko labwino.

    Nanunso

    Onani

    Muone.