Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Timasankha

Zimene Timasankha

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndathedwa nzeru.

    Ndasowa kolowera.

    Mtimawu

    Ngopusitsa;

    Ndili kale m’chikondi.

  2. 2. N’kovutadi

    Kumvera M’lungu.

    .Ndisamvere mtimawu.

    Ndidzamvera mawu ake.

  3. 3. Ndilitu pa nkhondo

    Yolimbana ndi mtima wanga.

    Koma mphamvu ndimazipeza,

    Kwa Yehova, pondiuza.

    (KOLASI)

    Kuti: “Ndimakukonda. Sindingakusiye.

    Undikhulupirire.

    Kuti ndikuthandize.”

  4. 4. Kuti zizitiyendera

    Tizisankhatu zinthu mwanzeru.

    Tiyambe ndikulimbana,

    Ndi mtima wopusitsawu.

    Ndipo tiuteteze.

  5. 5. Ndikayang’ana m’mbuyo

    Kusankhatu mwanzeru,

    Kunali kovutadi,

    M’lungu anandithandiza.